Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu—Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?

Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu—Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?

“Khulupilila mwa Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka.”—Machitidwe 16:31.

Mau osaiŵalika amenewa anakambidwa ndi mtumwi Paulo ndi Sila kuuza Woyang’anila ndende mumzinda wa Filipi ku Makedoniya. Kodi io anatanthauza ciani? Kuti timvetse m’gwilizano umene ulipo pakati pa kukhulupilila mwa Yesu ndi kupulumutsidwa ku imfa, tifunika kudziŵa cifukwa cake timafa. Tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa.

Anthu sanalengedwe kuti azifa

“Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalila. Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’”—Genesis 2:15- 17.

Mulungu anaika mwamuna woyamba Adamu m’munda wa Edeni umene unali paladaiso wokongola. Munda umenewu unali ndi nyama zosiyanasiyana. Munali mitengo ya zipatso imene Adamu anauzidwa kuti azidya. Ngakhale n’telo panali mtengo umene Yehova Mulungu anaumuuza momveka bwino kuti asadye zipatso zake. Ndipo anamucenjeza kuti ngati adzadya adzafa.

Kodi Adamu analiona bwanji cenjezo limenelo? Iye anali kuidziŵa bwino imfa cifukwa anali kuona nyama zikufa. Ngati Adamu anapangidwa kuti adzafa, cenjezo la Mulungu likanakhala lopanda tanthauzo. M’malo mwake, Adamu anali kudziŵa kuti akamvela lamulo la Mulungu lakuti asadye cipatso coletsedwa adzakhala kosatha, kutanthauza kuti iye sadzafa.

Anthu ena amakhulupilila kuti chimo limene Adamu anacita linali cigololo. Koma zimenezo sizoona. Yehova anali kufuna kuti Adamu ndi mkazi wake Hava ‘abelekane, aculuke,’ ndi kuti ‘adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Conco lamulo limeneli linali loletsa mtengo weniweni. Yehova anaucha “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa” cifukwa unali kuimila ufulu wake wosankhila anthu cabwino ndi coipa. Ngati Adamu sanadye cipatso cimeneci, akanaonetsa kuti akumvela Mlengi wake komanso kuti akumuyamikila kaamba ka zinthu zoculuka zimene anam’patsa.

Adamu anafa cifukwa sanamvele Mulungu

“Kwa Adamu, Mulungu ananena kuti: ‘Cifukwa . . . wadya cipatso ca mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye, . . . Udzadya cakudya kucokela m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwelela kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela’”—Genesis 3:17, 19.

Adamu anadya cipatso cimene analetsedwa. Kucita zimenezi sinali nkhani yamaseŵela. Kunali kupanduka ndi kusayamikila zinthu zabwino zimene Yehova anamupatsa. Pamene anadya cipatso, Adamu anakana Yehova, ndipo anasankha kudziimila payekha zimene zinabweletsa zotulukapo zovulaza.

Monga mmene Yehova anakambila, m’kupita kwa nthawi Adamu anafa. Mulungu anaumba Adamu “kucokela kufumbi lapansi” ndipo anali atamuuza kuti “kufumbiko udzabwelela.” Adamu atafa sanakhale cinthu cina kapena kukhala ndi moyo kwinakwake. M’malo mwake, iye atafa anakhala wopanda moyo monga fumbi limene anamuumbila.—Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10.

Timafa cifukwa tinacokela kwa Adamu

“Ndiye cifukwa cake monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”—Aroma 5: 12.

Kusamvela kwa Adamu kunabweletsa mavuto aakulu. Pamene Adamu anacimwa anataya moyo osati wa zaka 70 kapena 80, koma wokhala kwamuyaya. Kuonjezela apo, Adamu anataya moyo wangwilo ndipo mbadwa zake zinatengela kupanda ungwilo kumeneko.

Tonse ndife mbadwa za Adamu. Popeza ndife mbadwa za Adamu, tinatengela ucimo ndipo matupi athu ndi opanda ungwilo, conco timafa. Paulo anafotokoza bwino za vutoli. Iye anati: “Ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku ucimo. Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi? Kenako iye anayankha kuti, ‘Mulungu adzatelo kudzela mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.”—Aroma 7:14, 24, 25.

Yesu anapeleka moyo wake kuti tikhale ndi moyo kosatha

“Atate anatumiza Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko.”—1 Yohane 4: 14.

