Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova Zinatenga Kuti Dzina Lao?

Kodi Mboni za Yehova Zinatenga Kuti Dzina Lao?

Yehova ndi dzina la Mulungu malinga n’zimene Baibulo limanena. (Ekisodo 6:3; Salimo 83:18) Mboni ndi munthu amene amalengeza kapena kukamba za nkhani inayake imene amakhulupilila kuti ndi ya zoona.

Conco, timachedwa Mboni za Yehova cifukwa cakuti ndife Akristu amene timalengeza coonadi ponena za Yehova, Mlengi wa zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Timacitila umboni kwa anthu mwa zocita zathu ndiponso mwa kuwaphunzitsa zimene timaphunzila m’Baibulo.—Yesaya 43:10-12; 1 Petulo 2:12