Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KHALANI MASO!

Kulambila Zifanizilo—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?

Kulambila Zifanizilo—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?

 Pofotokoza mwambo womwe unacitikila ku chalichi ca St. Peter’s Basilica pa March 25, 2022, Catholic News Service inanena kuti: “Papa Francis, ataimilila pamaso pa cifanizilo ca Mariya Woyela, anatseka maso, kuŵelamitsa mutu, na kuyamba kupemphela mwakacetecete. Iye anacondelela mtendele kwa Mayi Mariya.” Ndipo Lipoti la Vatican News linawonjezela kuti: “Papayo anapembedzela mtima woyela wa Mariya kuti anthu onse akhale pamtendele, maka-maka maiko aŵili a Russia na Ukraine.”

 Nanga inu muganiza bwanji? Kodi n’koyenela kupemphela pamaso pa zifanizilo, kapena kuzigwilitsa nchito polambila? Ganizilani zimene mavesi awa a m’Baibo amanena:

  •   “Usadzipangile fano kapena cifanizilo ca cinthu ciliconse cakumwamba kapena capadziko lapansi, kapenanso cam’madzi a padziko lapansi. Usaziwelamile kapena kuzitumikila, cifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipeleka kwa ine ndekha.”—Ekisodo 20:4,, 5. a

  •   “Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide, Ntchito ya manja a munthu wocokela kufumbi. Pakamwa ali napo koma salankhula, Maso ali nawo koma saona. Makutu ali nawo koma satha kumva. Mphuno ali nayo koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu. Mapazi ali nawo koma sayenda. Satulutsa mawu ndi mmelo wawo. Amene amawapanga adzafanana nawo. Onse amene amawakhulupilila adzakhala ngati mafanowo.”—Salimo 115:4-8.

  •   “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapeleka ulemu wanga kwa wina aliyense, kapena kupeleka ulemelelo wanga, kwa zifanizilo zogoba.”—Yesaya 42:8.

  •   “Thawani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.

  •   “Pewani mafano.”—1 Yohane 5:21.

 Kuti mudziŵe zambili pa zimene Baibo imakamba za kuseŵenzetsa zifanizilo polambila, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopembedza Zizindikiro?” Mungatambenso vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amafuna Kuti Anthu Azigwiritsa Ntchito Zizindikiro Pomulambira?

 Mungafunenso kudziŵa zimene Baibo imakamba pa nkhani izi:

Photo credit: Vincenzo Pinto/AFP via Getty Images

a Dzina lenileni la Mulungu ni Yehova. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”