Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Nyimbo Zimene Zimatiyandikizitsa kwa Mulungu

Nyimbo Zimene Zimatiyandikizitsa kwa Mulungu

NOVEMBER 1, 2021

 Nyimbo ni mphatso yabwino yocokela kwa Yehova. Zingakhudze maganizo athu, kutitonthoza, komanso kutilimbikitsa. Ni mmene zilili na nyimbo zathu zopekedwa koyamba. Koma koposa pamenepa, nyimbo zimenezi zimatiyandikizitsa kwa Yehova.

 Kuyambila mu 2014, patulutsidwa nyimbo zopekedwa koyamba zopitilila 70. Ndipo tsopano, zina mwa nyimbo zimenezi zipezeka m’zinenelo zopitilila 500. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Ndani amakonza nyimbo zimenezi? Nanga zimakonzedwa bwanji?’

Zimene Zimacitika Pokonza Nyimbo

 Kagulu kopeka nyimbo kali m’Dipatimenti Yoona za Mavidiyo na Zomvetsela. Dipatimenti imeneyi amaiyang’anila ni a Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa. M’kagulu kopeka nyimbo muli abale na alongo 13 amene amathandizila popanga nyimbo, kuseŵenzela pamakina a nyimbo, kupanga ndandanda, komanso nchito zina. Kuwonjezela apo, Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa inavomeleza atumiki oseŵenzela kunyumba padziko lonse kuti azithandiza pa nchito yopeka, kuimba nyimbo pogwilitsa nchito zipangizo, komanso kuimba nyimbo pakamwa. Abale na alongo odzicepetsa amenewa amaseŵenzetsa maluso awo mosafuna kuchuka kapena kutamandidwa.

 Kodi nyimbo imapekedwa bwanji? Coyamba, Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa imasankha Malemba pamene pangazikidwe nyimboyo, komanso mmene ifunika kukhudzila omvetsela. Ndiyeno kagulu kopeka nyimbo kamakonza nyimboyo, na kulemba mawu ake. Kenaka, amajambula nyimbo yoyeselapo. Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa imaimvetsela nyimbo yoyeselapo imeneyo, na kupeleka malangizo enanso. Kenako, kagulu kopeka nyimbo kamakonzanso nyimboyo mwina na mwina na kujambula yeniyeni tsopano. Nyimbozi amazijambulila kumalo osiyanasiyana, kuphatikizapo m’maofesi a nthambi komanso m’nyumba za abale.

 Pozipeka komanso kuzijambula nyimbo zimenezi, abale athu amaseŵenzetsa mapulogilamu osiyana-siyana a pa kompyuta. Amagwilitsa nchito zipangizo monga, zida zoimbila, zokuzila mawu, komanso mamaikolofoni. Maikolofoni imodzi imagulidwa pa mtengo woyambila madola a ku America 100 mpaka 1,000. M’caka ca 2020, tinaseŵenzetsa ndalama zokwana madola 116,000 pa zipangizo zojambulila nyimbo.

 Kodi timacita ciyani kuti pasawonongeke ndalama zambili? M’malo mokhala na gulu lalikulu lopeka nyimbo pa Beteli, amagwilitsa nchito abale na alongo ambili oseŵenzela kunyumba. Cina, m’malo mwakuti anthu ambili abwele pamodzi kudzajambulitsa nyimbo zimenezi, kambili abale athu amapeka nyimbozi poseŵenzetsa mapulogilamu a pa kompyuta.

Nyimbo Zolimbitsa Cikhulupililo

 Abale na alongo amakonda kumvetsela nyimbo zopekedwa koyamba. Tara amene akukhala ku Germany, anati: “Nyimbozi zimanithandiza kukhazika mtima pansi nikakhala na nkhawa. Nikamazimvetsela mu cinenelo canga nimamva monga Yehova wanikumbatila.” Dmitry, m’bale wa ku Kazakhstan ananena kuti: “Nikamamvetsela nyimbozo sinimakhala na nkhawa yakuti mwina n’zosagwilizana na mfundo za m’Baibo.Ndipo nyimbozo zanithandiza kuikabe maganizo anga pa zinthu zauzimu.”

 Delia wa ku South Africa, anafotokoza mmene amamvela na nyimbo zopekedwa koyamba. Anati: “Nyimbo zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo canga. Nikakhala wosakondwa kapena nikakumana na zovuta zina zake, pamakhala nyimbo yogwilizana kwambili na zimene nikupitamo. Ndipo nthawi zina, malimba ake cabe a nyimbo amanitsitsimula.”

 Ena apeza nyimbo zina zopekedwa kukhala za pamtima pawo. Mwacitsanzo, Lerato wa ku South Africa, anati: “Nyimbo yakuti ‘Dziko Latsopano Lili Pafupi Kwambili,’ komanso yakuti ‘Dziko Latsopano Likubwelalo,’ zimanithandiza kuyelekeza kuti nili m’dziko latsopano ndipo nikulandila amayi anga okondeka. Nthawi zonse nikamazimvetsela, nimakhala ngati nikuona amayi akunithamangila atatambasula manja kuti anikumbatile.”

 Nyimbo ina yopekedwa koyamba inam’thandiza kwambili mtsikana wina ku Sri Lanka. Iye anati: “Aphunzitsi anga a sayansi ananizazila mwaukali pamaso pa anzanga m’kalasi, cifukwa cokhala mmodzi wa Mboni za Yehova. N’nacita mantha, moti n’nasoŵa cokamba. N’tabwelela kunyumba, amayi ananilimbikitsa kuti nimvetsele nyimbo yakuti ‘Ukaŵelenga, Udzalimba.’ Nyimbo imeneyi inanithandiza kuona kuti nifunika kufufuza na kukonzekela mowayankhila. Tsiku lotsatila, n’nakambilana nawo aphunzitsi anga. Iwo ananimvetsela ndipo anati lomba amvetsetsa zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila. Niyamikila gulu la Yehova potipatsa nyimbo zolimbikitsa zimenezi.”

 Kodi timacotsa kuti ndalama zogwilitsa nchito pokonza nyimbo zimenezi? Timaseŵenzetsa ndalama za nchito ya padziko lonse, zimene ambili a inu mumapeleka kupitila pa donate.pr418.com. Timayamikila kupeleka kwanu mowolowa manja.