KHALANI MASO!
Kuombelana Mfuti Kocititsa Kakasi Padziko Lonse—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
M’mwezi wa July 2022, padziko lapansi panacitika zaciwawa zowombelana mfuti zocititsa kakasi aliyense. Nazi zitsanzo:
“Kuphedwa kwa wandale wodziŵika kwambili ku Japan [Nduna yaikulu yakale ya boma dzina lake Shinzo Abe] kwacititsa anthu nthumanzi padziko lonse. Anthu ali kakasi osakhulupilila. Zili conco makamaka cifukwa m’dzikoli zaciwawa si kwenikweni, komanso cifukwa ca malamulo okhwima pankhani yokhala na mfuti.”—Inatelo nyuzipepala ya The Japan Times ya July 10, 2022.
“M’dziko la Denmark anthu ni odabwa kwambili cifukwa munthu wonyamula mfuti anapha anthu atatu pamalo aakulu ogulako zinthu mu Copenhagen.”—Inatelo nyuzipepala ya Reuters July 4, 2022,
“Ku South Africa: Anthu 15 anaphedwa anthu ena powawombela mfuti pamalo omwela moŵa ku komboni ya Soweto.”—Inatelo nyuzipepala ya The Guardian ya July 10, 2022.
“Anthu oposa 220 anaphedwa powombeledwa mfuti ku America. Ciwawaci cinacitika pa holide ya pa July 4.”—Inatelo CBS News ya July 5, 2022.
Kodi ciwawa cowombelana mfuti cidzatha? Kodi Baibo ikambapo ciyani?
Zaciwawa Zidzatha
Baibo imanena kuti masiku ano ni “masiku otsiliza.” Imati panthawi imeneyi anthu adzakhala oopsa, ankhanza, ndiponso zigananga. (2 Timoteyo 3:1, 3) Makhalidwe amenewa amapangitsa anthu kukhala mwamantha. (Luka 21:11) Komabe, Baibo imatilonjeza kuti nthawi idzafika pamene zaciwawa zidzatha. Imati “Anthu anga adzakhala pamalo amtendele ndi pamalo otetezeka. Adzakhala m’malo abata ndiponso aphee!” (Yesaya 32:18) Koma kodi ciwawa cidzatha motani?
Mulungu adzacotsa anthu onse oipa padziko lapansi, ndipo adzawononga zida zonse zankhondo.
“Koma oipa adzacotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.
Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:9.
Mulungu adzacotsa zoyambitsa ciwawa mwa kuphunzitsa anthu kuti akhale amtendele.
“Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phili langa lonse loyela, cifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.”—Yesaya 11:9.
Ngakhale masiku ano, Mulungu akuphunzitsa anthu padziko lonse kuti aleke kucita zaciwawa na kuseŵenzetsa zida zankhondo. Kutanthauza kuti asule “malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzila mitengo.”—Mika 4:3.
Kuti mudziŵe zowonjezela pa zimene Baibo imalonjeza kuti padziko lapansi sipadzakhalanso cocititsa mantha ciliconse, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi N’zotheka Kukhala Mopanda Mantha?”
Kuti mudziŵe zambili pa mfundo yakuti zaciwawa zidzathelatu padziko lapansi, ŵelengani nkhani yakuti “Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!”