Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Nkhani Zodalilika Komanso Zolimbitsa Cikhulupililo

Nkhani Zodalilika Komanso Zolimbitsa Cikhulupililo

DECEMBER 1, 2021

 Mboni za Yehova zimawakonda kwambili abale na alongo awo. (1 Petulo 2:17) Ambili a ife tingamve mmene anamvela mlongo wina wa ku Kenya dzina lake Tannis. Iye anati: “Nimafuna kudziŵa zimene zimacitika kwa abale na alongo anga padziko lonse.” Kodi mlongo Tannis, komanso mamiliyoni a Mboni zina amadziŵa bwanji zimene zikucitika padziko lonse? Kuyambila mu 2013, takhala tikuika malipoti a zocitika padanga lakuti Malo a Nkhani pa webusaiti yathu ya jw.org.

 Padanga lakuti Malo a Nkhani limeneli, pamaikidwa nkhani zodalilika zonena za Mboni za Yehova zokhudza kutulutsidwa kwa ma Baibo, nchito yopeleka thandizo pakagwa matsoka, nchito zamamangidwe, komanso zocitika zina. Pamapezekanso nkhani zokhudza abale na alongo athu amene ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. Cina, pamakhalanso zocitika zolimbikitsa monga makampeni a ulaliki, komanso mwambo wa Cikumbutso. Kodi nkhani zimenezi amafufuza ndani? Nanga zimalembedwa bwanji?

Kutola Nkhani na Kuzifalitsa

 Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani ndiyo imayang’anila Malo a Nkhani. Dipatimenti imeneyi ili ku likulu lathu la padziko lonse. Nayonso ili pansi pa Komiti ya Agwilizanitsi ya Bungwe Lolamulila. M’dipatimenti imeneyi muli abale na alongo oposa 100, ndipo ambili a iwo amagwilila nchito kunyumba. Pakati pawo pali olemba nkhani, ofufuza, ojambula zithunzi, komanso omasulila. Ena amaimilako gulu pokambilana na akulu-akulu aboma, mapulofesa, aziphunzitsi, ndiponso atolankhani. Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani imeneyi imathandizidwanso na maofesi enanso opitilila 80 ochedwa Maofesi a Zofalitsa Nkhani amene ali pa nthambi zosiyana-siyana padziko lonse.

 Kuti alembe nkhani ina, a mu Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani amaseŵenzela pamodzi na Maofesi a Zofalitsa Nkhani. Abale athu akatola nkhani yopatsa cidwi, amaifufuza kuti apeze maumboni odalilika. Izi ziphatikizapo kufunsa anthu mafunso, komanso kukambilana na akatswili. Akapeza maumboni odalilika, nkhaniyo amailemba, kuikonzanso bwino-bwino, kuiŵelenga, kuikamo zithunzi, na kuitumiza ku Komiti ya Agwilizanitsi kuti aione ngati angaivomeleze.

Mawu Oyamikila

 Kodi abale na alongo athu amamva bwanji poŵelenga nkhani zimenezi? Mlongo wina wa ku Philippines dzina lake Cheryl anati: “Tsiku lililonse, nimayamba na kuŵelenga nkhani zokhudza gulu la Yehova na anthu ake.”

 Anthu ambili amaona kuti pali kusiyana pakati pa nkhani zopezeka pa jw.org na nkhani zina za panyuzi. Tatiana wa ku Kazakhstan, anati: “Nkhani za pa jw.org nimaziŵelenga popanda cikaiko ciliconse. Ni zodalilika komanso zoona.” Mlongo Alma wa ku Mexico anati: “Nkhani za pa webusaiti yathu n’zolimbikitsa kwambili poziyelekezela na nkhani zopatsa nkhawa za m’dzikoli.”

 Nkhani za pa webusaiti yathu n’zodalilika, komanso zolimbitsa cikhulupililo. Bernard wa ku Kenya ananena kuti: “Nkhani za pa webusaiti yathu zanithandiza kuona abale na alongo padziko lonse monga banja langa, mosasamala kanthu za kumene akhala. Nimatha kuchula ngakhale maina awo m’mapemphelo anga, komanso zimene zikucitika kwa iwo.” Mlongo wina amenenso akukhala ku Kenya, anati: “Nthawi zonse nimakhala wokondwela nikaona nkhani yokamba za kutulutsidwa kwa Baibo m’cinenelo cina. Nkhani zimenezi zimanikumbutsa kuti Yehova alibe tsankho.”

Danga lakuti Malo a Nkhani limatithandiza kuchula mwacindunji mavuto amene abale na alongo athu akukumana nawo padziko lonse

 Nazonso nkhani zokamba za abale amene akuzunzidwa zimakhala zolimbikitsa. Mlongo Jackline wa ku Kenya anati: “Kuganizila za kulimba mtima kwawo kwalimbitsa cikhulupililo canga kwambili. Nthawi zonse nimafuna kuona cimene cinawathandiza kupilila. Naona kuti zinthu zimene anthu ena amaziona kukhala zazing’ono monga pemphelo, kuŵelenga Baibo, ngakhalenso kuimba nyimbo zimawathandiza abale athu kukhalabe olimba.”

 Mlongo wina wa ku Costa Rica dzina lake Beatriz, amayamikila kwambili nkhani zokamba pa matsoka a zacilengedwe. Iye ananena kuti: “Nkhani za pa webusaiti yathu, zimanithandiza kuona mmene gulu lathu limapelekela thandizo kwa abale athu mwamsanga komanso mwacikondi. Izi zimanitsimikizila kuti gulu lathu lilidi la Yehova.”

 Timayamikila kwambili mwayi umene tili nawo, wodziŵa zimene zikucitika kwa abale athu padziko lonse. Koma zimenezi sizikanatheka popanda zopeleka zanu za nchito ya padziko lonse. Ndipo ambili a inu mumacita zopeleka zanu kupitila pa donate.pr418.com. Timayamikila kwambili kupeleka kwanu mowolowa manja.