Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kufalitsa Buku Lofunika Kwambili Kuposa Onse

Kufalitsa Buku Lofunika Kwambili Kuposa Onse

JANUARY 1, 2021

 M’bale wina anati: “Nakhala nikuyembekezela zimenezi kwa zaka 19!” Kodi anali kuyembekezela ciani? Anali kuyembekezela Baibo ya Dziko Latsopano ya Malemba Acigiriki Acikhristu m’cinenelo cawo ca ci Bengali. Mofanana na m’baleyo, anthu ambili amakondwela kwambili ngati Baibo ya Dziko Latsopano yatulutsidwa m’cinenelo cawo. Koma kodi mudziŵa nchito imene imakhalapo kuti Mabaibo amenewa amasulidwe na kusindikizidwa?

 Coyamba, gulu lomasulila limakhazikitsidwa motsogoleledwa na Komiti Yoyang’anila Nchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulila. Kodi pamatenga nthawi yaitali bwanji kuti gulu lomasulila litsilize kumasulila Baibo? M’bale Nicholas Ahladis, wa m’Dipatimenti Yothandizila pa Nchito Yomasulila ku Warwick, mumzinda wa New York, anati: “Kutalika kwa nthawi yogwila nchitoyi kumadalila pa zinthu zambili, monga ciŵelengelo ca omasulila amene alipo, kuvuta kwa cinenelo cimene akumasulila, luso la anthu oŵelenga cineneloco lomvetsa cikhalidwe ca m’Baibo, komanso ngati cineneloco cimakambidwa mosiyanasiyana m’madela osiyanasiyana. Pa avaleji, zimatenga caka cimodzi mpaka zitatu kuti gulu lomasulila litsilize kumasulila cabe Malemba Acigiriki Acikhristu, ndiponso zaka zinayi kapena kupitilila kuti limasulile Baibo yonse. Ngati Baibo imene ikumasulidwa ni ya cinenelo camanja, nchitoyi imatenga zaka zambili kuposa pamenepa.”

 Si omasulila cabe amene amafunika kuti Baibo imasulidwe. Pamafunikanso gulu la oŵelenga ocokela m’madela osiyanasiyana, nthawi zina ocokela m’maiko angapo, kuti akaŵelenge zimene zamasulidwa na kuona ngati zimveka bwino. Iwo amacita zimenezo mongodzipeleka. Zokamba zawo zimathandiza omasulila kumasulila Baibo molondola, mosavuta kumva, komanso momveketsa bwino tanthauzo. Monga mmene m’bale wina wa ku South Africa amene amaphunzitsa nchito yomasulila Baibo anakambila, “omasulila amaona kuti ali na udindo waukulu kwambili kwa Yehova komanso kwa anthu amene amaŵelenga Mawu ake.”

 Nchito yomasulila ikatha, Mabaibo amapulintidwa na kukonzedwa. Kuti Baibo ipulintidwe na kukonzedwa, pamafunika zinthu 10 zoseŵenzetsa, zomwe ni: mapepala, inki, zikuto, zomatila, zikuto zapamwamba, zokongoletsela zasiliva, maliboni, zomangila mapepala, zolimbitsila, komanso zomangila zina kuti Baibo yonse ikhale yogwilana bwino. Mu 2019, tinagwilitsila nchito ndalama zokwana madola 20 miliyoni (a ku America) pogula cabe zinthu zimenezi zoseŵenzetsa popanga Mabaibo. Atumiki ogwila nchito m’mafakitale athu opulintila anaseŵenza kwa maola oposa 300,000 m’caka cimeneco kuti apange na kutumiza Mabaibo.

“Baibo ni buku lofunika kwambili limene timafalitsa”

 N’cifukwa ciani timaseŵenzetsa nthawi na ndalama zoculuka conco pa nchito zimenezi? M’bale Joel Blue wa m’Dipatimenti Yoyang’anila Nchito Yopulinta Mabuku Padziko Lonse anati: “Baibo ni buku lofunika kwambili limene timafalitsa. Conco. timafuna kuti maonekedwe ake akhale olemekeza Mulungu amene timalambila komanso uthenga umene timalalikila.”

 Kuwonjezela pa kupanga Mabaibo ozoloŵeleka, timapanganso Mabaibo a anthu amene ali na mavuto ena. Mwacitsanzo, Baibo ya Dziko Latsopano ya zilembo za akhungu imapezeka m’zinenelo 10. Baibo yathunthu imodzi ya cinenelo ca akhungu ingatenge maola 8 kuti aipange, ndipo cifukwa cakuti imapangidwa m’mavoliyamu ambili, imafuna malo osacepela mamita 2.3 osungila. Timapanganso Mabaibo apadela oseŵenzetsa akaidi m’ndende, cifukwa kumeneko amalola cabe mabuku a cikuto ca pepala.

 Baibo ya Dziko Latsopano imakhudza miyoyo ya anthu amene amaiŵelenga. Ganizilani za mpingo wa ci Kiluba ku Tombe, ku dziko la Democratic Republic of the Congo. Dela la Tombe lili pa mtunda wa makilomita oposa 1,700 kucokela ku likulu la dzikolo. Abale kumeneko anali na Baibo imodzi cabe, ndipo inali na mawu acikale a ci Kiluba. Iwo anali kubwelekana Baibo imeneyo kuti aliyense aiseŵenzetse pokonzekela mbali yake pa msonkhano. Koma kuyambila mu August 2018, aliyense mu mpingowo anakhala na Baibo ya Dziko Latsopano yathunthu komanso ya cinenelo camakono.

 Mlongo wina wokamba ci German anakamba izi ponena za Baibo ya Dziko Latsopano yokonzedwanso m’cinenelo cawo: “Sinikambanso kuti niyenela kuŵelenga Baibo. Koma nimadzifunsa kuti, ‘Ni nthawi yanji pamene ningapitilize kuiŵelenga?’” Mkaidi wina analemba kuti: “N’napatsidwa Baibo ya Dziko Latsopano, ndipo ikusintha umoyo wanga. Sin’namvetsetsepo Mawu a Mulungu ngati mmene nawamvetsetsela kucokela pamene n’nayamba kuŵelenga Baibo ya Dziko Latsopano. Nifuna kudziŵa zambili zokhudza Mboni za Yehova komanso zimene ningacite kuti nikhale mmodzi wa iwo.”

 Anthu onse amene amaŵelenga Baibo ya Dziko Latsopano amayamikila zopeleka zimene zimathandizila popanga Baibo imeneyi. Zopeleka za nchito ya padziko lonse zimenezi zimapelekedwa potsatila njila zimene zipezeka pa donate.pr418.com. Tikuyamikilani pa kuwolowa manja kwanu.