Kufuna-funa
Daunilodi
1. Tinayesa kusakila
Tinacipezadi Cuma
Tinali na mafunso pali M’lungu
Koma tinafufuza.
(MWANA WA KOLASI)
Sitinaleke kufuna-funa.
Tinadziŵa kuti tidzapeza co’nadi.
(KOLASI)
Ise tinasakila
mayankho oona
A mafunso tinafunsa.
Kulengedwa kwathu nakufunika
Kwa Ufumu wa M’lungu (Kufuna-funa)
2. Sitinali kudziŵa dzina ya M’lungu
Woona Yehova
Pamene tinaphunzila
Tinasangalaladi
(MWANA WA KOLASI)
Sitinaleke kufunafuna Co’nadi
Caciyambi na tsogolo la anthu.
(KOLASI)
Ise tinasakila
Mayankho oona
A mafunso tinafunsa.
Kulengedwa kwathu nakufunika
Kwa Ufumu wa M’lungu (Kufuna-funa)
(BILIJI)
Timathandiza ena
Kuti acipeze co’nadi tinapeza
Kusakila mayankho oona
timaŵathandizila
Kuti apeze co’nadi
(KOLASI)
Nawo anasakila
mayankho oona
A mafunso anafunsa.
Kulengedwa kwathu, moyo wosatha
Mu ufumu wa M’lungu (Kufuna-funa)