Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Chanelo ya JW Ifika ku Madela Kumene Kulibe Intaneti

Chanelo ya JW Ifika ku Madela Kumene Kulibe Intaneti

APRIL 1, 2021

 Mwezi uliwonse, timayembekezela mwacidwi kumvetsela mapulogilamu auzimu na mavidiyo, zimene zimatulutsidwa pa JW Broadcasting. Komabe, abale athu ambili mu Africa sakwanitsa kucita daunilodi mapulogilamu amenewa pa Intaneti. Cifukwa ciani?

 M’madela ambili mu Africa mulibe Intaneti. Ndipo kumene Intaneti iliko, nthawi zambili imakhala yopanda mphamvu kapena yodula kwambili. Mwacitsanzo, tsiku lina woyang’anila dela wina ku Madagascar, anapita pa malo enaake kukacititsa daunilodi pulogilamu imodzi ya mwezi na mwezi ya JW Broadcasting. Anamulipilitsa ndalama yokwana madola 16, imene iposa ndalama zimene ena amapeza pa mlungu! a

 Olo kuti pali mavuto amenewa, tsopano anthu ofika m’mamiliyoni mu Africa angaonelele mapulogilamu a pa JW Broadcasting popanda kuseŵenzetsa Intaneti. Motani?

 Kuyambila mu 2017, JW Broadcasting yakhala ikuulutsidwa kwa anthu okhala kum’mwela kwa Cipululu ca Sahara mu Africa kupitila pa chanelo ya TV. Chanelo imeneyi ni yaulele, ndipo imaulutsa mapulogilamu tsiku lililonse kwa maola 24, komanso m’zinenelo 16.

Mu 2018, abale ku Mozambique akuseting’a cipangizo pa Nyumba ya Ufumu cothandiza kuti azionelela JW Broadcasting ya pa TV

 Kuti izi zitheke, Mboni za Yehova zimalipila ndalama ku kampani youlutsa mapulogilamu a pa TV kuti iziulutsa mapulogilamu a JW Broadcasting. Makina a setilaiti amene amagwilitsidwa nchito ali na mphamvu yofika maiko 35 a kum’mwela kwa cipululu ca Sahara mu Africa. Ndalama zimene zimalipilidwa kuti mapulogilamu amenewa aulutsidwe ni madola oposa 12,000 pa mwezi. Nthawi na nthawi, gulu limapeleka ndalama zina ku kampaniyo kuti iulutse mapulogilamu ena amene akucitika pa nthawiyo. Mwa ici, anthu masauzande amakwanitsa kumvetsela misonkhano yapadela kapena mapulogilamu ena ocitika pa nthawi ya kucezela nthambi.

Mu 2018, kagulu ka atumiki a m’Dipatimenti ya Mapulani na Mamangidwe (LDC) ku Malawi kakuonelela JW Broadcasting ya pa TV

 Anthu ambili, kuphatikizapo amene si Mboni amaonelela chanelo ya JW pa nyumba zawo. Komabe, abale athu ena sangakwanitse kugula zipangizo zoseŵenzetsa kuti azionelela chanelo ya TV imeneyi panyumba. Pofuna kuwathandiza, pa Nyumba za Ufumu zoposa 3,670 anaikapo zipangizo zoonetsela mapulogilamu a pa TV a JW Broadcasting kuti abale na alongo azikaonelela kumeneko. Zipangizo zimenezo, kuphatikizapo thilansipoti yonyamulila, zimawononga ndalama yokwana madola 70 ngati pa Nyumba ya Ufumu pali kale TV kapena pulojekita. Ngati zimenezi palibe, ndiye kuti zipangizo zonse zofunikila zingawononge ndalama zokwana madola 530.

 Abale na alongo athu amayamikila kwambili kukhala na chanelo imeneyi. M’bale wina wa ku Cameroon, amene ni mkulu anati: “Pa banja pathu, chanelo imeneyi ili ngati mana mkatikati mwa cipululu.” M’bale Odebode, wa ku Nigeria, anati: “Timaonelela chanelo imeneyi monga banja katatu pa mlungu. Nthawi zonse ana anga amayembekezela mwacidwi nthawi yoonelela JW Broadcasting. Nthawi zina amapempha kuti tisinthe chanelo na kutsegula chanelo ya JW Broadcasting.” Mlongo Rose, amenenso akhala ku Nigeria, anati: “Kale n’nali kukonda kwambili kumvetsela nyuzi pa TV. Koma ndine wokondwa kuti tsopano timakonda kumvetsela chanelo ya JW Broadcasting. Kale nimati nikamvetsela nyuzi, n’nali kukhumudwa mwamsanga na zimene naona, ndipo BP inali kukwela. Koma JW Broadcasting ni yolimbikitsa ngako komanso yokhazika mtima pansi! Ndiyo chanelo ya kumtima kwanga. Chaneloyi ni dalitso lalikulu locokela kwa Yehova.”

Banja ku Malawi likuonelela vidiyo ya ana pa chanelo ya JW Broadcasting ya pa TV

 Woyang’anila dela wina ku Mozambique anakamba kuti m’dela lake, pa Nyumba za Ufumu anaikapo zipangizo zoonetsela chanelo imeneyi. Abale m’mipingo ya m’delalo amafika ku Nyumba ya Ufumu kukali ola limodzi kapena kupitilila misonkhano isanayambe, n’colinga cakuti akaonelele JW Broadcasting ya pa TV.

Mu 2018, mpingo wina ku Ethiopia unaonelela pulogilamu ya mwezi na mwezi ya JW Broadcasting popanda kuseŵenzetsa Intaneti

 Pa msonkhano wa maiko wa mu 2019, umene unacitikila ku Johannesburg, m’dziko la South Africa, chanelo imeneyi inagwilitsidwa nchito poulutsa nkhani zikulu-zikulu, kuphatikizapo zokambidwa na m’bale wa m’Bungwe Lolamulila, kuti zizimvekanso ku madela ena 9. M’bale Sphumelele, wa m’Dipatimenti ya local Broadcasting pa nthambi ya South Africa, anati: “Kale, tinali kuulutsa nkhanizi kupitila pa Intaneti. Izi zinali kufuna netiweki yamphamvu komanso ndalama zogulila mabando a Intaneti. Koma chanelo ya JW ni yochipilako komanso yodalilika.”

 Cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka mowolowa manja, tsopano abale na alongo athu ambili mu Africa angathe kuonelela JW Broadcasting pa chanelo ya TV. Tiyamikila kwambili zopeleka zimene mumapeleka poseŵenzetsa njila zosiyanasiyana zimene zipezeka pa donate.pr418.com.

a Ndalama zonse za madola zimene zachulidwa m’nkhani ino ni za ku America.