Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Maofesi Omasulila Amene Amathandiza Anthu Mamiliyoni

Maofesi Omasulila Amene Amathandiza Anthu Mamiliyoni

MARCH 1, 2021

 Kupitilila 60 pelesenti ya atumiki a nthawi zonse amene amagwila nchito yomasulila, amaseŵenzela ku maofesi omasulila (kapena kuti ma RTO) osati m’maofesi a nthambi. Kodi makonzedwe amenewa ali na ubwino wotani? Kodi omasulila amafunikila zipangizo zotani kuti azigwila bwino nchito yawo pa RTO? Nanga malo omangila ofesi yomasulila amathandiza bwanji kuti omasulila azigwila nchito yawo mwaluso?

 RTO imathandiza kuti omasulila azikhala ku dela limene anthu ambili amakamba cinenelo cawo. Mlongo Karin, amene amamasulila ci Low German anati: “Kucokela pamene tinakakhala pa RTO ku Cuauhtémoc, m’dela la Chihuahua, ku Mexico, nthawi zonse timaseŵenzetsa ci Low German pokamba na omasulila anzathu, mu ulaliki, komanso tikapita kukagula zinthu. Nthawi zonse timakhala na anthu okamba cinenelo cathu. Timamva mawu okuluŵika amene tinawamvelako kale-kale, ndipo timadziŵa bwino mawu amene anthu amaseŵenzetsa pokamba masiku ano.”

 ’bale James, amene amatumikila m’gulu lomasulila ci Frafra ku Ghana, anavomeleza kuti nthawi zina amayewa kuyanjana na a m’banja la Beteli amene ali pa ofesi yawo ya nthambi. Koma anakambanso kuti: “Nimakondwela kuseŵenzela pa RTO. Nimasangalala kulalikila m’cinenelo cathu na kuona mmene anthu amakhudzidwila akamvela uthenga wabwino.”

 Kodi abale athu amasankha bwanji malo omangapo RTO? “Vuto limodzi limene timakhala nalo n’lakuti ku malo ena kulibe magetsi okwanila kapena madzi. Kwinanso kulibe intaneti, imene ni yofunika kuti omasulila azilandila zinthu zofunika kumasulila. Conco pofuna kumanga RTO, nthawi zina timaganizila malo angapo kumene cineneloco cimakambidwa,” anatelo m’bale Joseph, wa m’Dipatimenti Yoona za Mapulani na Mamangidwe Padziko Lonse, imene ili ku Warwick, mumzinda wa New York, ku America.

 Kukamba mwacidule, njila yofulumila kwambili komanso yochipilako yopangila ofesi yomasulila, ni kuikhazikitsa pa Bwalo la Misonkhano, pa Nyumba ya Ufumu, kapena pa nyumba ya amishonale, kuti omasulila azicita kupita kukaseŵenzelako. Ngati zonsezi palibe, abale angapatsidwe cilolezo cakuti agule nyumba na ofesi kumene omasulila akhoza kumakhala na kugwililako nchito. Ngati zinthu zasintha ku gulu la omasulila cineneloco, nyumbazo zingagulitsidwe, ndipo ndalama zake zingagwilitsidwe nchito kumene kukufunikila kwambili thandizo.

Amapatsidwa Zofunikila Kuti Nchito Ipitilize Kuyenda

 M’caka cautumiki ca 2020, tinagwilitsila nchito ndalama zokwana madola 13 miliyoni (a ku America) kuti nchito m’ma RTO ipitilize kuyenda. Magulu omasulila m’ma RTO amafunikila makompyuta, mapulogilamu apadela a pakompyuta, zipangizo zojambulila mawu, Intaneti, madzi, magetsi, na zina zofunikila. Kompyuta imodzi yokhala na zonse zofunikila kuti munthu mmodzi aziseŵenzetsa ingawononge ndalama zokwana madola pafupi-fupi 750 (a ku America). M’makompyutawo amaikamo mapulogilamu olipila komanso pulogilamu yopangidwa na gulu lathu yochedwa Watchtower Translation System. Pulogilamu imeneyi imathandiza omasulila kuti azigwila bwino nchito yawo komanso kuti azipeza mosavuta malifalensi amene afuna.

 Omasulila amapatsidwanso zipangizo zojambulila mawu, zimene zimawathandiza kuti azitha kujambula mawu, ali pa ofesi yawo. Zipangizo zimenezo zinathandiza kwambili pamene mlili wa COVID-19 unayamba, cifukwa omasulila ambili anakwanitsa kutenga zipangizo zimenezo n’kupita nazo ku nyumba zawo kuti azikaziseŵenzetsa pomasulila zofalitsa zoŵelenga na mavidiyo.

 Abale na alongo a kufupi na ma RTO, nthawi zambili amathandiza kupenda ngati zofalitsa zamasulidwa bwino, komanso kusamalila pa malowo. M’bale Cirstin wa pa RTO ya ci Afrikaans mumzinda wa Cape Town, ku South Africa anati: “Ofalitsa ambili ndiponso apainiya a nthawi zonse amakhala na mwayi woseŵenzetsa maluso awo kuno.”

 Ofalitsa odzipeleka amenewo amakondwela kukhala na mwayi umenewu. Mlongo wina amene amathandiza nchito pa RTO anakamba kuti kugwila nchito ku RTO kuli ngati “kupuma kampweya kabwino.” Abale na alongo enanso amadzipeleka kuŵelenga zinthu zofunika kujambula. Mlongo Juana, amene amamasulila ci Totonac ku Veracruz, ku dziko la Mexico, anati: “Popeza tsopano tili pafupi na matauni okamba cinenelo cathu, n’zosavuta kuti abale na alongo ambili azibwela kudzatithandiza kujambula zofalitsa zathu zongomvetsela na mavidiyo.”

 Koma kodi ma RTO athandiza kuti omasulila azimasulila zomveka bwino? Ambili mwa anthu mamiliyoni amene amaŵelenga zofalitsa zathu amayankha kuti, ‘Inde.’ M’bale Cédric, amene ali m’gulu lomasulila ci Kongo ku Democratic Republic of Congo, anati: “Cifukwa ca mmene tinali kumasulila ci Kongo, abale na alongo ena anali kucicha ‘ci Kongo ca m’zofalitsa zathu,’ cifukwa cinali cosiyana na mmene anthu ambili anali kukambila cineneloci. Koma lomba, amakamba kuti zofalitsa zathu zimamasulidwa m’ci Kongo camakono, cimene anthu amakamba tsiku na tsiku.”

 M’bale Andile, wa m’gulu lomasulila ci Xhosa, anamvapo zofanana na zimenezi ku South Africa. Iye anati: “Ambili amatiuza kuti aona kusintha pa kamasulidwe ka zofalitsa zathu. Ngakhale ana amene anali kukonda kuŵelenga Nsanja ya Mlonda m’Cizungu, tsopano amaiŵelenga m’ci Xhosa. Iwo amakonda kwambili Baibo ya Dziko Latsopano cifukwa inamasulidwa mmene anthu amakambila.”

 Ndalama zonse zomangila ma RTO, kuwasamalila, na kusamalila atumiki a m’maofesi amenewa zimacokela pa zopeleka zaufulu za nchito ya padziko lonse, kuphatikizapo zimene zimapelekedwa kupitila pa donate.pr418.com.