Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kumvetsela Msonkhano Wacigawo pa TV na pa Wailesi

Kumvetsela Msonkhano Wacigawo pa TV na pa Wailesi

AUGUST 1, 2021

 Msonkhano wacigawo wa 2020 unali wosaiwalika! Unali msonkhano woyamba wa padziko lonse, umene unajambulidwa na kuikidwa pa Intaneti. Komabe, ku Malawi na ku Mozambique, abale na alongo athu ambili anamvetsela msonkhanowo popanda kuseŵenzetsa intaneti. Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

 Makomiti aŵili a Bungwe Lolamulila, Komiti ya Ogwilizanitsa komanso Yophunzitsa, anapeleka cilolezo capadela, cakuti msonkhano wacigawo uulutsidwe pa TV na pa wailesi ku Malawi na ku Mozambique. N’cifukwa ciani makonzedwe apadela amenewa anali ofunikila? Dziko la Malawi ni limodzi mwa maiko amene Intaneti ni yodula kwambili, moti ni Mboni zocepa cabe zimene zimakwanitsa kuseŵenzetsa Intaneti. M’bale William Chumbi, wa m’Komiti ya Nthambi ku Malawi anati: “Mawailesi na ma TV ndiwo anali njila yokhayo yopelekela cakudya cauzimu kwa abale na alongo.” Nayenso m’bale Luka Sibeko, wa m’Komiti ya Nthambi ku Malawi, anati: “Msonkhano wacigawo ukanapanda kuulutsidwa pa TV na pa wailesi, ni abale ocepa cabe m’gawo la nthambi yathu amene akanapindula na msonkhanowu.” Ku Mozambique nakonso, ni abale ocepa cabe amene akanakwanitsa kupeza zipangizo zoonelelapo msonkhano. Nanji Intaneti ndiyo yovutilatu.

Kupanga Makonzedwe

 Kaamba ka mlili wa COVID-19, machanelo ena a TV na mawailesi anali atayamba kale kuulutsa misonkhano yampingo. a Abale athu anapitanso kumeneko kukapempha nthawi yowonjezeleka kuti aulutse msonkhano wacigawo.

 Ku Malawi, abale athu anakumana na vuto linalake. Nthawi zambili machanelo a TV na mawailesi salola makasitomala awo kuulutsa kwa nthawi yoposa ola limodzi. Iwo amada nkhawa kuti mapulogilamu atali-atali akhoza kucititsa anthu ulesi. Koma abale athu anawafotokozela kuti nchito yathu imathandiza anthu. Anawafotokozelanso kuti ngakhale pa nthawi ya lamulo la boma la kusacoka pa nyumba, timayesetsa kuuza anthu uthenga wabwino wa m’Baibo wotonthoza, umene ungathandize anthu kukhala nzika zabwino, komanso kukhala na mabanja acimwemwe. Atamvela izi, akulu-akulu a machanelowo anamva pempho la abale lakuti awaonjezele nthawi youlutsa misonkhano.

 Ku Malawi, msonkhano wacigawo unaulutsidwa pa chanelo imodzi ya TV komanso pa chanelo imodzi ya wailesi. Machanelo onsewo amamveka kulikonse m’dzikolo, ndipo anthu ofika m’mamiliyoni angamvetsele machanelowo. Ku Mozambique, msonkhano wacigawo unaulutsidwa pa chanelo imodzi ya TV na pa nyumba za mphepo 85.

 M’maiko aŵiliwa, gulu la Mulungu linagwilitsila nchito ndalama zokwana madola 28,227 b poulutsa msonkhano wacigawo pa TV, komanso ndalama pafupifupi madola 20,000 poulutsa pa wailesi. Mitengo youlutsila msonkhano wacigawo pa wailesi inali kuyambila madola 15 ngati chanelo ni yaing’ono mpaka kukafika madola 2,777 ngati chanelo ni yaikulu, yomveka kulikonse m’dzikolo.

 Abale athu anayesetsa kuseŵenzetsa bwino ndalama za copeleka. Mwacitsanzo, ku Malawi, iwo anapempha kuti awacotseleko mtengo, ndipo ulendo wina anawacotselako 30 pelesenti. Zimenezi zinapulumutsa madola okwana 1,711. Ku Mozambique, machanelo ena analola kucepetsako mtengo cifukwa ca mbili yathu yabwino ya kuona mtima komanso kulipila pa nthawi yake.

Mawu Oyamikila

 Abale athu anayamikila kwambili kutamba msonkhano wacigawo pa TV kapena kuumvetsela pa wailesi m’dziko lawo. M’bale Patrick, amene ni mkulu ku Malawi, anati: “Tiyamikila abale a m’Bungwe Lolamulila cifukwa cotiganizila mwapadela pa nthawi ya mliliwu.” Nayenso m’bale Isaac, wa ku Malawi, anati: “Tilibe zipangizo zina. Conco tinayamikila kwambili kaamba ka makonzedwe apadela a gulu la Yehova akuti timvetsele msonkhano wacigawo pa wailesi. Makonzedwe amenewa anathandiza kuti banja langa lonse lipindule na msonkhano wacigawo. Tinaona kuti umenewu ni umboni wakuti Yehova amawakonda anthu ake.”

 Msonkhano wacigawo wa 2020 unali woyamba kwa wofalitsa wina ku Mozambique kuumvetsela. Iye anati: “Makonzedwe oonelela msonkhano wacigawo pa TV ananikumbutsa kuti Yehova ni Mulungu wamphamvuzonse. Mlili sunamulepheletse kutipatsa cakudya cauzimu. Iye anacita kutibweletsela cakudyaco m’nyumba yathu. N’naona umboni wa cikondi cimene anthu a Yehova ali naco pakati pawo. Sinikayika kuti ici ndico cipembedzo coona.”

 M’bale wina dzina lake Wyson, amene ni mkulu mumpingo anati: “Niyamikila kapolo wokhulupilika potisamalila pa nthawi ino ya mlili. Makonzedwe amenewa oulutsa msonkhano wacigawo pa wailesi na pa TV athandiza ambili a ife amene ndife osauka komanso amene timakhala m’maiko osauka. Takhala na mwayi womvetsela pulogilamu yauzimu imeneyi na kupindula nayo.”

 Makomiti aŵili a Bungwe Lolamulila, Komiti ya Ogwilizanitsa komanso Yophunzitsa apanganso makonzedwe apadela akuti msonkhano wacigawo wa 2021 uulutsidwe pa TV komanso pa wailesi m’madela ena. Kodi ndalama zoulutsila msonkhano wacigawo pa TV na pa wailesi zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka za nchito ya padziko lonse. Zambili mwa zopeleka zimenezi zimapelekedwa kupitila pa copezeka.pr418.com. Timayamikila kwambili zopeleka zanu zimene mumapeleka mowolowa manja.

a Kuciyambi kwa 2020, Komiti ya Ogwilizanitsa inavomeleza kuti misonkhano ya mpingo iziulutsidwa pa TV na pa wailesi m’madela ena panthawi ya mlili wa COVID-19. Makonzedwe amenewa athandiza abale na alongo amene sangakwanitse kusonkhana na mipingo yawo kapena kumvetsela misonkhano ya pa JW Stream, cifukwa amakhala m’madela kumene Intaneti komanso netiweki ya foni n’zovuta, kapena tokotaimu na mabando a intaneti n’zodula. Komabe, makonzedwe amenewa sanapangidwile abale na alongo amene angathe kulumikiza ku misonkhano ya mpingo wawo.

b Ndalama zonse za madola zimene zachulidwa m’nkhani ino ni za ku America.