NYIMBO 17
‘Nifuna’
(Luka 5:13)
-
1. Mwana wa Yehova M’lungu,
Anaonetsa cikondi.
Pobwela padziko Kutithandiza;
Iye anadzipeleka.
Anacilitsa
odwala,
Ogontha na osaona.
Nchito yake anakwanilitsa
Iye anati: ‘Nifuna.’
-
2. Tiyesetse kutengela,
Yesu mu umoyo wathu.
Pophunzitsa anthu, Kudziŵa M’lungu;
Tikhale okoma mtima.
Tithandize anthu onse,
Akasoŵa zilizonse.
Conco amasiye akapempha
Tiyankhe kuti: ‘Nifuna.’
(Onaninso Yoh. 18:37; Aef. 3:19; Afil. 2:7.)