Tsiku Iliyonse ili na Nkhawa Zake
Daunilodi:
1. Zonse zidzakhala bwino m’paradaiso,
Nimaikhulupilila lonjezo ya M’lungu
Koma n’covuta kuona madalitso a m’tsogolo
Na cikondi ca Yehova pamene nivutika,
Koma M’lungu alipo.
(KOLASI)
Nimapemphela kwa M’lungu,
Pamene nkhawa zibwela
Nimadalila iye.
Nthawi zonse amayankha
Kupitila mu Baibo
Na mabwenzi abwino.
Tsiku iliyonse i’na nkhawa.
Ine sinidela nkhawa
Za mavuto ya kutsogolo
Ni’na mtendele mu mtima wanga.
2. Mvela mawu anga mnzanga
Dziŵa nikukonda.
Ganizila zabwino osati pamavuto.
Kumbuka, M’lungu wathu atipatsa mwana wake.
Conco, iwe mudalile
Safuna tizivutika
Conco usayope.
(KOLASI)
Pemphela kwa M’lungu
Pamene nkhawa zibwela
Tizidalila iye.
Nthawi zonse amayankha
Kupitila mu Baibo
Na mabwenzi abwino.
Tsiku iliyonse i’na nkhawa
Tisazidela nkhawa
Za mavuto yakutsogolo
Mitima yathu i’na mtendele.
(KOLASI)
Pemphela kwa M’lungu
Pamene nkhawa zibwela
Tizidalila iye.
Nthawi zonse amayankha
Kupitila mu Baibo
Na mabwenzi abwino.
Tsiku iliyonse i’na nkhawa
Tisazidela nkhawa
Za mavuto yakutsogolo
Mitima yathu i’na mtendele
Ti’na mtendele.