Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Thomas Jackson/Stone via Getty Images

KHALANI MASO!

Kumene Mungapeze Ciyembekezo mu 2024—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Kumene Mungapeze Ciyembekezo mu 2024—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Anthu ambili amaona kuti palibe njila yothetsela mavuto amene adzakhudza dziko lonse mu 2024. Ngakhale n’telo, tingakhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino. Kodi tingacipeze kuti?

Baibo imatipatsa ciyembekezo

 Baibo inalonjeza kuti Mulungu adzacotsapo mavuto amene amapangitsa kutaya ciyembekezo masiku ano. Posacedwa, Mulungu “adzapukuta misozi yonse mʼmaso [mwathu] ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kubuula kapena kupweteka.”Chivumbulutso 21:4.

Mmene Baibo ingakuthandizileni pali pano

 Baibo imatipatsa ciyembekezo ca tsogolo labwino. Ciyembekezoci cingakuthandizeni kuti musataye mtima komanso kuti muziona zinthu m’njila yoyenela. (Aroma 15:13) Malangizo a m’Baibo angakuthandizeni kulimbana na mavuto amene mumakumana nawo pali pano, monga umphawi, kupanda cilungamo, komanso matenda.

 Cititsani kuti caka ca 2024 cikhale cabwino kwa inu na banja lanu. Phunzilani zambili za mmene Baibo ingakuthandizileni. Yambani kuphunzila Baibo kwaulele mothandizidwa na munthu wina. Dziŵani mmene Mulungu angakupatsileni “mtendele” pali pano, komanso “tsogolo labwino ndi ciyembekezo cabwino.”—Yeremiya 29:11.