Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kuteteza Ufulu wa Kulambila Pakati pa Anthu Otsatila Cikhalidwe ca Makolo

Kuteteza Ufulu wa Kulambila Pakati pa Anthu Otsatila Cikhalidwe ca Makolo

MAY 1, 2021

 Ku Latin America kuli anthu ofika m’ma 100 miliyoni, ndipo kulinso anthu mamiliyoni amene amakamba zinenelo za makolo awo akale na kutsatila cikhalidwe cawo. Mwa anthu amenewo, pali abale na alongo athu ambili amene amalemekeza cikhalidwe cawo. Pofuna kuthandiza anthu kuphunzila coonadi ca m’Baibo, abale athuwo amamasulila na kufalitsa mabuku a Mboni za Yehova m’zinenelo zoposa 130 za ku Latin America. a Ngakhale n’telo, ena a iwo amatsutsidwa cifukwa cosankha kutumikila Yehova na kukana kutengako mbali m’miyambo yosagwilizana na Malemba, imene ni yofala m’madela awo. Kodi zopeleka zanu zagwilitsidwa nchito motani pothandiza abale athu amenewa?

Anathandizidwa Kuti Abwelele Kwawo

 Ku Mexico, abale na alongo athu a ku Huichol, ku mapili a m’cigawo ca Jalisco, anakana mwaulemu kutengako mbali pa miyambo yacipembedzo yotsutsana na cikumbumtima cawo. b Koma izi zinakhumudwitsa ena m’delalo. Pa December 4, 2017, gulu laciwawa linaukila Mboni za Yehova pamodzi na anthu ena amene anali nawo. Gulu laciwawalo linathamangitsa Mboni m’delalo, linawononga katundu wawo, na kuwopseza kuti aliyense amene adzabwelela m’delalo adzamupha.

 Mboni za m’matauni apafupi zinawasamalila abale na alongo athuwo. Koma kodi n’ciani cikanathandiza kuti abwelelenso kwawo? M’bale wina dzina lake Agustin anati: “Tinalibe ndalama zokwanila zogulila loya, ndipo sitinadziŵe kuti tingapite kwa ndani kukafunsilako malangizo pa nkhani zamalamulo.”

 Popeza ufulu wa kulambila wa abale athu unapondelezedwa, ofesi ya nthambi ya ku Central America inacitapo kanthu mwamsanga. Coyamba, anapempha akulu-akulu a boma a m’delalo kuti afufuze za nkhaniyo. Kenako analandila cilolezo cocokela ku Komiti ya Agwilizanitsi ya Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova, kuti agwilile nchito pamodzi na Dipatimenti ya Zamalamulo ku likulu lathu, na kupeleka mlanduwo kukhoti m’malo mwa abale na alongo athu a ku Huichol. Pamapeto pake, mlanduwo unakafika ku Khoti Yaikulu Kwambili ya m’dzikolo—dziko la Mexico.

 Maloya ocokela m’maiko osiyana-siyana anakonzekela mfundo zomveka bwino zoti akakambe. Iwo anakamba kuti popeza anthu ena amafunika kulemekeza miyambo ya anthu otsatila cikhalidwe ca makolo, nawonso anthu otsatila cikhalidwe ca makolo ayenela kulemekeza na kuteteza ufulu wa anthu awo onse. Zili conco cifukwa anthu onse ali na ufulu, mosasamala kanthu za kumene amakhala.

 Pa July 8, 2020, Khoti Yaikulu Kwambili ku Mexico inagamula mlanduwo mokomela Mboni za Yehova. Khotiyo inalamula kuti onse amene anathamangitsidwa awalole kubwelela kwawo. Pofotokoza ciyamikilo cimene iye na anthu ena ali naco, m’bale Agustín, amene tamuchula poyamba paja anati: “Tiyamikila kwambili ndipo tili na cimwemwe cifukwa ca zimene abale aticitila. Cikanakhala kuti sanatithandize, palibe cimene tikanacita.”

‘Zazikulu kwa Anthu Ocepa’

 Ku mudzi wa San Juan de Ilumán umene uli ku Otavalo Valley m’dziko la Ecuador, kumakhala anthu ambili otsatila cikhalidwe ca makolo akale. Kumenekonso, abale athu anakumana na citsutso. Mu 2014, pambuyo potenga zilolezo zonse zofunikila, abalewo anayamba kumanga Nyumba ya Ufumu. Koma wansembe wina anatsogolela anthu aciwawa oposa 100 na kupita kukaletsa abale nchito yomangayo. Kenako anthu a m’delalo analamula Mboni za Yehova kuti zileke kusonkhana.

