KHALANI MASO!
Kodi Tsankho Pakati pa Mitundu Lingathe?—Nanga Baibo Imati Ciyani?
Anthu ambili amaona kuti tsankho pakati pa mitundu silingathe.
“Kusankhana mitundu kwatsamwitsa mabugwe, zikhalidwe za anthu, komanso umoyo wa anthu wa tsiku na tsiku kulikonse padziko.”—António Guterres, Kalembela Wamkulu wa bungwe la UN.
Kodi kusankhana mitundu kudzatha? Nanga Baibo imati ciyani?
Mmene Mulungu amaionela mitundu yosiyana-siyana
Baibo imatiphunzitsa mmene Mulungu amaonela anthu amafuko wosiyana-siyana.
“Kucokela mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.”—Machitidwe 17:26.
“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Baibo ionetsa kuti anthu onse ali pacibale ceniceni, ndipo Mulungu amalandila anthu a mitundu yonse.
Mmene kusankhana mitundu kudzathele
Cimene cidzathetse tsankho ni Ufumu wa Mulungu, umene ni boma lakumwamba. Boma limenelo lidzaphunzitsa anthu kucitilana cilungamo. Anthu onse adzaphuzila mothetsela maganizo ali onse atsankho amene angakhale nawo.
“Anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzila cilungamo.”—Yesaya 26:9.
“Nchito ya cilungamo ceniceni idzakhala mtendele, ndipo zocita za cilungamo ceniceni zidzakhala bata ndi mtendele mpaka kale-kale.”—Yesaya 32:17.
Masiku ano, athu mamiliyoni akuphunzila kucokela m’Baibo mmene angamacitile mwaulemu na anthu anzawo.
Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani ya m’magazini ya Galamuka! yakuti “Kodi Kuli Mankhwala Othetsela Tsankho?”
Ŵelenganinso nkhani yakuti “Mmene Mungauzire Mwana Wanu za Kuipa Kosankhana Mitundu,” kuti mudziŵe mmene makolo angathandizile ana awo pa nkhaniyi.