Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Tumasitandi twa Ulaliki Tothandiza Pocitila “Umboni ku Mitundu Yonse”

Tumasitandi twa Ulaliki Tothandiza Pocitila “Umboni ku Mitundu Yonse”

APRIL 1, 2023

 Kwa zaka zoposa 10, ulaliki wa tumasitandi wakhala ukukopa anthu cidwi. Zungulile dziko lonse, anthu amatudziŵa tumasitandi tumenetu. Tunapangidwa mocititsa cidwi komanso n’tosavuta kuseŵenzetsa. Mwina mungavomelezane na mlongo wa ku Poland, dzina lake Asenata, amene anati: “Si twapamwamba koma n’tooneka bwino. N’tosavuta kuseŵenzetsa na kunyamula.”

 Kodi munayamba mwadzifunsapo mmene tunapangidwila?

Tunapangidwa Mwaluso

 Mu 2001, Bungwe lolamulila linavomeleza abale na alongo athu ku France kuti ayese maulaliki apoyela osiyanasiyana kuphatikizapo wa pa tumasitandi. Iwo anayesapo njila zambili. Mwacitsanzo, anasintha zola zamawilo na zonyamulila katundu zamawilo, n’kuyamba kuyalapo zofalitsa na kuzisungilamo. M’kupita kwa nthawi, ofesi ya thambi ku France inasankha mtundu wa tumasitandi tumene ofalitsa anaseŵenzetsa kwa zaka zambili.

Kasitandi kaulaliki koyambilila, ku France

 Abale ku France anakondwela kwambili na zotulukapo zabwino za kuyesa kwawo ulaliki wa poyela. Conco mu 2011, Bungwe Lolamulila linavomeleza pulogilamu yoyesa ulaliki wa poyela mumzinda wa New York, ku America, poseŵenzetsa tumasitandi na matebulo. Apainiya amene anatengako mbali pa makonzedwewa, anaona ubwino wa tumasitanditu komanso kuti tunali tosavuta kunyamula. Iwo anapelekanso malingalilo a mmene tumasitanditu tungapangidwile kuti tukhale tosavuta kuseŵenzetsa. Tumasitandi twakale topangidwa na mapulanga tunali tolemela komanso tovuta kunyamula. Conco anatupanganso kuti tukhale topepuka, koma osati toleluka kwambili moti n’kugwa na mphepo. Tumasitandi twatsopanotu tuli na mawilo aakulu komanso okonzedwa bwino. Izi zimapangitsa kuti tuziyenda mosavuta munthu akamakatuguguza. Cina tuli na kabokosi kakang’ono kosungilamo zofalitsa.

 Kuyesa njila yolalikila imeneyi kunakhala ni zotulukapo zabwino! Conco mu 2012, Bungwe Lolamulila linavomeleza kuseŵenzetsa tumasitandi twa ulaliki pa dziko lonse. Ndiyeno anapeza kampani imene ikanapanga tumasitandi twambili pogwilitsa nchito zinthu zopepuka koma zolimba.

 M’kupita kwa zaka, masinthidwe ang’ono-ang’ono anapangidwa ku tumasitandi tumenetu. Mwacitsanzo, mu 2015, kunawonjezedwa kansalu koteteza kasitandi ku mvula kokhala na pulasitiki yoonetsa mkati kutsogolo kwake. Dina, amene akhala ku Georgia, amayamikila kwambili mbali imeneyi. Iye anati, “Kasitandi kali na cotetezela mabuku ku mvula.” Mu 2017, zikwangwani za magineti zinapangidwa m’zinenelo zina. M’bale Tomasz wa ku Poland, anati: “Panali kukhala nchito yaikulu kusintha zikwangwani zomatika. Koma zikwangwani za magineti zinacepetsako nchito.” Mu 2019, panapangidwanso masinthidwe ena a zinthu zimene anali kuseŵenzetsa popanga tumasitandi komanso mmene anali kutupangila, kuti tukhale tolimbilako.

Kupanga Tumasitandi twa Ulaliki

 Tumasitandi twa ulaliki tumapangidwa na kampani imodzi kenako tumatumizidwa ku mipingo pa dziko lonse. Pali pano, kasitandi kamodzi kamapangidwa pamtengo wokwana madola 43 a ku America, ndalamazi siziphatikizapo zotumizila komanso zofunika zina. Pali pano, madola opitilila16 miliyoni a ku America aseŵenzetsedwa popanga tumasitandi, ndipo tokwana 420,000 twatumizidwa ku mipingo pa dziko lonse.

 Kuti tiseŵenzetse bwino ndalama za copeleka, timagula tumasitandi twambili pa nthawi imodzi. Kuwonjezela apo, mipingo ingathe kuitanitsa zinthu zokonzela tumasitandi tukaonongeka m’malo moitanitsa twatsopano.

Kugwilitsa Nchito Tumasitandi Polalikila

 Ofalitsa pa dziko lonse amasangalala kuseŵenzetsa tumasitandi twa ulalliki. Martina, wa ku Ghana, anati: “Pa njila zambili zolalikila, ndife timalondola anthu. Koma cimene nimakondela ulaliki wa pakasitandi n’cakuti anthu ndiwo amatilondola. Ngakhale anthu opita cabe mumsewu amalalikidwa.”

 M’dziko lina mu Africa, mwamuna wina anafika pakasitandi ndipo anatenga zofalitsa m’cinenelo cake. Patapita mlungu umodzi, anabwelanso ndipo anati: “Ninaŵelenga mabuku onse. Uthenga wake ni wofunika kwambili. Nipita kukauzako banja langa kumudzi.” Mudziwu unali pa mtunda wa makilomita 500. Pambuyo pa miyezi iŵili, anabwelelanso n’kunena kuti: “Anthu akumudzi kwathu anaŵelenga mabuku onse ndipo ni osangalala na zimene anaŵelenga. Afunitsitsa kukhala Mboni za Yehova. Koma ali ni mafunso. Mwacitsanzo, anamvetsa kuti ngati afuna kubatizidwa, ayenela kumizidwa m’madzi. Komabe, kulibe mtsinje kufupi na kumudzi kwathu. Kodi tiyenela kubwela kuno kuti tibatizidwe?” Ofalitsawo anapezela mwamunayu mpainiya amene amalankhula cinenelo cake. Kucokela pa nthawiyo, aŵiliwo akhala akukambilana nthawi zonse.

 N’zokondweletsa kuona tumasitandi twa ulaliki tukugwilitsidwa nchito polalikila “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) Kodi ndalama zopangila tumasitandi tumenetu zimacokela kuti? Pa zopeleka za nchito ya pa dziko lonse, ambili amacita zopelekazi kupitila pa donate.pr418.com. Zikomo cifukwa ca kuwolowa manja kwanu.