Onani zimene zilipo

Nyumba ya wailesi ya WBBR mu 1924

ZA M’NKHOKWE YATHU

Kufalitsa Uthenga Wabwino Kupitila pa Wailesi Komanso pa TV

Kufalitsa Uthenga Wabwino Kupitila pa Wailesi Komanso pa TV

 Pa Sondo madzulo, pa February 24, 1924, nyumba ya wailesi ya Ophunzila Baibo a yochedwa WBBR inayamba kugwila nchito kwa nthawi yoyamba. Kodi pulogilamu yoyamba imeneyo inali na zotani? Nanga ndani anaimvetsela? Kodi Mboni za Yehova zacita zotani popitiliza kuseŵenzetsa zipangizo zamakono polengeza “Uthenga wabwino wa Ufumu . . . padziko lonse lapansi kumene kuli anthu”?—Mateyu 24:14.

Wa ku makina m’nyumba ya wailesi ya WBBR

“Tinayamba Kuulutsa”

 Pulogilamu yoyambayi inayamba na nthawi ya 20:30, ndipo inacitika kwa maola aŵili. Inaulutsidwa kucokela ku nyumba ya wailesi yatsopano ku dela la Staten Island, mu mzinda wa New York. M’bale Ralph Leffler amene nchito yake inali kuonetsetsa kuti zonse zikumveka bwino, anati anthu onse mu nyumba ya mphempo “anali okondwela koma analinso na mantha.” Anadzifunsa kuti, “Kodi kuli aliyense amene adzamvetsela pulogilamu yathuyi?” Anapitiliza kuti, “N’nayatsa magetsi ndipo tinayamba kuulutsa, tili na cidalilo cakuti zonse zidzayenda bwino

 M’bale Victor Schmidt ndiye anali woulutsa pulogilamu yosaiŵalika imeneyi. Ndiye analinso woyang’anila nyumba ya wailesi. Anayambitsa pulogilamu mwa kuitanitsa akatswili a nyimbo. Onse anali Ophunzila Baibo. M’bale woyamba analiza nyimbo pa piyano. Kenako, Mlongo Cora Wellman anaimba nyimbo yakuti “99,” yokamba za fanizo la Yesu la nkhosa zotayika. (Luka 15:4-7) Panaimbidwanso nyimbo zina, kuphatikizapo imene inaimbidwa na M’bale Frederick W. Franz yakuti “Wolapa.” Nyimboyi inali kukamba za mwana woloŵelela—Luka 15:11-25.

Pulogilamu ya tsiku loyamba ya pa WBBR

 Joseph F. Rutherford, amene anali kutsogolela Ophunzila Baibo pa nthawiyo, anakamba nkhani yopatulila nyumba ya wailesiyo. Iye anati colinga ca wailesiyo “n’kupititsa patsogolo ufumu wa Mesiya.” Anatinso, “Popeza Ambuye walola anthu kupanga wailesi, sitikayikila zoti akufuna kuti tiiseŵenzetse pophunzitsa anthu za kukwanilitsidwa kwa maulosi ake

“Panalibe Ngakhale Liwu Limodzi Limene Silinamveke”

 Ambili a kumpoto cakum’maŵa kwa America anamvetsela pulogilamu imeneyo. Mwamuna wina wa ku dela la Morrisville, mu mzinda wa Vermont womwe unali pa mtunda wa makilomita 320 kucokela ku nyumba ya wailesiyo, anakamba kuti: “Ndine wokondwela kukuuzani kuti zonse zinamveka bwino, makamaka mawu a M’bale Rutherford . . . Panalibe ngakhale liwu limodzi limene silinamveke.” Ngakhale mwamuna wina wa ku Monticello, mu mzinda wa Florida anakwanitsa kumvetsela pulogilamu imeneyi. Nyumba ya wailesi imeneyi inathandiza kwambili, ndipo anthu analemba makalata ambili oyamikila.

Joseph Rutherford ali pa maikolofoni m’cipinda cojambulila mawu ca WBBR. Victor Schmidt ndiye anali woulutsa

 Nyumba ya wailesi imeneyo inapitiliza kuulutsa uthenga wa Ufumu kwa zaka 33 b maka-maka kumpoto cakum’maŵa kwa America. Koma nthawi zina, nyumba ya wailesi ya WBBR inali kulumikizana na nyumba zina za wailesi moti uthenga wake unali kufika kwa anthu mamiliyoni a mu America, a ku Canada, ngakhale a ku madela akutali. Buku la Pacaka la mu 1975 la Mboni za Yehova linati: “Pofika mu 1933, caka cimene wailesiyo inafalitsa uthenga kwa anthu ambili kuposa kale lonse, panali nyumba za wailesi 408 zimene zinali kugwilitsidwa nchito kufalitsa uthenga ku zigawo 6 za dziko lapansi, ndipo nkhani za m’Baibo zosiyanayana zokwana 23,783 zinali kuulutsidwa . . . Pa nthawiyo, mapulogilamu a Watch Tower anali kuulutsidwa na nyumba za wailesi zosiyanasiyana pa nthawi imodzi. Anthu kulikonse anali kumvetsela mawu a coonadi otamanda Mulungu akangotsegula wailesi yawo.”

