Kuyankha Mafunso A m’Baibulo
N’cifukwa ciani tiyenela kukumbukila imfa ya Yesu?
Imfa ya Yesu ndi yapadela kwambili m’mbili ya anthu. Iye anafa kuti abwezeletse moyo wa anthu mmene unafunika kukhalila. Anthu sanalengedwe kuti azicita zoipa, kudwala kapena kuti azifa. (Genesis 1: 31) Koma ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu woyamba, Adamu. Ngakhale n’conco, Yesu anapeleka moyo wake kutipulumutsa ku ucimo ndi imfa.—Ŵelengani Mateyu 20:28; Aroma 6:23.
Mulungu anaonetsa cikondi cacikulu potumiza mwana wake padziko lapansi kuti adzatifele. (1 Yohane 4:9, 10) Yesu anauza otsatila ake kuti azikumbukila imfa yake pa mwambo wosavuta mwa kugwilitsila nchito mkate ndi vinyo. Mwa kucita zimenezi caka ciliconse timasonyeza kuyamikila cikondi cimene Mulungu ndi Yesu anationetsa.—Ŵelengani Luka 22:19, 20.
Ndani ayenela kudya mkate ndi kumwa vinyo?
Nthawi yoyamba pamene Yesu anali kuuza ophunzila ake kuti azikumbukila imfa yake, anachula za pangano. (Mateyu 26:26-28) Panganoli linatsegula mwai kwa ophunzilawo ndi anthu ena ocepa wokakhala mafumu ndi ansembe kumwamba pamodzi ndi Yesu. Ngakhale kuti anthu mamiliyoni ambili amakumbukila imfa ya Yesu, ndi okhawo ali m’panganoli amene ayenela kudya mkate ndi kumwa vinyo.—Ŵelengani Chivumbulutso 5:10.
Kwa zaka pafupifupi 2,000, Yehova wakhala akusankha amene adzakhale mafumu. (Luka 12:32) Ciŵelengelo cao ndi cocepa poyelekezela ndi amene adzakhala padziko kosatha.—Ŵelengani Chivumbulutso 7:4, 9, 17.