Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Baibo Imakamba pa Nkhani ya Kuteteza Akazi

Zimene Baibo Imakamba pa Nkhani ya Kuteteza Akazi

 Pa dziko lonse, azimayi na atsikana mamiliyoni acitilidwapo nkhanza. Kodi ndinu mmodzi wa iwo? Tiyeni tione cimene cionetsa kuti Mulungu amafuna kuti mukhale wotetezeka komanso zimene adzacita pa nkhani yocitila nkhanza akazi.

 “Nili mwana, mlongo wanga anali kunimenya na kuninyoza tsiku lililonse. N’takwatiliwa, naonso apongozi anga aakazi anali kunicitila nkhanza. Iwo na apongozi aamuna anali kucita nane zinthu monga kapolo. N’nayamba kuganiza zongodzipha.”​—Madhu, a India.

 Bungwe Loona Zaumoyo pa Dziko Lonse linati, “Khalidwe locitila nkhanza azimayi n’lofala kwambili padzikoli.” Bungweli linapeza kuti pafupi-fupi mkazi mmodzi pa akazi atatu alionse, panthawi ina anamenyedwapo kapena kucitilidwa nkhanza zokhudza kugonana mu umoyo wake.

 Ngati zaconco zinakucitikilamponi, mungamadzione ngati wosatetezeka. Mungamaganize kuti munthu aliyense angakucitileni nkhanza monga kukunyozani, kukumenyani, kapena kukucitani nkhanza zokhudza kugonana. Nkhanza zotelo zingakupangitseni kuyamba kuganiza kuti anthu ambili amaona akazi ngati anthu osafunika. Koma kodi Mulungu amaona kuti akazi ni ofunikadi?

Baibo imaonetsa kuti Mulungu amafuna kuti akazi azikhala otetezeka

Kodi Mulungu amawaona bwanji akazi?

 Lemba: “[Mulungu] anawalenga mwamuna ndi mkazi.”​—Genesis 1:27.

 Tanthauzo lake: Mulungu ndiye analenga amuna komanso akazi. Iye amaona kuti onse ayenela kulemekezedwa. Cina, amafuna kuti mwamuna “azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha,” osati kumulamulila, kaya pogwilitsa nchito mawu oipa, kapena kumucita nkhanza. (Aefeso 5:33; Akolose 3:19) Zimenezi zionetsa bwino kuti Mulungu amafuna kuti akazi azikhala otetezeka.

 “Nili mwana, acibale anga anali kunicitila nkhanza zokhudza kugonana. N’takwanitsa zaka 17, abwana anga ananiopseza kuti adzanicotsa nchito nikakana kugona nawo. N’takula, mwamuna wanga, makolo anga, komanso anansi anga, onse anali kunicitila zinthu mopanda ulemu. Koma m’kupita kwanthawi n’naphunzila za Yehova, b amene ni Mlengi. Iye amalemekeza akazi. Zimenezi zinanitsimikizila kuti iye amanikonda, komanso amaniona kuti ndine wofunika.”​—Maria, Argentina.

N’ciyani cingakuthandizeni kumvelako bwino?

 Lemba: “Pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”​—Miyambo 18:24.

 Tanthauzo lake: Mnzanu weniweni angakuthandizeni. Ngati muona kuti zingathandize, uzan’koni mnzanu amene mumadalila mmene mukumvela.

 Kwa zaka 20, mobweleza-bweleza n’nali kucitidwa nkhanza zokhudza kugonana. Izi zinanipangitsa kukhala wosasangalala, wankhawa, komanso wopsinjika maganizo. Koma pamene n’nafotokoza zimene zinanicitikila kwa wina wake amene anali wofunitsitsa kunimvetsela, n’namva monga natula cikatundu colema.”​—Elif, Türkiye.

 Lemba: Mutulileni “nkhawa zanu zonse [Mulungu], cifukwa amakufunilani zabwino”​—1 Petulo 5:7.

 Tanthauzo lake: Mukamapemphela, Mulungu amamvetseladi. (Salimo 55:22; 65:2) Cifukwa cakuti amasamala za inu, angakuthandizeni kudziŵa kuti ndinu wofunika kwambili.

 “Kuphunzila za Yehova kunayamba kucepetsako ululu wa mumtima umene n’nali nawo. Lomba nimapemphela kwa Mulungu na kumuuza zonse za mumtima mwanga. Iye ali monga bwenzi limene limamvetsadi mmene nikumvela.”​—Ana, Belize.

Kodi Mulungu adzathetsadi khalidwe locitila nkhanza akazi?

 Lemba: ‘Yehova . . . adzaweluza mwacilungamo mwana wamasiye komanso anthu opondelezedwa, kuti munthu wamba wocokela kufumbi asadzawacititsenso mantha.’ ​—Salimo 10:​17, 18.

 Tanthauzo lake: Posacedwa, Mulungu adzathetselatu zinthu zopanda cilungamo monga kucitila nkhanza akazi komanso kuwacitila zaciwawa.

 Kuphunzila zakuti posacedwa Yehova adzathetsa khalidwe locitila nkhanza azimayi na atsikana, kwakhala ngati mankhwala ocilitsa kwa ine. Kwanipatsa mtendele wa mumtima.”​—Roberta, Mexico.

 Kuti muphunzile za ciyembekezo cimene Baibo imapeleka, cifukwa cake muyenela kukhulupilila malonjezo ake, komanso mmene Mboni za Yehova zimathandizila anthu poseŵenzetsa Baibo masiku ano, pemphani kuti adzakuyendeleni.

 Citani daunilodi nkhani ino imene inapangidwa m’njila yakuti ingacitiwe pulinti.

a Maina asinthidwa.

b Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”