Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kupeleka Thandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mlili wa Padziko Lonse

Kupeleka Thandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mlili wa Padziko Lonse

JULY 1, 2021

 Mu March 2020, pamene bungwe la World Health Organization linalengeza kuti COVID-19 ni mlili wa padziko lonse, ambili sanali kuyembekezela kuti mliliwu udzapitiliza kuvutitsa anthu padziko lonse kwa nthawi yopitilila caka cimodzi. Anthu mamiliyoni ambili, kuphatikizapo a Mboni za Yehova, adwalapo matendawa, ataikilidwa okondedwa awo, komanso akumana na mavuto a zacuma cifukwa ca mliliwu. Kodi Mboni za Yehova zinapanga makonzedwe otani opelekela thandizo? Nanga thandizolo linapelekedwa bwanji?

Kupeleka Thandizo kwa Ofunikila Thandizo

 Motsogoleledwa na Komiti ya Ogwilizanitsa ya Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova, Makomiti Opeleka Thandizo Pakagwa Tsoka (DRC) oposa 950 anakhazikitsidwa padziko lonse kuti apeleke thandizo pa nthawi ya mlili wa COVID-19. Nthawi zina makomitiwa amapanga makonzedwe akuti abale azithandizana m’madela awo. Ndipo nthawi zina, Mboni zimalandila thandizo locokela ku boma. Makomitiwa amalinganizanso nchito yaikulu yopeleka thandizo.

 Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika ku Paraguay. Nyuzipepala ina inafotokoza kuti cifukwa ca mavuto a zacuma obwela kaamba ka mliliwu, “anthu ambili ku Paraguay akuvutika na njala.” Pa nthawiyo, komiti yopeleka thandizo ku Paraguay inali itayamba kale kupeleka mabokosi a zakudya, zoyeletsela, na zinthu zina zofunikila, zoti banja la anthu anayi lingakwanitse kuseŵenzetsa kwa milungu iŵili. Zinthu zimene zinali m’bokosi iliyonse zinali za ndalama zokwana madola pafupifupi 30 a ku America.

 Kodi ogwila nchito yopeleka thandizo amenewa amadziteteza bwanji komanso amateteza bwanji anthu ena ku mliliwu COVID-19? Amavala mamaski ndiponso amakhala motalikilana. Amaonetsetsanso kuti makampani amene amagulako zakudya, amasamalila bwino zakudyazo ndipo amayesetsa kupewa kufalitsa matenda. Izi ziphatikizapo kuonetsetsa kuti onse amene amagwila mabokosiwo amavala zodzitetezela ku matenda, amayeletsa mamotoka awo na kuwafafaza mankhwala opha tuzilombo, komanso amasunga mabokosiwo pa malo amene athilapo mankhwala opha tuzilombo. Ndipo cina, amene amapeleka mabokosiwo kwa abale, amakhala nawo motalikilana.

Kuseŵenzetsa Zopeleka Mwanzelu

 Pofika mu January 2021, Komiti ya Ogwilizanitsa inali itavomeleza kuseŵenzetsa ndalama zoposa madola 25 miliyoni a ku America, pothandiza ovutika cifukwa ca mlili wa COVID-19. Maofesi a nthambi komanso Makomiti Othandiza Pakagwa Tsoka, amaseŵenzetsa mosamala ndalama za copeleka zimenezi, ndipo amayesetsa kugula zinthu pa mtengo wabwino. Mwacitsanzo, ku dziko la Chile, abale ogwila nchito yopeleka thandizo anafuna kugula nyemba zokwana makilogilamu 750. Koma panthawiyo mtengo wa nyemba unali utakwela kuŵilikiza kaŵili poyelekezela na mtengo wa mwezi wapita! Abalewo anangogwilizana na wogulitsa kuti agule nyemba pa mtengo wokwelawo. Koma patangopita maola aŵili, wogulitsayo anauza abalewo kuti munthu wina amene anagula nyemba, wabweza nyemba zake. Conco, mmalo mowagulitsa nyembazo pa mtengo wodula umene anapangana, wogulitsayo anawagulitsa nyemba zimene zinabwezedwazo pa mtengo wotsika wa mwezi wapita!

 Koma abalewo atapita kuti akatenge nyembazo, wogulitsayo anafuna kusintha maganizo. Anawanena kuti amapeleka zakudya mokondela ngati mmene mabungwe ena anali kucitila. Atapeleka pemphelo lacidule lamumtima, mmodzi wa abaleyo anauza wogulitsayo kuti mpingo uliwonse unali utafufuzidwa kale kuti aone amene anali kufunikiladi thandizo. Abalewo anafotokozanso kuti cifukwa ca kusiyana kwa zikhalidwe za anthu a kumeneko, m’bokosi iliyonse yopelekela thandizo adzaikamo zinthu zoyenelela ku banja limene lidzalandila bokosiyo. Pamapeto pake anatsimikizila wogulitsayo kuti ndalama zonse zimene zimapelekedwa kwa Mboni za Yehova komanso thandizo limene amalandila, zimapelekedwa modzifunila. Iye anacita cidwi kwambili na zimenezi, moti anavomela kuwagulitsa nyembazo pa mtengo wochipawo, komanso anacita copeleka ca nyemba zokwana makilogilamu 400 pamene abalewo anapitanso kukagula nyemba kwa iye.

“Umboni wa Cikondi Ceniceni”

 Lusu, mayi wokalamba komanso wamasiye wa ku Liberia, ali m’banja la anthu 6. Tsiku lina m’maŵa pamene anali kudya cakudya na kukambilana lemba la tsiku, mdzukulu wake wa zaka 7 anazindikila kuti panyumbapo cakudya catha. Mdzukuluyo anafunsa kuti, “Kodi tizidya ciani?” Lusu anam’tsimikizila kuti anali ataipemphelela kale nkhaniyo, ndipo anali na cikhulupililo cakuti Yehova adzawathandiza kupeza cakudya. Tsiku lomwelo masana, Lusu analandila foni yocokela kwa akulu yomuitana kuti akatenge cakudya. Iye anati: “Mdzukulu wanga amakamba kuti tsopano akudziŵa kuti Yehova amamva na kuyankha mapemphelo cifukwa anayankha pemphelo langa.”

Ana ku Democratic Republic of Congo anajambula zithunzi zoyamikila abale cifukwa ca thandizo la cakudya

 Mayi wina ku Democratic Republic of Congo amakhala pa nyumba yapafupi na banja lina la Mboni. Ataona kuti banja la Mbonilo lalandila cakudya kucokela kwa Mboni zinzawo, anati, “Mliliwu ukatha, tidzakhala a Mboni za Yehova cifukwa iwo akusamalila abale na alongo awo pa nthawi yovutayi.” Mwamuna wake anamufunsa kuti, “Kodi udzakhala wa Mboni za Yehova cabe cifukwa ca thumba la mpunga?” Iye anayankha kuti, “Ayi, koma cifukwa cakuti thumba la mpunga limeneli ni umboni wa cikondi ceniceni.”

 Mboni za Yehova zakhala zikupeleka thandizo mwamsanga kwa abale na alongo ofunikila thandizo cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka moolowa manja. Zikomo kwambili cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka poseŵenzetsa njila zofotokozedwa pa donate.pr418.com.