Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUKAMBILANA NDI MUNTHU WINA NKHANI ZA M’BAIBULO

N’cifukwa Ciani Tifunika Kuphunzila Baibulo?

N’cifukwa Ciani Tifunika Kuphunzila Baibulo?

Nkhani yotsatilayi ikuonetsa mmene a Mboni za Yehova amacitila pokambilana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyelekeze kuti a Inoki ndi a Mboni, ndipo akumana ndi a Yohane.

BAIBULO LIMAKAMBA ZOONA PA NKHANI ZAKALE

A Yohane: Koma ndisakubisileni, ine sindikonda zopemphela. Conco, ndisakutaileni nthawi.

A Inoki: Ndayamikila cifukwa condiuza zimenezi. Koma dzina langa ndine Inoki. Nanga inu ndinu ndani?

A Yohane: Ndine Yohane.

A Inoki: Ndakondwela kukumana nanu a Yohane.

A Yohane: Zikomo.

A Inoki: Coyamba ndifunseko, kodi munakulila m’banja lacikristu?

A Yohane: Inde. Koma nditapita kukoleji, ndinasiya kupemphela.

A Inoki: Ohoo. Kodi munacita maphunzilo otani kukoleji?

A Yohane: Ndinacita maphunzilo okhudza cikhalidwe ca anthu ndi mbili yakale. Ndimakonda kuphunzila za mbili yakale kuti ndidziŵe mmene anthu apitila patsogolo.

A Inoki: N’zoona. Kuphunzila za mbili yakale n’kosangalatsa. Mwina mukudziŵa kuti Baibulo ndi buku la mbili yakale. Kodi munagwilitsilapo nchito Baibulo pofufuza zinthu zina?

A Yohane: Iyai. Ndimadziŵa kuti Baibulo ndi buku labwino, koma sindinali kudziŵa kuti ndi buku la mbili yakale.

A Inoki: Ndikuona kuti ndinu munthu womasuka. Ngati muli ndi nthawi, kodi mungandilole kuti ndikuonetseni zitsanzo zingapo zosonyeza kuti mbili ya m’Baibulo ndi yoona?

A Yohane: Pali bwino. Koma ndilibe Baibulo.

A Inoki: Palibe vuto. Tiyeni tigwilitsile nchito Baibulo langa. Citsanzo coyamba cili apa pa 1 Mbiri caputala 29 vesi 26 ndi 27. Mavesi amenewa amati: “Kunena za Davide mwana wa Jese, iye analamulila Isiraeli yense. Masiku onse amene iye analamulila Isiraeli anakwana zaka 40. Ku Heburoni analamulila zaka 7, ndipo ku Yerusalemu analamulila zaka 33.”

A Yohane: Nanga lembali lionetsa bwanji kuti mbili ya m’Baibulo ndi yoona?

A Inoki: Panthawi ina, anthu anali kutsutsa kuti munthu wochedwa Mfumu Davide analiko.

A Yohane: Zoona? N’cifukwa ciani anali kutsutsa zakuti iye analikodi?

A Inoki: Cinali cifukwa cakuti kupatulapo Baibulo panalibe maumboni ena otsimikizila kuti iye anali munthu weniweni. Koma mu 1993, gulu la ofufuza zinthu zakale linafukula mwala wakale kwambili, ndipo pamwalapo panali liu limene limatanthauza kuti “Nyumba ya Davide.”

A Yohane: Zimenezi n’zosangalatsa kwambili.

A Inoki: Munthu wina wochulidwa m’Baibulo amene anthu anali kutsutsa zakuti analiko ndi Pontiyo Pilato, bwanamkubwa amene anakhalako m’nthawi ya Yesu. Pa nduna za boma za m’nthawi yake, iyenso amachulidwa pa lemba la Luka caputala 3 vesi 1.

A Yohane: Zoonadi. Vesili lanena kuti: “Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode anali wolamulila cigawo ca Galileya.”

