Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kupeleka Thandizo kwa Anthu Okhudzidwa na Matsoka

Kupeleka Thandizo kwa Anthu Okhudzidwa na Matsoka

FEBRUARY 1, 2021

 Caka ca 2020 cinali ca matsoka ambili a zacilengedwe, komanso cinali caka cimene mlili wa COVID-19 unayamba padziko lonse. Kodi Mboni za Yehova zinawathandiza bwanji anthu amene anakhudzidwa?

 M’caka cautumiki ca 2020, a Komiti ya Agwilizanitsi ya Bungwe Lolamulila inavomeleza kuti ndalama zokwana madola 28 miliyoni b ziseŵenzetsedwe pa nchito yopeleka thandizo pakacitika matsoka. Izi zinathandiza kuti anthu okhudzidwa na matsoka oposa 200 alandile thandizo. Ena mwa matsokawo anali mlili wa COVID-19, mphepo zoopsa za mkuntho, kusefukila kwa madzi mu Africa, njala ku Venezuela, ndiponso cilala ku Zimbabwe. Zopelekazi zinathandizila kugula zakudya, madzi, zovala, na mankhwala. Zinathandizilanso kupezela malo okhala anthu okhudzidwa, komanso zinthu zina zofunikila poyeletsa, pokonza zinthu, ndiponso pokonza nyumba zowonongeka. Onankoni zina mwa zitsanzo pa nchito yopeleka thandizo.

 Mlili wa COVID-19. Padziko lonse, mliliwu wakhudza abale na alongo athu mwakuthupi, mwamaganizo, ndiponso m’zacuma. Pofuna kuwathandiza, padziko lonse panakhazikitsidwa makomiti oposa 800 opeleka thandizo kwa anthu okhudzidwa na matsoka. Abale a m’makomiti amenewa anapenda mosamala zimene abale athu anali kufunikila, ndipo mwamsanga anapeleka malipoti, amene anathandiza Komiti ya Agwilizanitsi kudziŵa mmene angapelekele thandizo.

 M’caka conse cautumiki ca 2020, makomiti opeleka thandizo kwa anthu amene akhudzidwa na matsoka anathandiza anthu ambili kupeza cakudya, madzi, zinthu zowathandiza kukhala aukhondo, komanso cithandizo camankhwala. Kumadela ena, makomiti amenewa anagwililanso nchito pamodzi na akulu kuti athandize abale kulandila thandizo limene boma limapeleka.

 Anthu amene si Mboni amaona nchito yopeleka thandizo imene timacita. Mwacitsanzo, mkulu woyang’anila boma la Nakonde m’dziko la Zambia, dzina lake Field Simwinga, anauza abale athu kuti: “Tikuyamikilani kwambili cifukwa copeleka thandizo lofunikila panthawi yake ku mabanja okhudzidwa.”

 Njala ku Angola. Cifukwa ca mlili wa COVID-19, cakudya cinacepa ku Angola ndipo cinadula kwambili. Zinali zovuta ngako kuti abale na alongo athu ambili agule cakudya.

Makatoni a zakudya anatumizidwa kucoka ku Brazil kupita ku Angola

 Ofesi ya nthambi ya Brazil inapemphedwa kuthandiza mwa kutumiza zakudya kwa abale athu ku Angola. Pofuna kuseŵenzetsa bwino ndalama za gulu, abale anafufuza njila yabwino imene angaseŵenzetse pogula na kutumiza zakudya, ndipo anagula zakudyazo mwacipiku. Conco, kugula na kutumiza katoni imodzi ya zakudya, kunatenga ndalama zokwana madola 22 cabe pa avaleji, ngakhale kuti m’katoni imodzi munali zakudya zokwana makilogilamu pafupifupi 20, zakudya monga mpunga, binzi, na saladi. Pofika pano, makatoni a zakudya okwana 33,544 anatumizidwa, kutanthauza zakudya zolemela mathani 654. Zakudya zonsezi kuphatikizapo zimene zinagulidwa m’dzikolo, zinathandiza anthu oposa 50,000.

 Kodi abale athu amamvela bwanji akalandila thandizo limeneli? Alexandre amene amakhala kudela lina lakutali m’dziko la Angola anati: “Niona kuti cimeneci n’cizikindikilo cakuti Yehova amanikonda komanso kuti sinili nekha. Gulu la Yehova limaniŵelengela!” Mariza, mayi amene amalela yekha ana anati: “Yehova anamva kulila kwanga. Nimamuyamikila kwambili kuphatikizapo gulu lake!”

