MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Nchito Yomasulila Msonkhano Wacigawo wa 2020 Wakuti “Kondwelani Nthawi Zonse”!
JULY 10, 2020
Mu July na August 2020, kwa nthawi yoyamba, abale na alongo padziko lonse lapansi adzatamba na kumvetsela msonkhano wacigawo pa nthawi imodzi. Kuti izi zitheke, pulogilamu yojambulidwa ya msonkhanowu inafunika kumasulidwa m’zinenelo zoposa 500. Nthawi zambili, pamatenga caka kapena kuposelapo kuti nchito yonse yojambula na kumasulila nkhani za msonkhano na mavidiyo ake ithe. Koma cifukwa ca mavuto obwela na mlili wa kolonavailasi, abale na alongo omasulila Msonkhano Wacigawo wa 2020 wakuti “Kondwelani Nthawi Zonse”! anafunika kutsiliza nchitoyi m’miyezi inayi cabe.
Nchito yaikulu imeneyi inacitika mothandizidwa na madipatimenti aŵili a ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova, Depatimenti Yothandizila pa Nchito Yomasulila na Depatimenti Yoyang’anila Nchito Yogula Zinthu Padziko Lonse. Depatimenti Yothandizila pa Nchito Yomasulila inaona kuti magulu ambili omasulila anali kufunikila zipangizo zowonjezeleka, maka-maka mamaikolofoni abwino, kuti akwanitse kugwila nchitoyi. Depatimenti Yoyang’anila Nchito Yogula Zinthu inakonza zogula mamaikolofoni 1,000 na kuwatumiza m’madela pafupi-fupi 200.
Kuti pasawonongeke ndalama zambili, anagula mamaikolofoni ambili panthawi imodzi, n’kuwanyamula kupita nawo pa malo amodzi. Kenako anawatenga kumeneko kupita nawo ku madela osiyana-siyana padziko lonse lapansi. Cifukwa cogula pa woda, maikolofoni imodzi inagulidwa madola 170 a ku America pa avareji, kuphatikizapo ndalama yonyamulila. Mtengowu unali wotsika na 20 pelesenti poyelekezela na kugula maikolofoni imodzi-imodzi.
A Dipatimenti Yoyang’anila Nchito Yogula Zinthu anafunika kugula na kutumiza zinthu zimenezi m’miyezi ya April na May 2020. Panthawiyi, makampani ambili sanali kuseŵenza mokwanila cifukwa ca mlili wa kolonavailasi. Ngakhale zinali conco, pofika kumapeto kwa May, maofesi ambili omasulila mabuku, maofesi a nthambi, komanso magulu ena omasulila anali atalandila zipangizo zofunikila.
M’bale Jay Swinney, amene amayang’anila depatimenti yoona zogula, anati: “Pa nthawi yonse ya nchitoyi, panali mgwilizano waukulu pakati pa madipatimenti osiyana siyana a pa Beteli na makampani osiyana-siyana amene anagwilitsidwa nchito. Tinakwanitsa kugwila nchitoyi mogwilizana, mwamsanga, komanso popanda kuwononga ndalama zambili za gulu pofuna kuthandiza abale athu. Si cina cinathandiza kuti izi zitheke, koma mzimu wa Yehova.”
M’bale Nicholas Ahladis, amene amatumikila m’Dipatimenti Yothandizila pa Nchito Yomasulila, anati: “Abale na alongo omasulila amene panthawiyo sanali kucoka panyumba cifukwa ca mlili, analimbikitsidwa kwambili atalandila katunduyo. Olo kuti anali kutali na anzawo oseŵenza nawo, anali kukwanitsa kuseŵenzela pamodzi na anzawowo pa nchito yomasulila na kujambula nkhani, maseŵelo, na nyimbo m’zinenelo zoposa 500.”
Iyi ni imodzi mwa nchito zambili zimene zinacitika kuti abale na alongo padziko lonse akhale na mwayi womvetsela Msonkhano Wacigawo wa mu 2020 wakuti “Kondwelani Nthawi Zonse”! Zopeleka zanu zimene mumapeleka mowoloŵa manja kupitila pa donate.pr418.com na njila zina n’zimene zinathandiza kuti tikwanitse kugula zinthu zofunika zimenezi.