Kukumbukila Imfa ya Yesu —Liti ndipo Kuti?
Pa usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu analamula ophunzila ake kukumbukila nsembe imene anali pafupi kupeleka. Iye anati: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—Luka 22:19.
Caka cino, Cikumbutso ca imfa ya Yesu cidzakhalako pa Cisanu, April 3 dzuŵa litaloŵa. Mboni za Yehova zikukuitanani pamodzi ndi banja lanu kuti mudzamvetsele nkhani imene idzafotokoza cifukwa cake imfa ya Yesu ndi yofunika kwambili ndiponso mmene mungapindulile ndi imfa yake.