 A m’dipatimenti ya zamalamulo pa ofesi ya nthambi ku Ecuador, na a m’dipatimenti ya zamalamulo ya ku likulu lathu, anagwilila nchito pamodzi kuti ateteze ufulu wa abale athu wa kulambila umene unali kupondelezedwa. Abale athu anapeleka nkhaniyo kukhoti. Izi zinapangitsa kuti anthu m’delalo aleke kutsutsa a Mboni za Yehova, moti anawalola kuyambanso kucita misonkhano yawo na kutsiliza kumanga Nyumba yawo ya Ufumu. Koma pofuna kuti abale athu asakalandidwenso ufulu wa kulambila m’tsogolo, maloya oimila gulu lathu anapempha makhoti aakulu kuti apeleke cigamulo pa nkhani yofunika kwambili yakuti: Kodi anthu otsatila cikhalidwe ca makolo awo akale ayenela kulemekeza mfundo zokhudza ufulu wa anthu zokhazikitsidwa na maiko padziko lonse?

 Pa July 16, 2020, khoti yaikulu kwambili ku Ecuador inayamba kuweluza mlanduwo. Abale a ku Ecuador amene ni maloya anaimilako mpingo. Kuwonjezela apo, abale anayi amene ni maloya odziŵa za malamulo a padziko lonse anakambako pa mlandu umenewo. Kaamba ka ziletso zobwela cifukwa ca mlili wa COVID-19, abalewo anakambila pa vidiyo-komfalensi kucokela m’maiko osiyana-siyana. Aka n’koyamba kuti khoti ilole gulu la maloya oimilako Mboni za Yehova padziko lonse kukamba mbali yawo pa mlandu m’khoti mwanjila imeneyi. c Gululo linachula za akatswili a zamalamulo padziko lonse, potsimikizila kuti anthu otsatila cikhalidwe ca makolo akale, sayenela kulandidwa ufulu wobadwa nawo cifukwa cakuti ali m’gulu la anthu otsatila cikhalidwe ca makolo.

Kupitila pa vidiyo-komfalensi, gulu la maloya ocokela m’maiko osiyana-siyana linateteza ufulu wa abale athu

 Abale athu okhala ku Otavalo Valley akuyembekezela mwacidwi kumva cigamulo ca khoti pankhaniyi. Koma palipano, iwo ni oyamikila kwambili cifukwa ca thandizo limene analandila. M’bale César, amene ni mkulu mumpingo wa Ilumán Quichua, anati: “Yehova yekha, kupitila mwa gulu lake, ndiye angacite zinthu zazikulu ngati zimenezi kwa anthu ocepa.”

 aloya onse amene anathandiza pa mlanduwu ni a Mboni za Yehova, ndipo ni okondwa kuseŵenzetsa cidziŵitso cawo pa zamalamulo popanda malipilo alionse. Ngakhale n’conco, kupeleka milandu imeneyi ku khoti, kuikonzekela, na kuikamba zimafuna nthawi na ndalama. Maloya athu na abale ena anathela nthawi yokwana maola oposa 380 pokonzekela zokakamba pa milanduyi, komanso maola ena 240 pomasulila madokyumenti oseŵenzetsa pa mlandu wa ku Mexico. Maloya pafupifupi 40 ocokela m’maiko osiyana-siyana padziko lonse, anathela maola mahandiledi pa mlandu wa ku Ecuador. Kodi ndalama zoseŵenzetsa poteteza ufulu wa abale athu zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka zimene mumapeleka poseŵenzetsa njila zosiyana-siyana zochulidwa pa donate.pr418.com. Zikomo kwambili cifukwa ca kudzipeleka kwanu.

a Mboni za Yehova zimamasulilanso mabuku na zofalitsa zina m’zinenelo zambili za ku Latin America, komanso m’zinenelo zina zamanja zokambidwa cabe kumeneko.

b Anthu a ci Huichol amachedwanso a Wixáritari, ndipo cinenelo cawo nthawi zambili cimachedwa ci Wixárika.

c Mlanduwo sunali kukhudza gulu lathu la padziko lonse. Ngakhale n’conco, oweluza anawalola abale athu kuonekela m’khoti monga amene amati amicus curiae, kutanthauza “bwenzi la khoti.”