Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cinyengo, Kodi Cidzatha?

Cinyengo, Kodi Cidzatha?

PANAYIOTA anakulila pacilumba cina ca ku Mediterranean. Ali wacitsikana, anali kukonda kwambili zandale. Patapita nthawi, anakhala kalembela wa cipani candale cimene cinali m’mudzi wao. Iye analinso kupita kunyumba ndi nyumba kupemphetsa ndalama za cipani cao. Koma m’kupita kwa nthawi, Panayiota anakhumudwa kwambili. Ngakhale kuti mamembala a cipani cao anali kugwilizana kwambili, makhalidwe monga kukondela, kufuna kuchuka, mikangano, ndi nsanje zinali zofala.

Daniel analeledwa m’banja lokonda za cipembedzo ku Ireland. Ngakhale n’telo, iye akumbukila bwino cinyengo ca abusa amene anali kuledzela, kuchova njuga, ndi kuba ndalama za m’mbale ya zopeleka kwinaku akumuphunzitsa kuti ngati wacimwa adzaochedwa ku moto wa helo.

Jeffery wakhala akucita zamalonda ndi makampani a masitima apamadzi ocokela m’maiko a United Kingdom ndi United States. Iye akumbukila zocitika zosiyanasiyana pamene makasitomala ndi ocita zamalonda anali kucita zinthu mwacinyengo pokambilana ndi akuluakulu a boma. Anali kucita zimenezi n’colinga cakuti asunge mapangano ao.

Izi ndi zitsanzo zocepa cabe za anthu amene amacita cinyengo. Masiku ano, cinyengo cili paliponse kaya m’zandale, m’zacipembedzo kapena m’zamalonda. Liu lacingelezi lomasulidwa kuti “cinyengo” linacokela ku liu la cigiriki limene limakamba za ocita maseŵelo amene kaŵilikaŵili amadzibisa nkhope kuti anthu asawadziŵe. M’kupita kwa nthawi, anthu anayamba kuseŵenzetsa liu limeneli pofuna kukamba za munthu amene amacita zinthu mwacinyengo kuti apeze zimene afuna.

Cinyengo cingapangitse anthu ena kukhumudwa ndi kukwiya kwambili. Mokhudzidwa mtima, io angafunse kuti: “Kodi Cinyengo cidzatha?” Mau a Mulungu amatitsimikizila kuti cinyengo cidzatha.

MMENE MULUNGU NDI MWANA WAKE AMAONELA CINYENGO

Baibulo limafotokoza mmene cinyengo cinayambila. Limatiuza kuti cinyengo cinayambila kumwamba ndi colengedwa cauzimu osati anthu. Paciyambi, Satana mdyelekezi kupitila mwa njoka monga cobisalilamo, ananamiza Hava, mkazi woyamba ndipo anadzionetsa ngati wabwino pofuna kum’soceletsa. (Genesis 3:1-5) Kucokela nthawiyo, anthu ambili amacita zinthu mwacinyengo kuti akwanilitse zolinga zao zadyela.

Mtundu wa Aisiraeli utayamba kulambila konama ndiponso kucita cinyengo ca kuuzimu, Mulungu anawacenjeza mobwelezabweleza za zotsatilapo zake. Kupitila mwa mneneli Yesaya, Yehova Mulungu anati: “Anthu awa ayandikila kwa ine ndi pakamwa pao pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yao yokha koma mtima wao auika kutali ndi ine.” (Yesaya 29:13) Mtunduwo utalephela kusintha, Mulungu analola olamulila amphamvu kuti aononge Yerusalemu ndi kacisi wake, likulu la cipembedzo ca Aisiraeli. Coyamba, Ababulo anaononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., kenako asilikali a Aroma anaononga mzindawo mu 70 C.E. Kukamba zoona, Mulungu salekelela zacinyengo.

Mulungu ndi Mwana Wake, Yesu, amakonda anthu amene ndi oona mtima ndi opanda cinyengo. Mwacitsanzo, kuciyambi kwa utumiki wa Yesu, mwamuna wina dzina lake Natanayeli anabwela kwa iye. Atamuona, Yesu anati: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.” (Yohane 1:47) Natanayeli amene anali kuchedwanso kuti Batolomeyo, anakhala mmodzi wa atumwi 12 a Yesu.—Luka 6:13-16.

Nthawi zambili Yesu anali kukhala ndi ophunzila ake, ndipo anali kuwaphunzitsa zinthu zokhudza Mulungu. Iwo sanafunike kukhala acinyengo. Pofuna kuwacenjeza, Yesu anatsutsa mwamphamvu atsogoleli acipembedzo a m’nthawiyo amene anali acinyengo. Onani mmene io anali kucitila zimenezi.

Anali kucita “cilungamo” kuti anthu aŵaone. Yesu anauza omvela ake kuti: “Samalani kuti musamacite cilungamo canu pamaso pa anthu ndi colinga cakuti akuoneni . . . muja amacitila onyenga.” Iye anawauzanso kuti azipeleka mphatso zacifundo ‘mwamseli’ kapena kuti mosaonetsela. Iwo anafunikanso kupemphela mwamseli osati modzionetsela kwa anthu. Kucita zimenezo kukanapangitsa kulambila kwao kukhala kovomelezeka kwa Atate wake.—Mateyu 6:1-6.