Abale a ku Angola akuyamikila pa thandizo la cakudya limene alandila

 Kupeleka Thandizo pa Cilala ku Zimbabwe. M’caka cautumiki ca 2020, ku Zimbabwe kunali cilala coopsa cimene cinapangitsa kuti anthu mamiliyoni akhale pa ciopsezo ca kufa na njala. Mboni za Yehova masauzande ku Zimbabwe zinalibe cakudya cokwanila.

 Makomiti asanu opeleka thandizo anakhazikitsidwa kuti athandize popeleka cakudya kwa abale athu. Ofalitsa mahandiledi anathandiza mwa kulonga zakudyazo, kuzikwezeka pa mamoto, kapena kubweleketsa mamotoka awo. c M’caka cautumiki ca 2020, ndalama zokwana madola 691,561 zinagwilitsidwa nchito pogula cakudya cimene cinathandiza anthu oposa 22,700!

Abale ku Zimbabwe alandila thandizo la cakudya (mlili usanayambe)

 Nthawi zina, abale anali kulandila cakudya panthawi imene cakudya cawo cathelatu. Cakudya cikafika, abale athu anali kutamanda Yehova. Ena anayamba ngakhale kuimba nyimbo za Ufumu.

 Kudela lina, azimayi aŵili amasiye amene ni Mboni, anapezeka ku msonkhano wa kudela lakwawo wokambilana za kulandila thandizo la cakudya limene bungwe lina linali kufuna kubweletsa. Komabe, pamsonkhanowo panaculuka zandale. Conco alongowo anaganiza zokana kucitako zimene zinafotokozedwa kuti munthu alandileko cakudyaco. Pamene anali kucoka pamsonkhanowo, ananyozedwa na kuuzidwa kuti, “Musabweleko kwathu kukapempha cakudya!” Koma patangopita mawiki aŵili, abale athu anafika kudelalo ndipo anapeleka thandizo la cakudya kwa alongo athu, bungwelo lisanafike kukapeleka thandizo.

“Yehova sanawagwilitsepo mwala atumiki ake,” anatelo mlongo Prisca

 Nchito yopeleka thandizo ku Zimbabwe yapangitsa kuti umboni wabwino upelekedwe. Mwacitsanzo, tiyeni tione citsanzo ca mlongo Prisca, amene akhala m’mudzi wina waung’ono. Olo kuti mlongo Prisca anali kukumana na mavuto ambili cifukwa ca cilala, iye anapatulabe tsiku la Citatu na la Cisanu kuti azipita mu ulaliki ngakhale m’nthawi yolima. Anthu a m’mudzi wake anali kumunyodola amvekele: “Mudzaphetsa banja lanu na njala cifukwa cogwila nchito yolalikila.” Mlongo Prisca anali kuwayankha kuti: “Yehova sanawagwilitsepo mwala atumiki ake.” Posapita nthawi, mlongoyu analandila thandizo la cakudya cocokela ku gulu lathu. Izi zinacititsa cidwi ena mwa anansi ake, moti anauza mlongo Prisca kuti: “Mulungu sanakugwilitseni mwala. Conco tifuna tidziŵe zambili za iye.” Palipano anansi ake okwana 7 amamvetsela ku misonkhano ya mpingo imene imakhalako pa wailesi.

 Pamene tikuyandikila kwambili mapeto, tidzapitilizabe kukumana na matsoka a zacilengedwe. (Mateyu 24:3, 7) Timaziyamikila kwambili zopeleka zanu zimene mumapeleka poseŵenzetsa njila zosiyana-siyana zopezeka pa donate.pr418.com. Tidzapitiliza kuziseŵenzetsa bwino popeleka thandizo loyenelela kwa anthu amene akuvutika.

a Caka cautumiki ca 2020 cinayamba m’mwezi wa September 2019 mpaka August 2020.

b Ndalama zamadola zimene zachulidwa m’nkhani ino ni madola a ku America.

c Cifukwa ca ziletso zokhudzana na mlili wa COVID-19, abale athu anafunika kutenga zilolezo kuti akapeleke zakudya. Analinso osamala kwambili kuti asakhale pa ciopsezo cotenga kalombo koyambitsa matenda amenewa.