Yehova Mulungu anakonza njila yothetsela mavuto amene amabwela kaamba ka ucimo ndi kutimasula kucilango ca imfa yosatha. Motani? Iye anatumiza Mwana wake wokondedwa kuti abadwe monga munthu wangwilo wofanana ndi Adamu. Mosiyana ndi Adamu, Yesu “sanacite chimo.” (1 Petulo 2:22) Cifukwa cakuti Yesu anali wangwilo, iye sanalandile cilango ca imfa ndipo akanakhala ndi moyo kosatha monga munthu.

Komabe, Yehova analola kuti Yesu aphedwe ndi adani ake. Patapita masiku atatu, Yehova anamuukitsa monga mzimu kuti m’kupita kwa nthawi adzapite kumwamba. Yesu anapeleka kwa Mulungu moyo wake wangwilo kuti abwezeletse zimene Adamu anataya ndi kuombola mbadwa zake. Yehova analandila nsembe imeneyo, kuti aliyense wokhulupilila mwa Yesu adzakhale ndi moyo wosatha.—Aroma 3: 23, 24; 1 Yohane 2:2.

Conco, Yesu anabwezeletsa zinthu zimene Adamu anataya. Anazunzidwa cifukwa ca ife kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. Baibulo limati: ‘Yesu  . .anazunzika mpaka imfa kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alaŵe imfa m’malo mwa munthu aliyense.’—Aheberi 2:9.

Makonzedwe amenewa akutiuza zambili za Yehova. Popeza kuti cilungamo ca Mulungu ndi capamwamba kwambili, zinali zosatheka kuti anthu opanda ungwilo adziombole okha. Conco, cikondi ndi cifundo cake, zinamusonkhezela kuombola anthu mwakucita cinthu cacikulu. Cinthu cimeneci cinali kupeleka Mwana wake kuti atiombole.—Aroma 5:6-8

Kuukitsidwa kwa Yesu ndi umboni wakuti enanso adzaukitsidwa

“Komabe, Kristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala cipatso coyambilila ca amene akugona mu imfa. Popeza imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Kristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akorinto 15:20- 22.

Sitikukaikila kuti Yesu anakhalapo ndi moyo kenako n’kufa. Nanga pali umboni wotani wotsimikizila kuti anaukitsidwa? Umboni wina waukulu ndi wakuti Yesu ataukitsidwa anawonekela kwa anthu ambili pa malo osiyanasiyana ndiponso pa nthawi zosiyanasiyana. Nthawi ina anaonekela kwa anthu oposa 500. Mtumwi Paulo analemba zimenezi m’kalata imene analembela Akorinto kuti anthu ena anali akali ndi moyo, kuonetsa kuti anthuwo akanacitila umboni pa zimene anaona ndi kumva zokhudza Yesu.—1 Akorinto 15: 3-8.

N’zoonekelatu kuti pamene Paulo analemba mau akuti Kristu ndi “cipatso coyambilila” ca anthu amene adzaukitsidwa, anatanthauza kuti pali ena amene adzauka. Ndipo Yesu anakamba kuti nthawi idzafika pamene “onse ali m’manda acikumbutso adzatuluka.”—Yohane 5: 28, 29.

Tifunika kukhulupilila Yesu kuti tidzakhale ndi moyo kosatha

“Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3: 16.

Buku loyambilila m’Baibulo limatiuza mmene imfa inayambila ndi mmene Paladaiso anataikila. Buku lomaliza limatiuza za nthawi imene imfa idzaonongedwa ndi kuti Mulungu adzabwezeletsa Paladaiso padziko. Limakambanso kuti anthu adzasangalala ndi moyo wamuyaya. Lemba la Chivumbulutso 21:4 limati: “imfa sidzakhalaponso.” Pofuna kutsimikizila ulosi umenewu, vesi 5 limati: “Mau awa ndi odalilika ndi oona.” Zimene Yehova amalonjeza adzakwanilitsadi.

Kodi mumakhulupilila kuti “mau awa ndi odalilika ndi oona”? Phunzilani zambili zokhudza Yesu Kristu ndi kumukhulupilila. Mukacita zimenezi Yehova adzakuyanjani. Mudzadalitsidwa kwambili palipano ndiponso mudzalandila moyo wosatha m’Paladaiso mmene simudzakhala imfa, “kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”