Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANI MASO!

Nkhondo ya ku Ukraine Iwonjezela Njala Padziko Lonse

Nkhondo ya ku Ukraine Iwonjezela Njala Padziko Lonse

 Pa May 19, 2022, nthambi ya UN yoona zacitetezo yochedwa United Nations Security Council, inalandila malipoti kwa akulu-akulu a boma oposa 75. Malipotiwo anaonetsa kuti, “ngakhale kuti mlili wa COVID-19 komanso kusintha kwa nyengo zabweletsa vuto la kucepa kwa cakudya padziko lonse, nkhondo ya ku Ukraine yawonjezela vutoli, cakuti m’maiko ena njala yafika poopsa kwambili.” Posakhalitsa, magazini yochedwa The Economist inalengeza kuti, “cifukwa ca nkhondo imeneyi, anthu oculuka padzikoli la mavuto kale, akhala pa njala yadzaoneni.” Baibo inakambilatu kuti m’nthawi yathu ino kudzakhala mavuto aakulu a kusoŵa cakudya. Koma imapelekanso njila ya mmene tingacitile nawo mavutowa.

Baibo inakambilatu za kusoŵeka kwa cakudya

  •   Yesu analosela kuti: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala.”Mateyu 24:7.

  •   Buku la Chivumbulutso limanena za amuna anayi ophiphilitsa okwela pamahachi. Mmodzi wa iwo amaimila nkhondo. Wina amene akubwela pambuyo pake akuimila njala yadzaoneni panthawi imene cakudya cidzakhala cosoŵa kwambili, komanso ca mtengo woboola m’thumba. “Ndinaona hachi yakuda. Wokwelapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mawu . . . akuti: “Kilogalamu imodzi ya tiligu, mtengo wake ukhala dinari imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi.”—Chivumbulutso 6:5, 6.

 Maulosi a m’Baibo onena za njala amenewa akukwanilitsidwa m’nthawi yathu ino, imene Baibo imaicha “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Kuti mudziŵe zambili za “masiku otsiliza,” komanso za okwela pamahachi ochulidwa m’buku la Chivumbulutso, tambani vidiyo yakuti Dziko Linasintha Kuyambila mu 1914. Komanso ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?

Mmene Baibo Ingatithandizile

  •   Baibo ili na ulangizi wanzelu umene ungatithandize kudziŵa mocitila na zovuta zimene timakumana nazo, kuphatikizapo kukwela kwa mitengo ya cakudya, ngakhalenso kusoŵa kumenene kwa cakudyaco. Onani zitsanzo m’nkhani yakuti “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”

  •   Baibo imatipatsanso ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino. Imatiuza kuti nthawi izafika pamene “padziko lapansi padzakhala tiligu wambili,” moti munthu aliyense adzakhala na cakudya ca mwana alilenji. (Salimo 72:16) Ngati mufuna kudziŵa zambili za tsogolo limene Baibo ikulonjeza, komanso cifukwa cake muyenela kuikhulupilila, ŵelengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”