MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Cida Cophunzitsila Baibo Cosiyana Kwambili na Zina
APRIL 1, 2022
Mu January 2021, Bungwe Lolamulila linalengeza za kutulutsidwa kwa buku latsopano lophunzitsila Baibo, lochedwa Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! a Kodi munamvela bwanji mutamva cilengezoci? Matthew, amene amakhala ku Canada, anati: “N’nakondwela! Ndipo cimwemwe canga cinawonjezeka pamene n’nali kumvetsela nkhani na mavidiyo amene anafotokoza cifukwa cake bukuli linapangidwa, komanso mmene ofalitsa analiyesela. N’nali kungolakalaka kuliona na kuyamba kuliseŵenzetsa.”
Buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! lili na njila yatsopano yotsogozela maphunzilo. Koma palinso mbali zina zimene zimasiyanitsa buku latsopanoli na mabuku amene tinali kuseŵenzetsa kumbuyoku. Ngati munagwilitsapo nchito buku lopulinta lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya, mwina mutaligwila munamva m’manja mwanu kuti n’losiyana na mabuku ena. Kuti mudziŵe cifukwa cake, tiyeni tione mmene linapangidwila.
Buku Latsopano Losiyana na Ena
Mapepala otikama. N’cifukwa ciani bukuli linapangidwa na mapepala otikama? Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! lili na zithunzi zokongola zoposa 600, kuŵilikiza pafupi-fupi ka 10 ciŵelengelo ca zithunzi za m’buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse! Masamba a buku latsopanoli alinso na mbali zambili zopanda mawu kapena zithunzi. Zifukwa ziŵili zimenezi zinapangitsa kuti pakhale vuto linalake. Vuto lake n’lakuti ngati pepala n’lopepuka, zithunzi za pa tsamba zimaonekela kuseli kwa tsambalo, ngakhale kuti nthawi zina zingaoneke pang’ono. Pofuna kupewa zimenezi, abale a m’Dipatimenti Yoona za Nchito Yopulinta Mabuku ku Wallkill, mumzinda wa New York, ku America., anayesa mitundu inayi ya mapepala amene timagwilitsa nchito pali pano populinta. Komiti Yoona za Nchito Yolemba ya Bungwe Lolamulila itawaona mapepalawo, inasankha pepala lotikama losaonetsa zakuseli. Popeza kuti mtundu umenewu wa pepala suonetsa zithunzi zakuseli, ophunzila angaŵelenge buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya popanda kuceutsidwa na kuonekela kwa zithunzi zakuseli. Komabe, mtengo wa mapepala amenewa ni okwela na 16 pesenti poyelekezela na mapepala ena.
Cikuto copangidwa mosiyana. Cikuto ca buku latsopanoli n’cosiyana na zikuto za mabuku ena. Zili conco cifukwa kapepala koteteza cikuto kamene anagwilitsa nchito n’kosiyana na tumapepala tumene tumagwilitsidwa nchito nthawi zambili. Tumapepalato tumapangitsa cithunzi ca pacikuto kuoneka bwino kwambili. Tumatetezanso bukuli kuti lisaonongeke. Komabe, tumapepala twamtundu umenewu toteteza cikuto n’todula kuŵilikiza kasanu mtengo wa tumapepala twa nthawi zonse. Conco, nthambi zingapo zinathandizana kuti zigule tumapepala tolimbato pa mtengo wochipilako.
N’cifukwa ciani abale anasankha kuseŵenzetsa zinthu zodula popanga mabukuwa? M’bale wina amene amatumikila mu dipatimenti yoona za nchito yopulinta mabuku pa dziko lonse anati: “Tikhulupilila kuti bukuli lidzagwilitsidwa nchito kwambili. Conco, tifuna kuti likhale lolimba kuti lizionekabe bwino olo lagwilitsidwa nchito nthawi yaitali.” M’bale Eduardo, amene amatumikila mu Ofesi Yopulinta Mabuku pa nthambi ya ku Brazil, anati: “Ndife okondwa kwambili kuona kuti gulu la Yehova lagwilitsa nchito zipangizo zabwino kuti bukuli likhale lokongola komanso lolimba. Panthawi imodzimodziyo, gululi likuseŵenzetsa mosamala ndalama za copeleka.”
