Kodi Mboni za Yehova ndi Akristu?
Inde. Ndife Akristu pa zifukwa zotsatilazi:
Timatsatila kwambili zimene Yesu Kristu anaphunzitsa ndiponso makhalidwe ake.—1 Petulo 2:21.
Timakhulupilila kuti Yesu ndiye njila yotitsogolela ku cipulumutso, ndipo “
palibe dzina lina pansi pa thambo, limene lapelekedwa kwa anthu, limene tiyenela kupulumutsidwa nalo.
”—Machitidwe 4:12.Anthu akabatizika m’dzina la Yesu, m’pamene amakhala Mboni za Yehova.—Mateyu 28:18, 19.
Timapemphela kwa Mulungu kupitila m’dzina la Yesu.
Timakhulupilila kuti Yesu ndiye Mutu, kapena kuti munthu amene wapatsidwa udindo, pa munthu wina aliyense.—1 Akorinto 11:3.
Komabe, timasiyana kwambili ndi zipembedzo zina zimene zimati n’zacikristu. Mwacitsanzo, timakhulupilila zimene Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, osati kuti ali mbali ya Utatu. (Maliko 12:29) Sitikhulupilila kuti moyo sumafa, ndiponso kuti pali umboni wa m’Malemba wakuti Mulungu amazunza anthu ku helo. Sitikhulupililanso kuti atsogoleli a mipingo ayenela kukhala ndi maina audindo amene amawacititsa kukhala apamwamba kuposa ena.—Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4; Mateyu 23:8-10.