A Inoki: Zikomo kwambili. Kwa zaka zambili akatswili ena a Baibulo anali kukaikila kuti Pontiyo Pilato anali munthu weniweni. Koma zaka pafupifupi 50 zapitazo, ku Middle East anthu anapeza mwala umene panali dzina limeneli.

A Yohane: Ohoo! Ine sindinamveko zimenezi.

A Inoki: Inde, ndi mmene zilili.

A Yohane: Kunena zoona, ndimaona kuti Baibulo ndi buku labwino, koma ndimaona kuti ndi lacikale. Ngakhale kuti limakamba zoona pa nkhani zakale, ndimaona kuti lilibe phindu kwenikweni masiku ano.

BAIBULO NDI LAKALE KOMA N’LOTHANDIZA MASIKU ANO

A Inoki: Anthu ambili amaganiza conco. Koma ine ndimakhulupilila kuti Baibulo ndi lothandiza masiku ano. Cifukwa cake n’cakuti zinthu zimene anthu amafunikila pa umoyo sizinasinthe kucokela pamene anthu analengedwa. Mwacitsanzo, kuyambila kalekale anthufe timafunikila cakudya, zovala, ndi pogona. Timafunanso kuceza ndi anzathu ndiponso kukhala ndi banja lacimwemwe. Kodi si zoona kuti tonsefe timaona kuti zinthu zimenezi n’zofunika?

A Yohane: N’zoona.

A Inoki: Baibulo lili ndi malangizo othandiza pa mbali zonsezi. Ilo ndi buku lakale koma lili ndi mfundo zamakono.

A Yohane: Mutanthauza ciani?

A Inoki: M’mau ena ndinganene kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza masiku ano monga mmene zinalili zaka zambilimbili zapitazo pamene linalembedwa.

Mfundo za m’Baibulo n’zothandiza masiku ano monga mmene zinalili zaka zambilimbili zapitazo pamene linalembedwa

A Yohane: Zoona? N’lothandiza pa mbali ziti?

A Inoki: Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kudziŵa mmene tiyenela kuonela ndalama, kapena mmene tingakhalile ndi banja lacimwemwe, ndiponso mmene tiyenela kukhalila ndi anzathu. Baibulo lili ngati nyale yotiunikila njila imene tiyenela kuyendamo kuti zinthu zitiyendele bwino. Mwacitsanzo, kodi muona kuti n’copepuka munthu masiku ano kukhala mwamuna kapena mutu wa banja wabwino?

A Yohane: Iyai, si copepuka. Ine ndi mkazi wanga takhala m’banja pafupifupi caka cimodzi, koma si nthawi zonse pamene timagwilizana maganizo.

A Inoki: Ndaonapo zimenezi. Koma m’Baibulo muli mfundo zosavuta kumva zimene zimathandiza. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zili pa Aefeso caputala 5. Tiyeni tiŵelenge mavesi 22, 23, ndi 28. Ngati mungakonde, ŵelengani mavesi amenewa.

A Yohane: Cabwino. Pakamba kuti: “Akazi agonjele amuna ao ngati mmene amagonjelela Ambuye, cifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala mpulumutsi wa thupilo.” Ndipo pa vesi 28 pakuti: “Mwa njila imeneyi amuna akonde akazi ao monga matupi ao. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha.”

A Inoki: Zikomo kwambili. Mwaŵelenga bwino. Kodi muganiza kuti ngati mwamuna ndi mkazi agwilitsila nchito malangizo amenewa angakhale ndi banja lacimwemwe?

A Yohane: Inde, ndiganiza conco. Koma kucita zimenezi n’kovuta.

A Inoki: N’zoona. Palibe munthu wangwilo. Ndipo m’caputala cimeneci muli vesi lina limene limatilimbikitsa kukhala anzelu. * Anthu onse amene ali pabanja afunika kukhala ololela. Ine ndi mkazi wanga tinaona kuti Baibulo limatithandiza kukhala ololela.

A Yohane: Ohoo!