Kupulinta pa Nthawi ya Mlili wa COVID-19
Nchito yopulintha buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! inayamba mu March 2021. Iyi inali nthawi ya mlili wa COVID-19. Conco, tinakumana na zovuta zina. Popeza kuti anthu sanali kuloledwa kubwela pa Beteli, panalibe atumiki oyendela oti n’kuthandiza pa nchito yopulinta. Zinali zosathekanso kuitana abale ena kuti ayambe kutumikila pa Beteli. Pa cifukwa cimeneci, nthambi zina zopulinta mabuku zinalibe anthu okwanila ogwila nchitoyi, ndipo mafakitale ena opulintila anatsekedwa kwa kanthawi cifukwa ca malamulo a boma.
Kodi mavuto amenewa tinathana nawo bwanji? Nchito itayambanso m’mafakitale opulinta mabuku, abale na alongo a m’madipatimenti ena pa Beteli anali kuuzidwa kuti akathandize dipatimenti yopulinta kwa kanthawi. M’bale Joel, amenenso ali m’dipatimenti yoona za nchito yopulinta mabuku pa dziko lonse, anati: “Abale na alongowa anali na mtima wodzimana komanso anali okonzeka kuphunzila nchito zatsopano. Izi zinathandiza kwambili kuti nchito iyende.”
Ngakhale panali zovuta, takwanitsa kupulinta makope mamiliyoni a buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Kupulinta mabukuwa kulila zinthu zambili, monga zipangizo zopulintila, zinthu zolimbitsila zikuto, mapepala, inki, na zomatila. M’miyezi isanu yoyambilila imene tinapulinta mabukuwa, tinagwilitsa nchito ndalama zoposa madola 2.3 miliyoni a ku America pogula cabe zinthu zopulintila. Pofuna kusewenzetsa ndalama mosamala, timangopulinta ciwelengelo ca mabuku cimene cikufunikila ku mipingo pa nthawiyo.
“Buku Lopangidwa Mwaluso”
Kodi ophunzitsa Baibo na ophunzila awo amamva bwanji akamaseŵenzetsa buku latsopanoli? M’bale wina wa ku Australia, dzina lake Paul anati: “Buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya limanisangalatsa kwambili nikamaliseŵenzetsa potsogoza maphunzilo a Baibo. Bukuli linapangidwa mocititsa cidwi kwambili, ndipo linapangidwadi m’njila yolimbikitsa makambilano na wophunzila. Bukuli limafotokoza zinthu mosavuta kumva, lili na mafunso ofika pamtima, mavidiyo, zithunzi, machati, na zolinga zoti wophunzila azikwanilitse. Bukuli linapangidwa mwaluso, ndipo limanilimbikitsa kunola maluso anga akuphunzitsa.”
Wophunzila Baibo wina wa ku America anati: “Nimalikonda kwambili buku latsopanoli. Ndipo zithunzi zake zimanithandiza kumvetsa mfundo zazikulu. Mavidiyo ake amanifika pamtima, ndipo amanilimbikitsa kucitapo kanthu.” Wophunzilayu amaphunzila kaŵili pamlungu, ndipo amapezeka pa misonkhano ya mpingo mokhazikika.
Makope ofika m’mamiliyoni a buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya afunikabe kupulintidwa m’zinenelo zambili. Kufika pano, Bungwe Lolamulila lavomeleza kuti bukuli lipulintidwe m’zinenelo zokwanila 710. Ciŵelengelo cimeneci cipitilila na zinenelo 340 pa zinenelo zimene munatulutsidwa buku lakuti Zimene Baibulo Lingatiphunzitse.
Kodi ndalama zopulintila zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka zaufulu za nchito ya padziko lonse, ndipo zambili mwa ndalamazo zimapelekedwa kupitila pa donate.pr418.com. Timayamikila mzimu wanu wowoloŵa manja, umene umathandiza popanga zida zophunzitsila Baibo kuti anthu ofuna aphunzile za Yehova komanso kuti ‘akakhale na moyo kosatha.’—Salimo 22:26.
a Bukuli linatulutsidwa pa JW Broadcasting pa pulogilamu yauzimu ya msonkhano wa pacaka.