NKHANI YA PACIKUTO—AMUNA ANAYI OKWELA PA MAHOSI—KODI AMAKUKHUDZANI BWANJI?
Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
Amuna anayi okwela pa mahosi angaoneke odabwitsa ndi ocititsa mantha. Koma sitiyenela kuwaona conco. Cifukwa ciani? Cifukwa Baibo na zimene zakhala zikucitika masiku ano, zimatithandiza kudziŵa zimene wokwela pa hosi aliyense akuimila. Amuna okwela pa mahosi abweletsa mavuto padziko lapansi. Koma kumvetsetsa nkhani yake, kungakuthandizeni imwe na banja lanu kukhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino. Motani? Coyamba, tiyeni tikambilane zimene wokwela pa hosi aliyense akuimila.
WOKWELA PA HOSI YOYELA
Masomphenya akuyamba motele: “Ndinaona hachi yoyela. Wokwelapo wake ananyamula uta. Iye anapatsidwa cisoti cacifumu, ndi kupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.”—Chivumbulutso 6:2.
Kodi wokwela pa hosi yoyela n’ndani? Yankho ipezeka m’buku imodzi-modzi ya m’Baibo ya Chivumbulutso. M’caputa cina m’bukuli, iye amachedwa “Mau a Mulungu.” (Chivumbulutso 19:11-13) Yesu Khristu ndiye amachedwa Mau, cifukwa ni wokambilako Mulungu. (Yohane 1:1, 14) Amachedwanso kuti “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” komanso kuti “Wokhulupilika ndi Woona.” (Chivumbulutso 19:16) N’zoonekelatu kuti monga mfumu yankhondo, iye ali na mphamvu zoculuka, koma saseŵenzetsa mphamvuzo molakwa kapena mosayenela. Koma pakubuka mafunso ena.
N’ndani anapatsa Yesu mphamvu zogonjetsa? (Chivumbulutso 6:2) M’masomphenya, mneneli Danieli anaona Mesiya wooneka monga “mwana wa munthu” akupatsidwa “ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu.” Anam’patsa ndi “Wamasiku Ambili,” Yehova Mulungu. * (Danieli 7:13, 14). Conco, Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anapatsa Yesu mphamvu zolamulila na kupeleka ciweluzo. Hosi yoyela ni cizindikilo coyenelela ca nkhondo yacilungamo yomenyedwa na Mwana wa Mulungu, cifukwa m’Malemba kala yoyela imaimila cilungamo nthawi zambili.—Chivumbulutso 3:4; 7:9, 13, 14.
Kodi ni liti pamene amuna amenewa anakwela pa mahosi na kuyamba kuthamanga? Onani kuti wokwela pa hosi yoyamba, Yesu, anayamba ulendo wake pamene anapatsidwa cisoti cacifumu. (Chivumbulutso 6:2) Kodi Yesu anaikidwa liti kukhala Mfumu kumwamba? Iye sanaikidwe pambuyo pobwelela kumwamba ataukitsidwa. Baibo imaonetsa kuti anafunika kuyembekezela. (Aheberi 10:12, 13) Yesu anafotokozela ophunzila ake mmene angadziŵile kuti nthawi ya kuyembekezela yasila, ndi kuti wayamba kulamulila kumwamba. Anakamba kuti kuciyambi kwa ulamulilo wake, zinthu padzikoli zidzaipila-ipila. Panali kudzakhala nkhondo, njala, ndi milili. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Nkhondo yoyamba ya dziko lonse itayamba mu 1914, umboni unaonekelatu wakuti mtundu wa anthu waloŵa m’nthawi yovuta imene Baibo imakamba kuti “masiku otsiliza.”—2 Timoteyo 3:1-5.
Popeza Yesu anakhala Mfumu mu 1914, n’cifukwa ciani zinthu padzikoli zikuipila-ipila? Cifukwa panthawiyo, Yesu anayamba kulamulila kumwamba osati padziko lapansi. Ndiyeno kumwamba kunayambika nkhondo. Mfumu yatsopano, Yesu, amene akuchedwa Mikayeli, anaponya Satana ndi ziŵanda zake padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-9, 12) Panthawi ino, Satana ni wokalipa kwambili cifukwa adziŵa kuti ali na kanthawi kocepa. Posacedwa, Mulungu adzawononga Satana ndi kukwanilitsa cifunilo cake padziko lapansi. (Mateyu 6:10) Tsopano, tiyeni tikambilane mmene amuna ena atatu okwela pa mahosi atithandizila kutsimikiza kuti tikukhala mu “masiku otsiliza” komanso ovuta. Mosiyana ndi wokwela pa hosi yoyamba, amene akuimila munthu weni-weni, mahosi atatu otsatila akuimila zocitika zimene zikhudza anthu ambili padziko lonse.
WOKWELA PA HOSI YOFIILA
“Pamenepo, hachi ina inatulukila. Imeneyi inali yofiila ngati moto. Wokwelapo wake analoledwa kucotsa mtendele padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.”—Chivumbulutso 6:4.
Wokwela pa hosi imeneyi akuimila nkhondo. Onani kuti sakucotsa mtendele m’maiko ocepa cabe, koma padziko lonse. Mu 1914, kwa nthawi yoyamba, padziko panabuka nkhondo imene inakhudza maiko onse. Pambuyo pake, panabukanso nkhondo yaciŵili ya dziko lonse imene inawononga koposa. Malipoti aonetsa kuti anthu opitilila 100 miliyoni afa pankhondo kucokela 1914. Kuwonjezela apo, anthu ena ambili-mbili anapwetekedwa maningi.
