Nimayamikila Cilengedwe ca Mulungu
Daunilodi:
1. Maluŵa akumela pa phili
Kucoka kumaphili mphepo ipita
Dzuŵa nayo ikuŵala bwino,
M’makumbi mbalame ziuluka.
(MWANA WA KOLASI)
Niyang’ana zinthu zabwino
Nidzaonetsadi niyamikila.
(KOLASI)
Nimayamikila, cikondi ca M’lungu
Ni cikulu, amanisamala
Ni-kaona zinthu zimene Yehova ’manipatsa
Anapanga Zonse m’cikondi.
Nimayamikila.
Niyamikila.
2. M’mwamba nionamonso mphamvu zake,
Zonse anazipanga nikondwela nazo.
Madzi nawonso yapita bwino m’nyanja
Nyenyezinso ziwala na mwezi.
(MWANA WA KOLASI)
Niyang’ana zinthu zabwino
Nidziŵa zocita, nidzayamikila.
(KOLASI)
Nimayamikila, cikondi ca M’lungu
Ni cikulu, amanisamala.
Ni-kaona zinthu zimene Yehova ’manipatsa
Anapanga zonse m’cikondi
Nimayamikila.
(BILIJI)
Niona nzelu na mphamvu
Na ubwino wa M’lungu
Ni wacikondi, niyamikila
Nimayamikila
(KOLASI)
Nimayamikila, cikondi ca M’lungu
Ni cikulu, amanisamala
Ni-kaona zinthu zimene Yehova ’manipatsa
Anapanga zonse m’cikondi
Nimayamikila.
Nimayamikila.
Tiziyamikila.