Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANI MASO!

Kukwela Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse-Kodi Baibo Imakambapo Ciyani?

Kukwela Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse-Kodi Baibo Imakambapo Ciyani?

 “Cuma ca padziko lonse cikuloŵanso pansi,” anacenjeza motelo pulezidenti wa bungwe la World Bank Group mu lipoti la June 2022. Anapitiliza kuti, “Koma pa nthawi ino zinthu zakwela mitengo kwambili pamene cuma ca padziko lonse sicikupita patsogolo kwenikweni.”

 “Mitengo ya mafuta na zakudya yakwela mwamsanga, ndipo anthu okhala m’maiko osaukilapo ni amene akhudzidwa kwambili,” linatelo bungwe la International Monetary Fund.

 Baibo imatithandiza kumvetsa cifukwa cake tikukumana na mavuto a zacuma amenewa. Imatiuzanso zimene tingacite kuti tipilile mavuto amenewa. Ndipo imapelekanso ciyembekezo cakuti mavutowa adzathelatu.

Kukwela mitengo kwa zinthu ‘m’masiku otsiliza’

  •   Baibo imacha nthawi imene tikukhalamo kuti “masiku otsiliza.”—2 Timoteyo 3:1.

  •   Yesu anakamba kuti m’masiku otsiliza “kudzawoneka zowopsa,” kapena kuti zinthu zocititsa mantha. (Luka 21:11) Kukwela mitengo kwa zinthu kumadetsa anthu nkhawa. Anthu amadela nkhawa za tsogolo lawo komanso kuti adzayamba kupeza bwanji zofunikila za mabanja awo.

  •   Buku la Chivumbulutso linakambilatu kuti m’nthawi yathu ino zakudya zidzakwela mtengo. Linati: “Ndinamva mawu. . . Mawuwo anali akuti: “Kilogalamu imodzi ya tiligu, mtengo wake ukhala dinali imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balele, mtengo wake ukhala dinali imodzi.’”—Chivumbulutso 6:6.

 Kuti mudziŵe zambili za “masiku otsiliza” komanso za ulosi wa m’buku la Chivumbulutso, tambani vidiyo yakuti Dziko Linasintha Kucokela mu 1914 komanso ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?

Mmene mavuto onse a zacuma adzathele

  •   “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

  •   “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:16.

  •   “Yehova wanena kuti: ‘Cifukwa ca kupondelezedwa kwa osautsika, cifukwa ca kuusa moyo kwa anthu osauka, ndidzanyamuka pa nthawiyo.’”—Salimo 12:5. a

 Posacedwapa, Mulungu adzathetsa kupanda cilungamo m’zacuma kumene kukucitika padziko lonse lapansi, osati m’dziko limodzi cabe. Kuti mudziŵe mmene izi zidzacitikile, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Maiko Angathe Kuyendetsa Cuma Mokomela Aliyense?

 Ngakhale masiku ano, Baibo ingakuthandizeni kudziŵe zimene mungacite na kukwela mtengo kwa zinthu. Ingakuthandizeni bwanji? Ili na malangizo othandiza a mmene mungaseŵenzetsele ndalama mwanzelu. (Miyambo 23:4, 5; Mlaliki 7:12) Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Muzisamala Ndalama” komanso yakuti “Zimene Mungacite Ngati Mukupeza Ndalama Zocepa.

a Yehova ni dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.