Kodi nkhondo yafika pamlingo wotani masiku ano? Kwa nthawi yoyamba, anthu afika pakuti angathe kufafaniza mtundu wonse wa anthu. Ngakhale mabungwe amene amati ni osungitsa mtendele, monga United Nations, alephela kuimitsa wokwela pa hosi yofiila.
WOKWELA PA HOSI YAKUDA
“Nditayang’ana, ndinaona hachi yakuda. Wokwelapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mau ngati ocokela pakati pa zamoyo zinayi zija. Mauwo anali akuti: ‘Kilogalamu imodzi ya tiligu, mtengo wake ukhala dinali imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balele, mtengo wake ukhala dinali imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.’”—Chivumbulutso 6:5, 6.
Wokwela pa hosi imeneyi akuimila njala. Lembali likuonetsa kucepekela kwa cakudya cakuti kilogalamu imodzi ya tiligu ingagulidwe ndi dinali imodzi, imene inali malipilo a tsiku lathunthu m’zaka 100 zoyambilila. (Mateyu 20:2) Ndalama imodzi-modziyo ingagule makilogalamu atatu a balele, cakudya cimene anthu sanali kucikonda poyelekeza ndi tiligu. Kodi banja lalikulu lingadye masiku angati cakudya cimeneco? Anthu akucenjezedwa kuti asawononge ngakhale cakudya cimene anali kudya nthawi zonse, monga mafuta a maolivi ndi vinyo.
Kodi tauona umboni woonetsa kuti wokwela pa hosi yakuda ali pa liŵilo kucokela mu 1914? Inde! Anthu pafupi-fupi 70 miliyoni anafa ndi njala m’zaka za m’ma 1900. Lipoti lina linati “anthu 805 miliyoni anali kudya mopeleŵela mu 2012 mpaka 2014.” Lipoti linanso linati: “Caka ciliconse, anthu amene amafa ndi njala ni ambili kuposa amene amafa ndi matenda a AIDS, maleliya, na TB tikawaphatikiza pamodzi.” Ngakhale kuti anthu ayesa-yesa kuthetsa njala, wokwela pa hosi yakuda akupitiliza kuthamanga.
WOKWELA PA HOSI YOTUŴA
“Nditayang’ana, ndinaona hachi yotuŵa. Wokwelapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda anali kumutsatila pafupi kwambili. Iwo anapatsidwa ulamulilo pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi lupanga lalitali, njala, mlili wakupha, ndi zilombo za padziko lapansi.”—Chivumbulutso 6:8.
Wokwela pa hosi yacinayi akuimila imfa imene ikucitika cifukwa ca milili ndi zinthu zina. Pambuyo pa 1914, cimfine ca ku Spain cinapha anthu mamiliyoni ambili. N’kutheka kuti anthu 500 miliyoni anadwalapo matendawa, pafupi-fupi munthu mmodzi pa atatu alionse panthawiyo.
Koma cimfine ca ku Spain cinali ciyambi cabe. Akatswili aonetsa kuti anthu ofika m’mahandiledi miliyoni anafa ndi nthomba m’zaka za m’ma 1900. Mpaka lelo, anthu mamiliyoni ambili amafa ndi matenda a AIDS, TB, na maleliya, ngakhale kuti a zacipatala ayesa-yesa kufufuza mankhwala.
Zoonadi, anthu ambili afa cifukwa ca nkhondo,
njala, ndi milili. Manda akupitiliza kutenga anthu, ndipo siyapeleka ciyembekezo ciliconse.ZINTHU ZIDZAKHALA BWINO KUTSOGOLO
Nthawi yovuta ino idzasila manje-manje. Kumbukilani kuti: Yesu ‘anapita kukagonjetsa’ mu 1914. Ngakhale kuti Yesu anaponya Satana padziko lapansi, iye akalibe kutsiliza kugonjetsa. (Chivumbulutso 6:2; 12:9, 12.) Posacedwa, pa Aramagedo, Yesu adzathetsa ulamulilo wa Satana, na kuwononga onse amene ali kumbali ya Mdyelekezi. (Chivumbulutso 20:1-3) Yesu sadzangotsiliza mavuto amene amuna atatu okwela pa mahosi abweletsa, koma adzakonzanso zinthu zimene iwo awononga. Adzacita bwanji zimenezo? Onani malonjezo a m’Baibo awa.
M’malo mwa nkhondo, padzakhala mtendele. Yehova ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Adzathyola uta ndi kudula-dula mkondo.’ (Salimo 46:9) Koma anthu okonda mtendele, “adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:11.
M’malo mwa njala, padzakhala cakudya cambili. “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:16.
M’malo mwa milili na imfa, anthu onse adzakhala na thanzi labwino komanso moyo wosatha. Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.
Pamene Yesu anali padziko lapansi, anacita zinthu zoonetsa kuti umoyo udzakhala bwino akadzayamba kulamulila. Iye analimbikitsa mtendele, anadyetsa anthu ambili mozizwitsa, anacilitsa odwala, na kuukitsa akufa.—Mateyu 12:15; 14:19-21; 26:52; Yohane 11:43, 44.
Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuonetsani m’Baibo yanu zimene mungacite kuti mukhale okonzeka pamene mapeto a okwela pa mahosi afika. Kodi mungakonde kuphunzila zambili??