Kodi a Mboni za Yehova Amatsatila Mfundo Ziti pa Nkhani Yokhala na Cibwenzi?
A mboni za Yehova amakhulupilila kuti malamulo na mfundo za m’Baibo zimatithandiza kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu komanso zotipindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Sikuti tinacita kudzipangila malamulo na mfundo zimenezi. Komabe, timazitsatila. Tiyeni tione malamulo ndiponso mfundo zina za m’Baibo pankhani ya cibwenzi. a
Cikwati ni mgwilizano wa moyo wonse. (Mateyu 19:6) Popeza kuti a Mboni za Yehova amaona kuti kukhala pa cibwenzi ni sitepu yoloŵela m’banja, iwo satenga mopepuka nkhani yokhala pa cibwenzi.
Anthu amene ayenela kukhala pa cibwenzi ni okhawo amene anafika pa msinkhu wotha kukhala pa banja. Iwo ayenela kukhala amene ‘anapitilila pacimake pa unyamata,’ kapena amene anapitilila pa msinkhu umene cilako-lako ca kugonana cimakhala camphamvu.—1 Akorinto 7:36.
Amene ayenela kukhala pa cibwenzi ni aja amene sali pa banja. Mulungu saona kuti anthu ena amene anathetsa mabanja awo kukhoti angakhale omasuka kukwatila kapena kukwatiwanso. Zili conco cifukwa cakuti iye amaona kuti banja lingathe kokha ngati wina wacita cigololo.—Mateyu 19:9.
Mkhristu amene afuna kukwatila ayenela kusankha munthu amene ni wokhulupilila mnzake. (1 Akorinto 7:39) A Mboni za Yehova amaona kuti lamuloli silikamba za kusankha munthu amene amalemekeza cabe zimene timakhulupilila, koma limakamba za kusankha munthu amene amakhulupilila zinthu zofanana na zathu na kuzitsatila ndiponso Mboni yobatizika. (2 Akorinto 6:14) Kuyambila kale, Mulungu amalimbikitsa olambila ake kukwatila anthu acikhululupililo cofanana na cawo cabe. (Genesis 24:3; Malaki 2:11) Masiku ano, ofufuza apeza kuti lamulo limeneli ni lothandizanso. b
Ana afunika kumvela makolo awo. (Miyambo 1:8; Akolose 3:20) Kwa ana amene akali pa nyumba pa makolo awo, kumvela lamuloli kumaphatikizapo kumvela zimene makolo asankha pankhani yokhala na cibwenzi. Izi zingaphatikizepo zaka zimene mwanayo angayambe cibwenzi ndiponso zinthu zimene sayenela kucita akakhala pa cibwenzico.
Mogwilizana na malangizo a m’Malemba, wa Mboni aliyense amasankha yekha pa nkhani ya kukhala pa cibwenzi ndiponso munthu amene angakhale naye pa cibwenzico. Izi zikugwilizana na mfundo yakuti: “Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.” (Agalatiya 6:5) Komabe, a Mboni ambili amene akufuna kukhala pa cibwenzi, amafunsila nzelu kwa a Mboni acikulile amene amawafunila zabwino.—Miyambo 1:5.
Zinthu zambili zimene anthu amakonda kucita akakhala pa cibwenzi ni macimo akulu-akulu. Mwacitsanzo, Baibo imatilangiza kuti tifunika kupewa khalidwe laciwelewele. Izi ziphatikizapo kugonana komanso kucita makhalidwe ena onyansa pakati pa anthu osakwatilana, monga kuseŵeletsa malisece a munthu wina, kapena kugonana m’kamwa kapena kumatako. (1 Akorinto 6:9-11) Zingaphatikizeponso kucita zinthu zina zoutsa cilako-lako ca kugonana ngakhale kuti safika pogonana. Kucita zinthu “zodetsa” zimenezi sikukondweletsa Mulungu. (Agalatiya 5:19-21) Cinanso, Baibo imaletsa kukambilana “nkhani zotukwana” zokhudza kugonana.—Akolose 3:8.
Mtima, kapena kuti umunthu wathu wamkati, ni wonyenga. (Yeremiya 17:9) Ungasonkhezele munthu kucita zinthu zimene adziŵa kuti n’zoipa. Conco, kuti anthu amene ali pa cibwenzi asasoceletsedwe na mitima yawo, afunika kupewa kukhala kumalo kwa okha-okha kumene kulibe anthu ena amene akuwaona. Iwo angasankhe kuti nthawi zonse azikhala pa gulu kapena limodzi ndi munthu wina oŵapelekeza. (Miyambo 28:26) Akhristu amene sali pa banja amazindikila kuti si bwino kungoyamba cibwenzi pa intaneti na munthu amene samudziŵa kweni-kweni.—Salimo 26:4.
a Anthu a zikhalidwe zina amakhala pa cibwenzi asanakwatilane. Koma a zikhalidwe zina sacita zimenezo. Baibo sikamba kuti anthu afunika kukhala pa cibwenzi kuti akwatilane.
b Mwacitsanzo, nkhani ina m’magazini yochedwa Marriage & Family Review inati: “Anthu ena anapanga kafuku-fuku maulendo atatu ndipo anapeza kuti anthu ambili amene akhala pa banja nthawi yaitali (zaka 25 mpaka 50 kapena zoposa) ni amene ali m’cipembedzo cimodzi ndipo amakhulupilila zofanana.”—voliyumu 38, magazini yoyamba, peji 88 (2005).