NYIMBO 61
Patsogolo! Inu Mboni Zake
(Luka 16:16)
-
1. Mboni za Yehova n’zolimba mtima
Zimalengeza Ufumu wa Yehova.
Ngakhale Satana ‘zizunze,
Sizileka, zidalila Yehova.
(KOLASI)
Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!
Tumikilani Yehova na cimwemwe!
Uzani onse kuti omvela M’lungu
Adzakhala m’dziko latsopano.
-
2. Atumiki a Yehova Mulungu,
Sacita mantha polalikila anthu.
Samakonda zinthu za m’dziko;
Iwo saiŵala Mulungu wao.
(KOLASI)
Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!
Tumikilani Yehova na cimwemwe!
Uzani onse kuti omvela M’lungu
Adzakhala m’dziko latsopano.
-
3. Anthu amanyoza dzina la M’lungu.
Samalemekeza ucifumu wake.
Tiyeni’se tiwacenjeze;
Tidziŵikitse dzina la Yehova.
(KOLASI)
Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!
Tumikilani Yehova na cimwemwe!
Uzani onse kuti omvela M’lungu
Adzakhala m’dziko latsopano.
(Onaninso Eks. 9:16; Afi. 1:7; 2 Ti. 2:3, 4; Yak. 1:27.)