Anali kuweluza ena mwamsanga. Yesu anati: “Wonyenga iwe! Yamba wacotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatelo udzatha kuona bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mateyu 7:5) Ngati munthu amaganizila kwambili zolakwa za ena m’malo moganizila zolakwa zake zazikulu, amadzipanga kukhala munthu wosiyana ndi mmene alili. Zoona zake n’zakuti anthu “onse ndi ocimwa ndipo ndi opeleŵela pa ulemelelo wa Mulungu.”—Aroma 3:23.

Anali kubisa zolinga zao zoipa. Panthawi ina, ophunzila a Afarisi ndi acipani ca Herode anafika kwa Yesu ndi kumufunsa pankhani ya msonkho. Pofuna kumukopa, io anati: “Mphunzitsi, tikudziŵa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi.” Kenako pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ai?” Yesu anawayankha kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa?” Moyenelela Yesu anawacha kuti onyenga cifukwa sanali kufuna kumva yankho la funso lao, koma anali kufuna kuti “am’kole m’mawu ake.”—Mateyu 22:15-22.

Akristu oona amaonetsana “cikondi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumtima cabwino, ndiponso m’cikhulupililo copanda cinyengo.”​—1 TIMOTEYO 1:5

Pamene mpingo wacikristu unakhazikitsidwa pa Pentekosite mu 33 C.E., coonadi ndi kuona mtima zinayamba kuonjezeka. Akristu oona anacita khama kuthetsa cinyengo ciliconse cimene anali naco. Mwacitsanzo, Petulo mmodzi wa atumwi  12, analimbikitsa Akristu anzake kuti akhale ‘omvela coonadi ndi kukonda abale mopanda cinyengo.’ (1 Petulo 1:22) Mtumwi Paulo, analimbikitsa anchito anzake kuti akhale ndi “cikondi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumtima cabwino, ndiponso m’cikhulupililo copanda cinyengo.”—1 Timoteyo 1:5.

MPHAMVU YA MAU A MULUNGU

Zimene Yesu ndi atumwi ake anali kuphunzitsa, n’zothandiza kwambili masiku ano monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi. Pankhani imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikila zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheberi 4:12) Kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa ndi kuyesetsa kucita zimene limakamba, kwathandiza anthu ambili kusiya cinyengo ndi kuyamba kucita cilungamo. Kumbukilani zitsanzo zitatu za anthu amene tawachula poyamba aja.

“Ndinaona anthu akuonetsana cikondi ceniceni.”​—PANAYIOTA

Panayiota anasintha umoyo wake, pamene anapezeka pamisonkhano ya mpingo ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Kumeneko, iye sanaone munthu aliyense akucita zinthu mwacinyengo pofuna kukondweletsa ena. Panayiota anati: “Pamisonkhano imeneyi, ndinaona anthu akuonetsana cikondi ceniceni, cimene sindinacionepo zaka zonse zimene ndinali kucita zandale.”

Panayiota anayamba kuphunzila Baibulo kenako anabatizidwa. Iye wakhala m’coonadi zaka 30 tsopano. Iye anati: “Tsopano ndili ndi moyo waphindu, osati cifukwa copita kunyumba ndi nyumba kupemphetsa ndalama za cipani, koma cifukwa colalikila za Ufumu wa Mulungu, umene udzabweletsa cilungamo padziko lapansi.”

“Sindinali kufuna kuti Akristu anzanga aziona kuti ndine munthu wabwino pamene sindinali conco.”​—DANIEL

Daniel anapita patsogolo mwakuuzimu ndipo anapatsidwa maudindo osiyanasiyana. Patapita zaka zocepa, iye analakwitsa zinazake ndipo cikumbumtima cake cinayamba kumuvutitsa. Iye anati: “Nditakumbukila za cinyengo cimene cinali m’chalichi canga cakale, ndinasankha kutula pansi maudindo amenewa. Sindinali kufuna kuti Akristu anzanga aziona kuti ndine munthu wabwino pamene sindinali conco.”

Patapita nthawi, Daniel anasintha ndipo anayambanso kutumikila pa maudindo ake mumpingo ali ndi cikumbumtima cabwino. Kuona mtima kotele kumapezeka kokha pakati pa anthu amene amatumikila Mulungu mopanda cinyengo. Iwo aphunzila kucotsa “mtanda wa denga” m’maso mwao asanacotse “kacitsotso” m’maso mwa m’bale wao.

“Ndinazindikila kuti sindiyenela kucita cinyengo. . . . Ndinakhala ndi cikumbumtima cabwino.”​—JEFFERY

Jeffery amene anali kucita zamalonda, anati: “Nditapita patsogolo kuphunzila Baibulo, ndinazindikila kuti sindiyenela kucita cinyengo pocita pangano la zamalonda. Ndinakhala ndi cikumbumtima cabwino cifukwa coŵelenga Malemba monga Miyambo 11:1 limene limakamba kuti ‘masikelo acinyengo amam’nyansa Yehova.’” Mosiyana ndi anthu amene anafunsa Yesu funso lokhudza msonkho, Jeffery anaphunzila kuthetsa maganizo olakwika pocita zinthu ndi Akristu anzake ndi anthu ena.

Mboni za Yehova mamiliyoni padziko lonse zimayesetsa kucita zimene zaphunzila m’Baibulo. Izo zimayesetsa “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.” (Aefeso 4:24) Tikupemphani kuti mudziŵe zambili zokhudza Mboni za Yehova, zimene zimakhulupilila, ndi mmene zingakuthandizileni kudziŵa zimene Mulungu walonjeza kudzacita m’dziko latsopano. M’dziko limenelo “mudzakhala cilungamo” ndipo cinyengo sicidzakhalamonso.—2 Petulo 3:13.