Kodi Phunzilo la Baibulo N’ciani?
A Mboni za Yehova amacita maphunzilo a Baibulo ndi anthu, ndipo pa maphunzilo amenewa amayankha mafunso osiyanasiyana monga awa:
Kodi Mulungu Ndani?
Kodi Mulungu Amasamala za Inu?
Ndingacite Ciani Kuti Cikwati Canga Ciziyenda Bwino?
Ndingacite Ciani Kuti Ndizisangalala Paumoyo?
Pansi apa pali mayankho a mafunso amene anthu amafunsa kaŵilikaŵili ponena za phunzilo la Baibulo.
Kodi phunzilo la Baibulo limacitika bwanji? Timasankha mitu yosiyanasiyana, monga mutu wakuti “Mulungu” kapena “cikwati,” ndiyeno timakambitsilana malemba osiyanasiyana a m’Baibulo ogwilizana ndi mutu umenewo. Timayelekezela mavesiwo kuti tidziŵe zimene Baibulo lonse limanena pa nkhaniyo, ndipo mwanjila imeneyi, timalola kuti Baibulo lizizitanthauzila lokha.
Kuti tiphunzile Baibulo mosavuta, timagwilitsa nchito buku lakuti Zimene Baibo Iimaphunzitsa M’ceni-ceni? Buku limeneli limafotokoza momveka bwino zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana, monga zokhudza Mulungu, Yesu ndi tsogolo lathu.
Kodi ndiyenela kulipila ndalama zingati kuti ndiziphunzila Baibulo? Phunziloli ndi laulele, ndipo mabuku amene timagwilitsila nchito pophunzila alibe mtengo.
Phunzilo la Baibulo limatenga nthawi yaitali motani ulendo uliwonse? Anthu ambili amasankha kuti tizicita nao phunzilo la Baibulo pafupifupi kwa ola limodzi mlungu uliwonse. Komabe, kutalika kwa nthawi ya phunziloli kumakhala kosiyana malinga ndi mmene zinthu zilili kwa inu. Ife timavomela kusintha kuti tigwilizane ndi zimene inu mufuna.
Cimacitika n’ciani munthu akapempha kuti tiziphunzila naye Baibulo? Mukapempha phunzilo la Baibulo, munthu wa Mboni za Yehova adzabwela kuti aonane nanu pa nthawi ndi malo amene inu mungakonde. Kwa nthawi yocepa, iye adzakuonetsani mmene timacitila phunzilo. Kenako, mungapitilize kuphunzila ngati mungakonde.
Ngati ndavomela kuti ndiziphunzila Baibulo, kodi ndiyenela kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova? Ai. Ife timakondwela kuphunzitsa anthu Baibulo, koma sitimawakakamiza kuloŵa cipembedzo cathu. M’malo mwake, timawafotokozela mwaulemu zimene Baibulo limakamba, ndipo timazindikila kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene afuna kuti azikhulupilila.—1 Petulo 3:15.