Ndise Banja Lanu
Daunilodi:
1. Tafika kumalo ena tacokeladi kutali.
Ulendo wonse tiyamikila madalitso a M’lungu.
Olo nchitoyi siyopepuka, ticitila Yehova.
Cikondi cathu ni cazoona, conco tikunena kuti:
(KOLASI)
Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.
Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.
2. Munali kuyembekeza kuti tipatsane moni
Nyimbo zayamba pa misonkhano m’gwilizano ulimba
Yehova ndiye amapangitsa kuti tigwilizane
Tidzamutamanda mpaka kumalekezelo adziko lonse
(KOLASI)
Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.
Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.
3. Tinawolokanso nyanja kubwela kumalo ano.
Kuti tilalikile kwa anthu ofuna kumvetsela.
Timamasukanso tikaona, cikondi ca abale.
Conco, kulikonse tingayende tikonda abale onse.
(BILIJI)
Tikondwela kupeza banja konse tingayende
Ku Mali, ku Mexico, ku Japan na ku Congo.
(KOLASI)
Ndise anthu a M’lungu, pamodzi ndisedi banja.
Ngakhale muli kutali, dziŵani tikukondani.
Mitundu yonse m’dziko, pamodzi ndisedi banja.
Timaonetsa cikondi, ndisedi banja la Yehova.
India, Colombia na ku Madagascar.
Russia, Tahiti na Malawi,
Azerbaijan, Kazakhstan, na Estonia.
Dziŵani, tikukondani!