MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Thandizo pa Matsoka a mu 2021—Abale na Alongo Athu Sananyalanyazidwe
JANUARY 1, 2022
Mu caka conse cautumiki ca 2021, a dziko lonse linali pa mavuto cifukwa ca mlili wa COVID-19. Monga inakambila nkhani yakuti “Kupeleka Thandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mlili wa Padziko Lonse,” tinawononga mamiliyoni a madola b popeleka thandizo panthawi ya mlili, komanso tinakhazikitsa makomiti opeleka thandizo oposa 950.
Pamene mliliwu unali kufalikila-falikila, ngozi zinanso zacilengedwe komanso zobwela cifukwa ca dyela la munthu, zinakhudza abale na alongo athu padziko lonse. Pofuna kuthandiza pa ngozi zotelo zoposa 200, Komiti ya Agwilizanitsi ya Bungwe Lolamulila inavomeleza kuwononga ndalama zina zokwana madola 8 miliyoni kuwonjenzela pa thandizo limene linalipo kale la COVID-19. Onani mmene zopeleka zanu zinagwilila nchito pothandiza anthu okhudzidwa na ngozi ziŵili zimene zinacitika posacedwapa.
Kuphulika kwa Phili la Nyiragongo
Pa May 22, 2021, Phili la Nyiragongo linaphulika m’dziko la Democratic Republic of the Congo. Ciphala ca moto wonyeketsa cinawononga manyumba, masukulu, komanso malo osungila madzi akumwa. Koma coopsa sicinali ciphala camoto cokhaci. Kwa masiku ndithu phililo litaphulika, utsi woipa unali paliponse mu mzinda wa Goma. Cina, panatsatilanso zivomezi zambili zing’ono-zing’ono. Kupitilila hafu ya anthu mu mzindawo anauzidwa kuti acoke. Masauzande ambili anacoka mu mzindawo, ndipo ena anathaŵila kumalile kwa dziko la Rwanda.
Pa anthu amenewa panali Mboni za Yehova pafupifupi 5,000. Ena nyumba zawo zinawonongeka phililo litaphulika, ndipo enanso katundu wawo unabedwa iwo atacoka. Conco a komiti yopeleka thandizo ku Rwanda komanso ya ku Democratic Republic of the Congo, anakonza zakuti apeleke thandizo kwa okhudzidwawo. Pokamba za komiti yopeleka thandizo, nthambi ya ku Congo (Kinshasa) inalemba kuti: “Olo kuti mu mzindawo munali cipwilikiti cokha-cokha, ndiponso anthu asanauzidwe kucokamo, komiti yopeleka thandizo inali itayamba kale kupeleka cakudya, madzi, zofunda, komanso zovala. Mu mzinda wina mmene munali abale athu oposa 2,000, komiti yopeleka thandizo inawakhomela matenti, kuwapatsa mamasiki, na kuwafotokozela mmene angapewele kutengela matenda a COVID-19 komanso kolela.
M’miyezi itatu cabe, abale athu anapeleka matani opitilila 6 a mpunga, matani 6 a cimanga, matani atatu a mafuta ophikila, komanso matani atatu a madzi. Kuti isawononge ndalama zambili, nthambi inakonza zogula zakudya m’dziko momwemo, m’malo moitanitsa zakudya zodula kucokela ku maiko ena.
Mlongo wina amene nyumba yake yatsopano inawonongeka na kuphulika kwa phililo anati: “Cinatiŵaŵa kwambili, ndipo tinakhwethemukilatu.” Koma banja lake litalandila thandizo lakuthupi komanso lauzimu, iye tsopano anati: “Na thandizo la Yehova, zofunikila kwenikweni tikali nazo. Taona kuti Yehova amatinyamulila katundu wathu, ndipo izi zimapangitsa kuti tipilila mosavuta.”
Mavuto Azacuma ku Venezuela
Kwa zaka zambili, ku Venezuela kwakhala mavuto aakulu azacuma. Abale athu kumeneko akukhala umoyo wovuta, kusoŵa cakudya, komanso kuwonjezeleka kwa zaupandu. Ngakhale n’telo, gulu la Yehova silinawasiye okha.
M’caka cautumiki capita, gulu lathu linawononga ndalama zopitilila madola 1.5 miliyoni kugula zakudya komanso sopo, na kuzipeleka ku mabanja ofunikila thandizo. Nthambi ya ku Venezuela inakamba kuti: “Sicinali copepuka kupeleka zakudya matani 130 mwezi uliwonse m’dziko lonse, na kuonetsetsa kuti abale ofunikila thandizo alandila.” Pofuna kuonetsetsa kuti cakudya cisawonongeke, kambili abale anali kutumiza zakudya zimene zimakhala nthawi yaitali. Nthambi inalembanso kuti: “Timagulilatu zakudya zambili m’nyengo yokolola pamene mitengo imakhala yotsika. Ndiyeno timapeleka zakudyazo poseŵenzetsa njila zosalila ndalama zambili.”
Leonel, wa m’komiti ya ku Venazuela, yopeleka thandizo pakacitika matsoka, amaukonda kwambili utumiki wake. Iye anati: “Nchito yopeleka thandizo ni yapadela. Utumiki umenewu wanilimbikitsa kwambili cimwalilile mkazi wanga na COVID-19. Nimakhala wotangwanika ndipo nimaona kuti ningapeleke thandizo lofunikila kwa abale. Nadzionela nekha kuti Yehova amasunga lonjezo lake lakuti sadzasiya anthu ake.”
M’bale wina amene analandila thandizo limeneli, anali mmodzi wa m’komiti yopeleka thandizo kumbuyoku. Iye anati: “Inenso inali nthawi yanga yolandila thandizo. Sanatipatse thandizo la kuthupi lokha. Abale anathandizanso ine na mkazi wanga kuti tisataye mtima. Iwo anatisamalila, kutitonthoza, na kutilimbikitsa.”
Ngozi zina zimangocitika mwadzidzidzi. Nthawi zonse gulu la Yehova limakhala lokonzeka kupeleka thandizo lofunikila mwamsanga. Timayamikila kwambili zopeleka zanu za nchito ya padziko lonse. Njila zina zimene mungatumizile copeleka canu azifotokoza pa donate.pr418.com. Timayamikila zedi kuwolowa manja kwanu.