Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 154

“Cikondi Sicitha”

“Cikondi Sicitha”

(1 Akorinto 13:8)

  1. 1. Pakati pathu;

    Tiona cikondi—

    Cimene m’dziko mulibe.

    Timaonetsa

    Cikondi coona,

    Sitili mbali ya dziko.

    (MWANA WA KOLASI)

    M’lungu analonjeza.

    Cikondi sicitha.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu—

    Iye ni cikondi.

    Atikonda.

    Cikondi ici—

    Tizionetsana.

    Mu umoyo wathu,

    Tizikondanabe—

    Kwa muyaya.

  2. 2. Nthawi zambili

    Nkhawa na mavuto

    Zingatitsilize mphamvu,

    Kuthandizana

    Kumasangalatsa,

    M’lungu amatitonthoza.

    (MWANA WA KOLASI)

    Cikondi sicisila.

    Cipilila zonse.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu—

    Iye ni cikondi.

    Atikonda.

    Cikondi ici—

    Tizionetsana.

    Mu umoyo wathu,

    Tizikondanabe.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu—

    Iye ni cikondi.

    Atikonda.

    Cikondi ici—

    Tizionetsana.

    Mu umoyo wathu,

    Tizikondanabe—

    Kwa muyaya,

    Kwa muyaya,

    Kwa muyaya.