Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

M’patseni Ulemelelo Yehova

M’patseni Ulemelelo Yehova

(Salimo 96:8)

Citani Daunilodi:

  1. 1. Ndani angakuposeni

    Inu Yehova M’lungu?

    Ningakupatseni ciani

    Pa zonse mumanipatsa?

    Nikayang’ana kumwamba

    Nimasowa conena.

    Munthu ni ndani, Yehova,

    Kuti muzim’ganizila?

    (KOLASI)

    M’lungu wanga, conde mvetselani

    Nyimbo yacitamando.

    M’lungu wanga, citamando conse;

    Ulemelelo wonse

    Zikwele kwa inuyo.

  2. 2. Mawu na zocita zanga

    Zikulemekezeni.

    Nidzathandizanso ena

    Kuti adziwe za inu.

    Kulambila inu M’lungu,

    Ni mwayi wapadela.

    Ndinu pothawila panga

    Tsopano mpaka muyaya.

    (KOLASI)

    M’lungu wanga, conde mvetselani

    Nyimbo yacitamando.

    M’lungu wanga, citamando conse;

    Ulemelelo wonse

    Zikwele kwa inuyo.

  3. 3. Nyanja komanso mapili,

    Dzuwa, mwezi, nyenyezi

    Zimaonetsa ufumu

    Na mphamvu zanu zosatha.

    M’cilengedwe canu conse

    Nimaonanso nzelu.

    Nilekelenji Yehova

    Kukupatsani ulemu?

    (KOLASI)

    M’lungu wanga, conde mvetselani

    Nyimbo yacitamando.

    M’lungu wanga, citamando conse;

    Ulemelelo wonse

    Zikwele kwa inuyo.

(Onaninso Sal. 96:1-10; 148:3, 7.)