Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Nchito Yomanga Inayenda Bwino Mlili Usanayambe

Nchito Yomanga Inayenda Bwino Mlili Usanayambe

NOVEMBER 1, 2020

 Popeza anthu masauzande ambili amabatizika caka na caka, pafunika malo ambili olambilila. Pa cifukwa cimeneci, Madipatimenti Oona za Mapulani na Zomanga-manga padziko lonse (LDC) anakonza zomanga kapena kukonzanso malo olambilila oposa 2,700 m’caka cautumiki ca 2020. a

 Komabe, cifukwa ca mlili wa COVID-19, nchito zina zinalepheleka. Pofuna kuteteza abale na alongo athu, komanso potsatila malamulo a boma, Komiti Yoyang’anila Nchito Yofalitsa ya Bungwe Lolamulila inaimitsa nchito zambili zomanga padziko lonse. Ngakhale n’conco, m’caka cautumiki ca 2020, malo olambilila oposa 1,700 anamangidwa na kukonzedwanso mlili usanayambe. Kuwonjezela apo, nchito zikulu-zikulu zomanga zoposa 100 za m’maofesi a nthambi zinatha. Onani mmene abale athu apindulila na zimango ziŵili zimene zinatha kumangidwa.

 Ofesi ya Nthambi ya Cameroon. Ofesi ya nthambi yakale imene inali ku Douala inali yaing’ono kwambili, ndipo zinthu zambili zinafunika kukonzedwanso. Poyamba, Komiti Yoyang’anila Nchito Yofalitsa inafuna kukonzanso ofesi ya nthambiyo, koma inaona kuti padzaloŵa ndalama zambili kuposa ndalama zimene angapeze ngati aigulitsa. Anaganizilanso zogula malo na kumangapo ofesi ya nthambi yatsopano kapena kugula nyumba yakale n’kuikonza kuti ikhale ofesi ya nthambi. Koma zonsezo sizinatheke cifukwa ca mmene zinthu zinalili.

 Patapita nthawi yocepa, abale anamvela kuti a boma afuna kukonza msewu kumpoto kwa mzinda wa Douala, pafupi na Bwalo lathu la Misonkhano. Anaona kuti msewuwo udzapepukitsa mayendedwe na kuthandiza kuti pa bwalolo pakhale madzi na magetsi. Izi zinapangitsa kuti malowo akhale oyenelela kumangapo ofesi ya nthambi. Conco, Bungwe Lolamulila linavomeleza zomanga ofesi ya nthambi yatsopano kumbali ina ya Bwalo la Misonkhanolo.

Abale na alongo akuthandiza pa nchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ku Cameroon

 Abale na alongo na makampani anaseŵenzela pamodzi pogwila nchitoyo, zimene zinapulumutsa nthawi na ndalama. Nchitoyo inawononga ndalama zocepa kwambili kusiyana na zimene anali kuyembekezela. Inapulumutsa ndalama zoposa madola 2,000,000 a ku America! Banja la Beteli linakukila ku ofesi ya nthambi yatsopanoyo mlili wa COVID-19 utatsala pang’ono kuyamba.

Nchito yomanga Ofesi ya Nthambi ya Cameroon inatha mlili wa COVID-19 usanayambe

 Atumiki a pa Beteli ku Cameroon apindula cifukwa tsopano ali na malo abwino okhala na oseŵenzelapo. Iwo amaona kuti ofesi yawo ya nthambi yatsopano ni mphatso yocokela kwa Yehova. M’bale wina na mkazi wake anati: “Cimene tifuna ni kuseŵenza mwakhama na kupewa kuona mphatsoyi mopepuka.”

Abale na alongo akuseŵenza mu ofesi yawo yatsopano mlili usanayambe

 Ofesi Yomasulila Mabuku ya Citojolaba, ku Mexico. Kwa zaka zambili, gulu la abale na alongo omasulila Citojolaba linali kuseŵenzela ku ofesi ya nthambi ya Central America, imene ili kufupi na mzinda wa Mexico City. Komabe, anthu ambili okamba Citojolaba amakhala ku Altamirano na ku Las Margaritas. Madelawo ali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 1,000 kucokela ku ofesi ya nthambiyo! Conco, zinali zovuta kuti omasulila azimasulila cineneloci mogwilizana na mmene anthu amakambila. Zinalinso zovuta kuti ofesi ya nthambi ipeze abale na alongo oyenelela pafupi amene akanathandiza panchito yomasulila, komanso amene akanagwilitsidwa nchito pojambula zofalitsa za Citojolaba.

