Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
Kodi n’zotheka kukhala ndi boma limodzi padziko lonse?
Ganizilani mmene boma la padziko lonse lingathandizile anthu. Masiku ano anthu ambili akuvutika cifukwa ndi osauka kwambili pamene ena ndi olemela kwambili. Komabe, boma la padziko lonse limene limaganizila anthu likhoza kuonetsetsa kuti anthu onse ali ndi zimene amafunikila. Kodi muona kuti n’zotheka anthu kupanga boma lotelo?—Ŵelengani Yeremiya 10:23.
Kuyambila kale, maboma alephela kusamalila anthu, makamaka osauka. Maboma ena ndi ankhanza. (Mlaliki 4:1; 8:9) Koma Mulungu Wamphamvuyonse walonjeza kuti adzabweletsa boma limene lidzaphwanya maboma onse ndi kuyamba kulamulila. Wolamulila wake adzasamalila bwino anthu.—Ŵelengani Yesaya 11:4; Danieli 2:44.
Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani?
Yehova Mulungu wasankha Wolamulila wa dziko lonse wabwino kwambili. Wolamulila ameneyu ndi Yesu Mwana wake. (Luka 1:31-33) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anali wofunitsitsa kuthandiza anthu. Monga Mfumu, iye adzagwilizanitsa anthu a mitundu yonse ndi kuthetsa mavuto onse a anthu.—Ŵelengani Salimo 72:8, 12-14.
Kodi ndi anthu onse amene amavomeleza Yesu kukhala Wolamulila wao? Iyai. Ngakhale ndi conco, Yehova ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Iye akupatsa anthu mwai wovomeleza Yesu kukhala Wolamulila wao. Posacedwapa Yesu adzaononga anthu onse oipa padzikoli ndi kubweletsa mtendele ndi citetezo—Ŵelengani Mika 4:3, 4.