Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Zoculuka Zimathandizila pa Zimene Zikusoŵa

Zoculuka Zimathandizila pa Zimene Zikusoŵa

OCTOBER 1, 2020

 Mboni za Yehova zimagwila nchito zokhudza kulambila komanso zothandiza anthu m’maiko oposa 200. Koma maiko 35 okha ndiwo amalandila zopeleka zokwanila za m’dziko lawo zimene zimawathandiza kulipilila zofunikila. Kodi ndalama zimene zimagwilitsidwa nchito m’maiko amene si olemela zimacokela kuti?

 Bungwe Lolamulila limapenda zimene Mboni za Yehova padziko lonse zikufunikila kuti zizilambila bwino Yehova na kulalikila uthenga wabwino. Ndalama amazipangila bajeti mosamala na kuziseŵenzetsa mwanzelu. Ngati ofesi ya nthambi yalandila ndalama zambili kuposa zimene zikufunikila, zotsalazo amazipeleka kuti zikathandizile m’maiko osoŵa. Kucita zimenezi n’kofanana na zimene Akhristu oyambilila anali kucita. Iwo anali kuthandizana “kuti pakhale kufanana.” (2 Akorinto 8:14) Anali kuseŵenzetsa zoculuka zimene anali nazo kuti athandizile Akhristu ena amene anali osoŵa.

 Kodi abale athu amene amalandila thandizo la ndalama kucokela ku maofesi ena a nthambi amamvela bwanji? Mwacitsanzo, ndalama zocokela ku maofesi ena a nthambi zinagwilitsidwa nchito pokonzanso Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Mafinga ku Tanzania. Ku dzikolo, anthu opitilila pa hafu ni osauka kwambili. Mpingowo unalemba kuti: “Kucokela pamene Nyumba ya Ufumuyi inakonzedwanso, ciŵelengelo ca opezeka pa misonkhano cakwela ngako! Tiyamikila kwambili gulu la Yehova komanso abale padziko lonse cifukwa ca kuwolowa manja kwawo, kumene kwathandiza kuti tikhale na malo okongola amenewa olambilila.”

 Abale na alongo athu ena ku Sri Lanka anali kuvutika na njala cifukwa ca mlili wa COVID-19. Mlongo Imara Fernando na mwana wake wamwamuna, Enosh, ni ena mwa amene anakhudzidwa na vutoli. Koma cifukwa ca zopeleka zocokela ku maiko ena, pano tikamba analandila thandizo. Iwo anapanga khadi na kulembapo kuti: “Tiyamikila abale amene anationetsa cikondi panthawi yovuta imeneyi. Ndife okondwela kwambili kukhala m’banja limeneli, ndipo tipempha kuti Yehova apitilize kuthandiza abale athu onse m’masiku otsiliza ano.”

Imara and Enosh Fernando

 Mosasamala kanthu kuti amakhala kuti, abale na alongo athu ni okonzeka kugaŵana na ena zimene ali nazo. Mwacitsanzo, Enosh, anapanga kabokosi kake kakang’ono ka zopeleka kuti nayenso azipelekako zopeleka zokathandizila mabanja osauka. Mlongo Guadalupe Álvarez nayenso ali na mzimu wowolowa manja ngati umenewo. Iye amakhala ku Mexico, m’dela limene anthu ambili amalandila ndalama zocepa kwambili, kapena salandila ndalama zilizonse za pamwezi. Ngakhale n’conco, iye amapeleka zopeleka mmene angathele. Mlongoyu anati: “Nimayamikila Yehova cifukwa ca ubwino wake na cikondi cake cokhulupilika. Nidziŵa kuti zopeleka zanga zidzaphatikizidwa na za ena, ndipo zidzathandiza abale anga amene afunika thandizo.”

 Maofesi a nthambi amene amatumiza ndalama ku madela osauka amakondwela kucita zimenezo. M’bale Anthony Carvalho, amene amatumikila m’Komiti ya Nthambi ku Brazil anati: “Kwa zaka zambili, tinali kufunika thandizo la ndalama locokela ku maiko ena kuti nchito ya Ufumu iziyenda bwino m’dziko lathu. Cifukwa ca thandizo limenelo, tinaona kupita patsogolo kwakukulu. Koma lomba zinthu zinasintha m’dziko lathu pa zacuma, ndipo tili na mwayi wothandizako ena. Abale tsopano akaganizila nchito ya padziko lonse yolalikila, amaona kuti ali na udindo wothandiza pa nchitoyi monga ophunzila a Yesu odzimana.”

 Kodi Mboni za Yehova zingathandize bwanji abale na alongo awo amene afunika thandizo? Osati mwa kutumiza ndalama mwacindunji ku maofesi a nthambi a ku maiko ena, koma mwa kupeleka zopeleka za nchito ya padziko lonse. Angacite zimenezi mwa kuponya zopeleka zawo m’bokosi la mpingo wawo lolembedwa kuti “Za Nchito ya Padziko Lonse”, kapena kupitila pa donate.pr418.com. Timayamikila kwambili zopeleka zonse zimenezi.