Kodi a Mboni za Yehova Ali na Baibo Yawo-yawo?
A Mboni za Yehova akhala akuseŵenzetsa ma Baibo azimasulilo zosiyana-siyana pophunzila Baibo. Ngakhale n’telo, timakonda kuseŵenzetsa kwambili Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zimene linamasulidwa. Timaikonda cifukwa imachula dzina lenileni la Mulungu, ndipo ni lolondola, komanso ni losavuta kumva.
Kuchula dzina lenileni la Mulungu. Ena omasulila Baibo amalephela kuthokoza Mwini Wake weniweni. Mwacitsanzo m’Baibo ina anandandalikamo maina oposa 70 a anthu amene anathandizila poimasulila. Ngakhale n’conco, m’Baibo imeneyi anacotselatu dzina la Mwini Wake weniweni, Yehova Mulungu.
Mosiyana na zimenezi, Baibulo la Dziko Latsopano linabwezeletsa dzina la Mulungu m’malo ofika masauzande mmene linali kupezeka m’mipukutu yoyambilila yamakedzana. Ndipo amene anamasulila Baibo imeneyi maina awo sanalembedwemo pena paliponse.
Kulondola kwake. Si ma Baibo onse amene anamasulila Mawu a Mulungu molondola kwenikweni. Mwacitsanzo, Baibo ina pa Mateyu 7:13 imakamba kuti: “Loŵani pa cipata copapatiza, cifukwa cipata ca ku helo n’cacikulu ndipo msewu wopita kumeneko ni wosavuta kuyendamo.” Komabe mu mpukutu woyambilila munali liwu lakuti “ciwonongeko,” osati “helo.” Mwina omasulila anaikapo liwu lakuti helo pokhulupilila kuti anthu ocita zoipa amakazunzidwa kwamuyaya m’moto wa helo. Koma Baibo siiphunzitsa zimenezo. Ndiye cifukwa cake mu Baibulo la Dziko Latsopano vesili analimasulila molondola kuti: “Lowani pacipata copapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuciwonongeko.”
Ni yosavuta kumva: Baibo yomasulidwa bwino siiyenela kukhala yolondola cabe ayi, iyenelanso kukhala yosavuta kuiŵelenga ndiponso yosavuta kumva. Ganizilani citsanzo ici. Pa Aroma 12:11, mtumwi Paulo anaseŵenzetsa liwu lotanthauza “mzimu kuŵila”. Popeza mawu amenewa ni ovuta kumva mu Chichewa camakono, Baibulo la Dziko Latsopano linamasulila vesiyi m’njila yosavuta kumva. Imakamba za Akhristu kuti “yakani ndi mzimu.”
Kuwonjezela pa kuchula dzina lenileni la Mulungu, kulondola kwake, komanso kumveka mosavuta, palinso cinthu cina capadela na Baibulo la Dziko Latsopano: Limagaŵidwa kwa anthu kwaulele. Mwa ici, anthu mamiliyoni amatha kuŵelenga Baibo m’cinenelo cawo—ngakhale aja amene sakanakwanitsa kugula Baibo yawo-yawo.