Abale na alongo akuthandiza pa nchito yomanga Ofesi Yomasulila Mabuku (RTO)

 Pa zifukwa zimenezi, Komiti Yoyang’anila Nchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulila inakonza zosamutsila gulu la omasulila Citojolaba ku dela limene cineneloci cimakambidwa. Conco, ofesi ya nthambi inakonza zogula nyumba na kuikonza kukhala ofesi yomasulila. Kucita zimenezi kunawononga ndalama zocepa poyelekezela na kumanga ofesi yatsopano kapena kucita lendi.

 Pofotokoza mmene wapindulila, womasulila wina anati: “M’zaka 10 zimene n’nagwila nchito yomasulila ku ofesi ya nthambi sin’nakumaneko na banja lililonse pafupi lokamba cinenelo cathu. Koma tsopano ofesi yathu ili kucimake kweni-kweni kwa anthu okamba Citojolaba. Nimalankhula ndi anthu okamba Citojolaba tsiku lililonse. Izi zathandiza kuti nicidziŵe bwino cinenelo cathu na kuwonjezela luso pa nchito yomasulila.”

Ofesi yomasulila mabuku ya Citojolaba isanakonzedwe komanso itakonzedwa

Nchito Zomanga m’Caka ca Utumiki ca 2021

 Ngati mikhalidwe idzalola, pali mapulani akuti m’caka ca utumiki ca 2021 timange maofesi omasulila (ma RTO) 75 na maofesi ophunzitsilako masukulu aumulungu. Komanso nchito 8 zikulu-zikulu zomanga maofesi a nthambi zidzapitiliza, kuphatikizapo nchito ya ku likulu la padziko lonse yomanga ofesi ya nthambi ku Ramapo, mumzinda wa New York, komanso nchito yosamutsa maofesi a nthambi a Argentina na Italy. Kuwonjezela apo, pafunika Nyumba za Ufumu zatsopano zoposa 1,000. Palinso Nyumba za Ufumu zoposa 6,000 zimene n’zowonongeka kwambili moti zifunika kuphwanyidwa na kumanga zina. Ndiponso pali Nyumba zina za Ufumu 4,000 zimene zifunika kukonzedwanso.

 Kodi ndalama zoseŵenzetsa pomanga na kukonzanso zimango zimenezi zimacokela kuti? M’bale Lázaro González, wa m’Komiti ya Nthambi ku Central America, anayankha funso limeneli pofotokoza za nchito yomanga Ofesi Yomasulila Mabuku ya Citojolaba. Iye anati: “M’dela la nthambi yathu, tilibe zinthu zambili zakuthupi. Conco popanda thandizo la gulu lonse la abale, sembe sitinakwanitse kumanga maofesi omasulila mabuku kuti abale athu kuno apindule. Ndalama zimene abale na alongo padziko lonse amapeleka, zathandiza kuti cikhale cotheka kumanga maofesi a omasulila m’madela amene zinenelo zawo zimakambidwa. Tiyamikila na mtima wonse gulu la abale la padziko lonse cifukwa ca kupeleka kwawo mowoloŵa manja.” Inde, nchito zomanga zimenezi zimatheka cifukwa ca zopeleka zanu ku nchito yapadziko lonse, zimene nthawi zambili zimapelekedwa kupitila pa donate.pr418.com.

a Dipatimenti Yoona za Mapulani na Zomanga-manga (LDC) imapanga mapulani na kutsogolela pa nchito yomanga Nyumba za Ufumu m’dela la nthambi yawo. Dipatimenti Yoona za Mapulani na Zomanga-manga Padziko Lonse, imene ili ku likulu la padziko lonse, imaona nchito zimene zingakhale zoyambilila kugwilidwa na mmene angazigwilile.