Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Rui Almeida Fotografia/Moment via Getty Images

KHALANI MASO!

Kodi Baibulo Limatipo Ciyani pa Ciwawa Cocitika Cifukwa ca Ndale?

Kodi Baibulo Limatipo Ciyani pa Ciwawa Cocitika Cifukwa ca Ndale?

 Ciwawa cocitika cifukwa ca ndale cikuonjezeka pa dziko lonse.

  •   Atsogoleli 39 a magulu a zandale anaphedwa ku Mexico, uku n’kuyamba zotelezi kucitika pa mlingo waukulu conco. Kuwonjezela apo, zaciwawa zocitika cifukwa ca ndale zikuonjezekanso. Zimenezi zadabwitsa anthu m’dzikolo ndipo zikuwasokoneza pamene akucita masankho a mu 2023-2024.

  •   Posacedwapa ku Europe, zaciwawa zocitika cifukwa ca ndale zakhala zikuonjezeka. Mwacitsanzo, pa May 15, 2024 anthu anayesa kupha nduna yaikulu ya dziko la Slovakia.

  •   Anthu m’dziko la America ndi odabwa kwambili cifukwa pa July 13, 2024 anthu ena anayesa kupha Donald Trump, yemwe anali pulezidenti wakale wa dzikolo.

 N’cifukwa ciyani ciwawa cocitika cifukwa ca ndale cikuonjezeka? Kodi cidzatha? Nanga Baibulo limakambapo ciyani?

Baibulo linakambilatu kuti anthu adzagawikana cifukwa ca ndale

 Baibulo linakambilatu kuti m’nthawi yathu ino, imene limati ndi “masiku otsiliza,” anthu ambili adzakhala ndi makhalidwe amene adzayambitsa ciwawa komanso kusagwilizana.

  •   “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Anthu adzakhala . . . osayamika, osakhulupilika, . . . osafuna kugwilizana ndi ena, . . . oopsa, . . . ocitila anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula cifukwa ca kunyada.”—2 Timoteyo 3:1-4.

 Baibulo linakambilatunso kuti zipolowe, monga anthu kuukila boma komanso mavuto a zandale, zidzaonjezeka m’nthawi yathu ino. (Luka 21:9, mawu a m’munsi) Ngakhale n’conco, ciwawa cocitika cifukwa ca ndale komanso kugawikana, sizidzakhalako mpaka kalekale.

Kutha kwa ciwawa cocitika cifukwa ca ndale

 Baibulo limafotokoza kuti Mulungu adzacotsapo maboma onse a anthu ndipo adzakhazikitsa boma lake lakumwamba.

  •   “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.

 Ufumu wa Mulungu udzagwilizanitsa anthu ndipo udzabweletsa mtendele padziko lonse.

  •   Wolamulila wake, Yesu Khristu, amachedwa “Kalonga Wamtendele,” ndipo iye adzaonetsetsa kuti “mtendele sudzatha.”—Yesaya 9:6, 7.

  •   Ngakhale panopa, nzika za Ufumu umenewu zikuphunzila kukhala mwamtendele. Pa cifukwa cimeneci, Baibulo limati: “Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzila mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo.”—Yesaya 2:3, 4.

 Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?” ku Chichewa, ndiponso onelelani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?