Kungomwetulila
Mawu a Nyimbo:
1. Pofuna kulimbikitsa, tingayese zambili,
Koma kuti amvetsele, kwa iwo n’zovuta.
Tingaonetse cikondi, mu mawu na zocita,
Koma nthawi zina, nikumwetulila.
(KOLASI)
Mwetulila, ungalimbikitse.
Mwetulila, ungathandizile.
Tikapemphela tidzapambana.
Cofunika, nikumwetulila.
2. Zoipa zaculuka, padzikoli lapansi.
Anthu amavutitsidwa, na zocitika m’dziko.
Ise tingaŵathandize mwa kuŵalalikila.
Inde onse tingapeze tiŵalimbikitse.
(KOLASI)
Mwetulila, ungalimbikitse.
Mwetulila, ungathandizile.
Tikapemphela tidzapambana.
Cofunika, nikumwetulila
3. Timamvela cisoni anthu akakana
Kumvetsela uthenga wocokela kwa M’lungu.
Koma ise sitileka kulalika uthenga,
Mwina tikamwetulila, ena angamvele
(KOLASI)
Mwetulila, ungalimbikitse.
Mwetulila, ungathandizile.
Tikapemphela tidzapambana.
Cofunika, nikumwetulila.