NKHANI YA PACIKUTO | KODI MUNGAKONDE KUPHUNZILA BAIBULO?
N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?
-
Kodi colinga ca moyo n’ciani?
-
N’cifukwa ciani anthu amavutika ndi kufa?
-
Kodi mtsogolomu muli zotani?
-
Kodi Mulungu amasamala za ine?
Kodi munadzifunsapo mafunso otelewa? Ngati ndi conco, sindinu nokha. Anthu padziko lonse amaganizila mafunso ofunika kwambili. Kodi mungapeze mayankho ake?
Anthu mamiliyoni amayankha kuti, “Inde.” Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti apeza mayankho a m’Baibulo okhutilitsa pa mafunso ao. Kodi mungakonde kudziŵa zimene Baibulo limanena? Ngati mufuna, mungapindule ndi pulogalamu yophunzila Baibulo kwaulele ndi Mboni za Yehova. *
Pa nkhani ya kuphunzila Baibulo anthu ena amanena kuti: “Ndine wotangwanika.” “Baibulo ndi lovuta kulimvetsa”. Ndipo ena amakamba kuti, “Ndimacita mantha kuyamba kuphunzila Baibulo.” Koma ena amaona zinthu mosiyanako. Iwo amakhala ndi mwai wa kuphunzila zimene Baibulo limaphunzitsa. Tiyeni tikambilane zitsanzo izi:
-
“Ndinakhalapo m’Katolika, m’Pulotesitanti, m’Hindu, M’buda wokhala m’nyumba ya ansembe ndipo ndinacita maphunzilo apamwamba a zaumulungu pa yunivesite. Ngakhale ndi conco, sindinapeze mayankho a mafunso amene ndinali nao okhudza Mulungu. Ndiyeno wa Mboni za Yehova anafika panyumba yanga. Nditakhutila ndi mayankho a m’Baibulo amene anandiuza, ndinavomela kuphunzila Baibulo.”—Gill, England.
-
“Ndinali ndi mafunso ambili okhudza moyo, koma abusa a ku Chalichi sanandiuze mayankho ogwila mtima. Koma wa Mboni za Yehova anandiyankha mafunsowo pogwilitsila nchito Baibulo. Atandifunsa ngati ndikufuna kudziŵa zambili, ndinavomela mokondwela.”—Koffi, Benin.
-
“Ndinali kufunitsitsa kudziŵa mmene akufa alili. Ndinali kukhulupilila kuti akufa angavulaze amoyo, komabe ndinali kufuna kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa. Conco ndinayamba kuphunzila Baibulo ndi m’nzanga amene anali wa Mboni.”—José, Brazil.
-
“Ndinayesako kuŵelenga Baibulo koma sindinalimvetse. Ndiyeno a Mboni za Yehova anabwela ndipo anafotokoza momveka bwino maulosi ena a m’Baibulo. Conco ndinafuna kudziŵa zina zimene ndikanaphunzila.”—Dennize, Mexico.
-
“Ndinali kukayikila ngati Mulungu amatisamaliladi. Ngakhale n’telo, ndinaganiza zakuti ndipemphele kwa Mulungu wa m’Baibulo. Ndiyeno tsiku lina a Mboni anafika panyumba n’kundipempha kuphunzila nao Baibulo ndipo ndinavomela kuphunzila nao.”—Anju, Nepal.
Zocitika zimenezi zimatikumbutsa mau a Yesu akuti: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu.” (Mateyu 5:3) Kunenadi zoona, anthu mwacibadwa amafuna kudziŵa Mulungu. Cifukwa iye ndi amene angakwanilitse zofuna zao ndipo amakwanilitsa zimenezo kudzela m’Mau ake Baibulo.
Kodi phunzilo la Baibulo n’ciani? Nanga lingakupindulitseni bwanji? Mafunso awa ayankhidwa m’nkhani yotsatila.
^ par. 8 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.