Kukaona Malo pa Beteli
Tikuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi, amene timayacha kuti Beteli. Maofesi ena a nthambi ali na ma miziyamu yakuti munthu akhoza kudzionela yekha zinthu popanda wina kumutsogolela.
Kuyambilanso Kukayendela Maofesi a Nthambi: Pa June 1, 2023, m'maiko ambili tinayambilanso kulola anthu kukayendela maofesi athu a nthambi. Kuti mumve zambili, funsilani ku ofesi ya nthambi imene mufuna kukayendela. Koma conde, osapitako ngati munapezeka na COVID-19, ngati muli na cimfine, kapena ngati caposacedwa munakhalako pafupi na munthu wodwala COVID-19.
Ghana
Nungua Police Checkpoint
Hse. No. J 348/4
Tema Beach Road
Nungua
ACCRA
GHANA
+233 30-701-0110
+233 30-2712-456
+233 30-2712-457
+233 30-2712-458
Kuona Malo
Pa Mande mpaka pa Cisanu
8:00hrs mpaka 11:00hrs ndi 13:00hrs mpaka 16:00hrs.
Nthawi yoona malo: Ola limodzi
Zimene Timacita
Timamasulila mabuku ofotokoza Baibulo m’Citwi, Ciewe, Ciga, Cidangime, Cinzema, Cifrafra, ndi Cidagaare. Ndipo timapanga ma CD a zofalitsa ndi mavidiyo m’Citwi, Ciewe, ndi m’Ciga. Timamanga Nyumba za Ufumu 60 caka ciliconse pa avaleji ndipo timatumiza mabuku olemela matani mahandiledi ambili m’dzikoli.