Anayamba Kugwilitsa Nchito Kwambili Ulaliki wa Nyumba na Nyumba M’malo mwa Wailesi

 Ophunzila Baibo atayamba kuseŵenzetsa pulogilamu ya WBBR, pa avaleji, ku America kunali Alengezi a Ufumu okwana 1,064. Mapulogilamu a pa wailesi amenewa anathandiza gulu locepa limeneli kulalikila uthenga wabwino kwa anthu ambili. Koma pofika mu 1957, ku America kunali Alengezi a Ufumu okwana 187,762 pa avaleji komanso okwana 653,273 padziko lonse. Cinathandiza kwambili ni malangizo amene anali kuphunzila pa misonkhano ya mpingo. Abale na alongo akhama amenewo, anakhala aluso kwambili pocita ulaliki wa kunyumba na nyumba komanso njila zina zolalikilila.

 Zotulukapo zabwino zimenezi zinapangitsa abale otsogolela kuunikanso mapindu oseŵenzetsa wailesi poyelekezela na ulaliki wa nyumba na nyumba. Kodi panakhala zotsatilapo zotani? Anapanga cigamulo cogulitsa nyumba ya wailesi ya WBBR. Pa nthawiyo, imeneyo ndiyo inali nyumba yawo ya wailesi yothela imene a Watchtower Society anali akali kuiseŵenzetsa. Nyumbayo inagulitsidwa pa April 15, 1957. Pa mwambo wa pulogilamu yothela pa April 14, M’bale Nathan H. Knorr anafunsidwa cifukwa cake anali kugulitsa nyumba ya wailesiyo. Anafotokoza kuti cacikulu cimene cinapangitsa kuti ciŵelengelo ca Mboni za Yehova ciwonjezeke ni ulaliki wa nyumba na nyumba. Anakambanso kuti: “N’zoona kuti anthu oculuka athandizidwa kwambili na mapulogilamu a WBBR. Koma kuwonjezeka kwa ziŵelengelo n’kofanana pakati pa madela okhala na WBBR na madela ena omwe samvetselako mapulogilamu amenewa.” Pa cifukwa cimeneci, abale anaona kuti ulaliki wa nyumba na nyumba ungathandize kwambili poyelekezela na wailesi. Komabe, awa sindiwo anali mapeto a kufalitsa uthenga wabwino poseŵenzetsa wailesi kapena TV. Patapita zaka zambili, tinayambanso kugwilitsa nchito zida zimenezi, koma m’njila yatsopano.

Kuseŵenzetsa Wailesi na TV Masiku Ano

 Pa October 6, 2014, m’gulu la Yehova munacitika cinthu cocititsa cidwi kwambili. Wailesi ya kanema ya pa intaneti yochedwa JW Broadcasting inayamba kugwila nchito pa tsikuli. Mboni za Yehova komanso anthu ena amatamba na kumvetsela mapulogilamu a pa mwezi poseŵenzetsa intaneti, JW Laibulale, komanso zipangizo zina zamakono. c Ngakhale n’telo, anthu a Yehova m’madela ena akali kuseŵenzetsa wailesi na TV pofalitsa uthenga wabwino. Kodi amacita motani zimenezi?

Pulogilamu yoyamba ya JW Broadcasting mu October 2014

 M’zaka za posacedwapa, gulu la Yehova lagwilitsa nchito machanelo a pa wailesi na pa TV a makampani ena poulutsa misonkhano ya mlungu na mlungu komanso misonkhano ya cigawo ku madela komwe intaneti ni yovuta. Anthu ambili amene si Mboni za Yehova, amvetselako mapulogilamu amenewa. Ena mwa iwo ali na cidwi cophunzila Baibo. Mwacitsanzo, m’caka ca 2021 na 2022, oyang’anila nyumba za wailesi anauza ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku East Africa kuti anthu ambili amene si Mboni amaiyamikila ngako misonkhano yathu. Anthu angapo amene anamvetsela misonkhano yathu ku Kenya, ku South Sudan, komanso ku Tanzania anafika ngakhale popempha phunzilo la Baibo.

 Koma kwakukulukulu, Mboni za Yehova zimaseŵenzetsa ulaliki wa nyumba na nyumba, ulaliki wa tumasitandi komanso webusaiti ya jw.org pofalitsa uthenga wa Ufumu padziko lonse la pansi. Pa webusaiti yathu pali Baibo na zofalitsa zofotokoza Baibo m’zinenelo zoposa 1,080 zimene anthu acidwi angaŵelenge mosavuta. Ndipo zonsezi n’zaulele. Angapezenso mayankho a mafunso awo kucokela m’Baibo komanso kudziŵa kumene misonkhano ya Cikhristu imacitikila. Cifukwa ca zimenezi, Mboni za Yehova zapangitsa kuti uthenga wabwino wa Ufumu ufalikile kwambili kuposa kale lonse! Kunena zoona, monga mmene Baibo inakambila, uthengawu ukulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mateyu 24:14.

a Mu 1931, Ophunzila Baibo anayamba kudziŵika na dzina lakuti Mboni za Yehova.

b Kwa kanthawi, Mboni za Yehova zinali na nyumba zina za wailesi m’mayiko ena monga ku Australia na ku Canada.