Kodi Mudziŵa
Kodi Ayuda amene anapezeka pa Pentekosite mu 33 C.E. anacokeladi “mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo”?
Lemba la Machitidwe 2:5-11 lionetsa kuculuka kwa anthu amene anapezeka pa Pentekosite mu 33 C.E. Wolemba nkhani wina waciyuda, dzina lake Philo, anatsimikizila zimenezi.
Ponena za anthu amene anali kupita ku Yerusalemu, Philo analemba kuti: “Anthu osaŵelengeka, ocokela m’mizinda yosaŵelengeka, ena ocokela kum’maŵa, kumadzulo, kum’mwela, ndi kumpoto, anali kubwela kucikondwelelo ciliconse. Ndipo ena anali kuyenda wa pansi, kapena pa bwato.” Iye anagwilanso mau a mu kalata ya Agiripa Woyamba, mdzukulu wa Herode Wamkulu, yopita kwa Mfumu Yaciroma dzina lake Kaligula. M’kalatayi, Agiripa analemba zokhuza Yerusalemu kuti: “Mzinda Woyela . . . si mzinda wa dziko la Yudeya cabe ai, koma ndi wa maiko ena ambili kuphatikizapo oyandikana nalo. Izi zili conco cifukwa cakuti maiko enawa akhala akulamulidwa ndi mafumu aciyuda.”
Mfumu Agripa analemba maiko amene mafumu aciyuda anali kulamulila kuphatikizapo madela akutali monga Mesopotamiya, kumpoto kwa Africa, Asia Minor, Girisi, ndi zilumba za pa nyanja ya Mediterranean. Katswili wina wa zamaphunzilo, dzina lake Joachim Jeremias, analemba kuti: “Ngakhale kuti zimene Agripa analemba sizichula mwacindunji za maulendo opita ku Yerusalemu, mfundo ndi yakuti anthu anali kupita ku Yerusalemu cifukwa Ayuda onse acikulile anali kulamulidwa kupanga maulendo amenewa.—Deuteronomo 16:16.
Kodi anthu masauzande ambili amene anali kubwela ku Yerusalemu kudzacita zikondwelelo zaciyuda anali kugona kuti?
Ayuda anali kucita zikondwelelo zitatu caka ciliconse ku Yerusalemu. Zikondwelelo zimenezi ndi Pasika, Pentekosite, ndi Cikondwelelo ca Misasa. M’nthawi ya Atumwi, anthu masauzande ambili anali kupita ku Yerusalemu kukacita zikondwelelo zimenezi. Anthu amenewa anali kucokela m’dziko la Aisiraeli ndiponso m’dziko lililonse kumene kunali kukhala Ayuda. (Luka 2:41, 42; Machitidwe 2:1, 5-11) Conco, alendo onse amene anali kufika pa zikondwelelo zimenezi anali kufunika kupeza malo ogona.
Ena anali kugona m’nyumba za anzao, ndipo ena anali kugona ku nyumba za alendo. Ambili anali kumanga misasa yogonamo mkati kapena kunja kwa mzinda. Pa tsiku lothela kukhala ku Yerusalemu, Yesu anakagona mumzinda wapafupi wa Betaniya. (Mateyu 21:17)
Mabwinja a nyumba zingapo amene anali pafupi ndi pamene panali kacisi apezeka ndi mabeseni osambilamo. Anthu amaganiza kuti m’nyumba zimenezi ndi mmene anthu anali kugona ndiponso kudziyeletsa asanaloŵe m’kacisi. Mau amene analembedwa pa cipupa ca nyumba ina, akuonetsa kuti munthu wina dzina lake Theodotus, amene anali wansembe ndiponso mtsogoleli wa sunagoge, ndi amene “anamanga sunagoge woŵelengelamo Tora . . . komanso nyumba yogona anthu ambili, zipinda, ndiponso mabeseni osungilamo madzi.”