Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ima, Uone Zinthu Mwatsopano

Ima, Uone Zinthu Mwatsopano

Citani Daunilodi:

  1. 1. Kwada tiotha moto, nyenyezi ziwala,

    Tipumeko lomba ndipo tisimbe pali nkhani zokoma.

    N’kosangalatsa ngako kupatula nthawi

    Yosinkhasinkha za cikondi ca M’lungu—Tidzasangalala!

    (KOLASI)

    Masukako pang’ono, utsitsimukeko.

    Dekhani, penyani kumwamba—

    Kuzodabwitsadi. Tiyambe taima,

    Tione zinthu,

    Mwatsopano.

  2. 2. Pamene mwezi wawala, usiku wakongola.

    Tikusangalala na zabwino zonse Atate watipatsa.

    Poona zinthu mopyola pa mavuto athu,

    Titsimikizatu tidzapililadi. Yehova atikonda.

    (KOLASI)

    Masukako pang’ono, utsitsimukeko.

    Dekhani, penyani kumwamba—

    Kuzodabwitsadi. Tiyambe taima,

    Tione zinthu,

    Mwatsopano.

    Mwatsopano;

    Mwatsopano.

    (KOLASI)

    Masukako pang’ono, utsitsimukeko.

    Dekhani, penyani kumwamba—

    Kuzodabwitsadi. Tiyambe taima,

    Tione zinthu,

    Mwatsopano.

    (KUTSILIZA)

    Tizionenso mwatsopano.

    Tione zinthu.

    Tizionenso mwatsopano.

    Dekha, ona zinthu,

    Mwatsopano.