MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Kuwonjezela Ukhondo pa Nyumba za Ufumu Kuti Osonkhana Azikhala Otetezeka m’Nthawi ya COVID-19
OCTOBER 1, 2022
“Bungwe Lolamulila lagamula kuti ngati boma la kwanuko sililetsa, mipingo yonse idzayambilanso kucita msonkhano wapakati pamlungu na msonkhano wa kumapeto kwa mlungu wa pamasom’pamaso kuyambila mlungu wa April 1.” Cilengezo cimeneci comwe cinaikidwa pa jw.org kuciyambi kwa mwezi wa March 2022, cinasangalatsa kwambili Mboni za Yehova padziko lonse. Koma mlili wa COVID-19 unali usanathe. a Kodi ni zinthu ziti zimene zinafunika kukonzedwa kapena kugulidwa kuti matendawa asayambukile anthu obwela kudzasonkhana? Pambuyo pa zaka ziŵili osasonkhana pamasom’pamaso, kodi Nyumba zathu za Ufumu zikanakhalabe malo abwino kusonkhanamo?
Miyezi yambili kumbuyoko, abale athu anali atayamba kale kukonzekela kuyambilanso kusonkhana pa Nyumba za Ufumu.
Zofunika Kukonza Zosiyana, Njila Zokonzela Zosiyananso
Patangopita mwezi umodzi kucokela pamene tinaleka kusonkhana pamasom’pamaso mu 2020, Dipatimenti Yoona za Mapulani na Mamangidwe Padziko Lonse (WDC), ku Warwick, mu mzinda wa New York, inayamba kuunika mmene mlili wa COVID-19 udzakhudzile mmene timagwilitsila nchito Nyumba za Ufumu. Inafufuzanso zofunika kucita kuti anthu azikhala otetezeka pa malo athu a misonkhano.
Nthawi zambili, zimene zinali kufunika ku dela lina, zinali zosiyana na zimene zinali kufunika kumalo ena. M’bale Matthew De Sanctis, wa m’dipatimenti ya WDC anati: “M’maiko ena cosowa cimodzi ni malo osambilapo m’manja. Ngati Nyumba za Ufumu zilibe madzi a kumpopi, madzi amacita kugulidwa kapena kukatapidwa ku mtsinje kapena pacitsime. M’maiko ena, maboma anasinthako zofunika zokhudza kaikidwe ka zozizilitsa m’nyumba, motulukila mphepo, na zikwangani zokhudza umoyo na ukhondo.”
Kodi abale athu anathana nawo bwanji mavuto amenewo? Malinga na zimene m’bale Mathew ananena, abalewo anaona kuti pa Nyumba za Ufumu zambili, “zinthu zosavuta komanso zochipa zimaseŵenza bwino kwambili.”. Mwacitsanzo, m’dziko la Papua New Guinea, malo osambilapo m’manja anakonzedwa mwa kuika mabekete apulasitiki okwana malita 20 okhala na potulukila madzi. Conco, pa Nyumba ya Ufumu iliyonse ya kumudzi, abale athu anasewenzetsa cabe ndalama zokwana madola 40 a ku America pokonza malo osambila m’manja. Ndipo mu Africa, mathanki abwino osambila m’manja opitilila 6,000 anagulidwa ku kampani inayake ya ku Asia kuti azigwilitsidwa nchito pa Nyumba za Ufumu.
Zokonza zina zinaphatikizapo kuika kapena kusinthako mafani na motulukila mphepo, kuti m’Nyumba ya Ufumu muzikhala mpweya wabwino komanso wokwanila. Mipingo yambili inagula zogwilila mamaikolofoni zitalizitali kuti asamacite kupatsilana m’manja mamaikolofoni. Panakonzedwanso kuti mbali zimene zimagwilidwa kaŵili-kaŵili monga zogwilila zitseko na mapompi, zisamagwilidwe kaŵili-kaŵili komanso zizipakidwa mankhwala opha tuzilombo popewa kufalitsa matenda. Kuwonjezela apo, m’mipingo ina, m’zimbudzi anaikamo mapompi amene amatseguka okha manja akafika pafupi. Ku dziko la Chile, kuika zofunika pa Nyumba ya Ufumu iliyonse kunatenga ndalama zokwanila madola 1,400 a ku America.
Colinga ca abale cinali kukonza Nyumba za Ufumu kuti anthu azikhala otetezeka pa misonkhano. Koma panthawi imodzimodziyo anayesetsa kusewenzetsa mosamala ndalama za copeleka. Mwacitsanzo, m’maiko ena abale anasewenzetsa mwayi umene maboma anapeleka wogula matanki osambila m’manja na zogwilila mamaikolofoni zitali-zitali popanda kulipila msonkho. Maofesi a nthambi naonso anasewenzela pamodzi pogula zinthu mu unyinji kusiyana na nthawi zonse pofuna kuti asaononge ndalama zambili. Maofesi a nthambi na Dipatimenti Yogula Zinthu Padziko Lonse nthawi zambili anali kugula zinthu mwacindunji kwa ozipanga. Izi zinacititsa kuti mtengo wogulila zinthuzo ucepeko ndiponso kuti zifike mwamsanga.
“Nimamva Kuti Ndine Wotetezeka”
Kukonza Nyumba za Ufumu kumeneku kwateteza anthu amene anayamba kupezeka pa misonkhano pamasom’pamaso na kuwathandiza kumva kuti ni otetezeka. Mwacitsanzo, mlongo Dulcine wa ku Peru ananena kuti anali na “mantha pang’ono” atamva kuti tidzayambanso kusonkhana ku Nyumba ya Ufumu. Iye anati: “N’nadwalapo COVID-19 patangopita nthawi yocepa kucokela pamene mliliwu unayamba.” Anapitiliza kuti: “Conco nitamva kuti tidzayambanso kusonkhana ku Nyumba ya Ufumu, n’nada nkhawa kuti mwina matendawa anganiyambukilenso. Koma n’tafika pa Nyumba ya Ufumu, n’naona kuti akulu anakonza zinthu zambili kuti tikhale otetezeka. Anakonza malo osambilapo m’manja, zogwilila maikolofoni zitalizitali, komanso anali kupaka mankhwala opha tizilomba msonkhano ulionse usanayambe na pambuyo pake. Cifukwa ca zonsezi nimamva kuti ndine wotetezeka.” b
Mlongo Sara amene akhala m’Zambia, anakumana na vuto losiyana. Iye anati: “Mwamuna wanga anamwalila na COVID-19 miyezi ingapo yapitayo. N’nada nkhawa kuti nidzamvela bwanji n’kadzapezeka pa msonkhano wa pamasom’pamaso kwa nthawi yoyamba popanda iye.” Kodi mlongoyu akumva bwanji tsopano? Iye anati: “Kusonkhana pamasom’pamaso kwanithandiza kuona kuti Yehova ali nafe m’masiku otsiliza ano. Kuposa kale lonse, tsopano nimaona kuti nimalimbikitsidwa, nimakondedwa na kuthandizidwa kwambili na akulu komanso abale na alongo ena onse.”
Olambila anzathu okondedwa padziko lonse amayamikila kuti ayambilanso kusonkhana ku Nyumba za Ufumu. Zikomo kwambili cifukwa ca zopeleka zanu zimene nthawi zambili munacitila pa intaneti pa donate.pr418.com. Zopeleka zimenezi zathandiza kuti malo a kulambila koona akhale otetezeka komanso abwino kusonkhanamo.