A Inoki: Mboni za Yehova zili ndi Webusaiti imene ili ndi nkhani zothandiza anthu kukhala ndi mabanja acimwemwe. Ngati muli ndi nthawi, ndingakuonetseni imodzi mwa nkhani zimenezi.

A Yohane: Palibe vuto. Mungandionetse.

A Inoki: Cabwino. Adilesi ya Webusaiti yathu ndi www.pr418.com. Ili ndilo tsamba loyambilila.

A Yohane: Eee! Koma pali zithunzi zokongola.

A Inoki: Zithunzi zimenezi zikuonetsa Mboni za Yehova zimene zikugwila nchito yolalikila padziko lonse. Eyaa, ndi apa pamene tifuna. Pamenepa pali cigawo cakuti “Mabuku.” Pa cigawo cimeneci pali zofalitsa zambili zothandiza. Mwacitsanzo pali buku ili lakuti “Khalanibe M’cikondi ca Mulungu.” M’bukuli muli nkhani ziŵili zokamba za cikwati. Ndi nkhani iti imene yakusangalatsani?

A Yohane: Iyi, yakuti “Cikwati Ndi Mphatso Yocokela kwa Mulungu Wacikondi.” Ndifuna kudziŵa mmene ndingaonele ukwati wanga monga mphatso.

A Inoki: Nkhani imeneyi ikufotokoza zimene mungacite kuti mukhale acimwemwe m’banja lanu. Onani ndime 17. Kodi mungakonde kuiŵelenga?

A Yohane: Inde. Panena kuti: “Ndiponso aliyense amene afuna kukwatila ayenela kukhala wokonzeka kusamalila zofuna za mnzakeyo. (Afilipi 2:4) Paulo analemba kuti: ‘Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.’” (Aefeso 5:33) Eee! Koma anafotokoza bwino.

A Inoki: Zikomo kwambili cifukwa coŵelenga bwino. Kodi mwaona kuti pamenepa akugogomeza mfundo yakuti aliyense ayenela kucita zimene mnzake amafuna?

A Yohane: Mukutanthauza ciani?

A Inoki: Cabwino, kodi simukuvomeleza kuti mwamuna amafuna kulemekezedwa ndi mkazi wake ndiponso mkazi amafuna kuti mwamuna wake azionetsa kuti amamukonda kwambili?

A Yohane: N’zoona.

A Inoki: Ngati mwamuna nthawi zonse amayesetsa kucita zinthu zoonetsa kuti amakonda mkazi wake, kodi zingakhale zovuta mkazi kumulemekeza?

A Yohane: Ndikuona kuti sizingakhale zovuta.

A Inoki: Conco, vesi limodzi lokha limeneli la m’Baibulo, ngakhale kuti linalembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, likufotokoza zimene mwamuna ndi mkazi afunika kucita. Mwamuna ndi mkazi m’banja akamatsatila malangizo amenewa amakondana ndi kulemekezana kwambili.

A Yohane: Tsopano ndaona kuti m’Baibulo muli zambili kuposa zimene ndinali kudziŵa.

A Inoki: Ndakondwela kumva zimenezi a Yohane. Ndingakonde kudzakumananso nanu pano kuti ndidzamve maganizo anu pa kamutu kakuti “Kodi Mungacite Ciani Kuti Cikwati Canu Cipitilize?” Kamutu kameneka kali m’nkhani imodzimodziyi pa Webusaiti imeneyi. *

A Yohane: Tidzaonana, ndipo ine ndi mkazi wanga tidzaŵelenga nkhaniyi pamodzi.

Kodi m’Baibulo muli nkhani ina imene simumvetsetsa? Kodi mumacita cidwi ndi zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila kapena zimene amacita? Ngati ndi conco, musazengeleze kufunsa mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye adzakondwela kwambili kukambilana nanu nkhani zimenezi.

^ par. 43 Onani Aefeso 5:17.

^ par. 61 Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 14 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.